Mungasunthe Mapiri!
MAY 29, 1953, inasimbidwa kukhala nthaŵi yoyamba pamene munthu anaima pamwamba pa nsonga ya phiri lalitali koposa m’dziko lapansi—Phiri la Everset mamita 8,848 pamwamba pa malekezero a nyanja. Ndi chichirikizo cha oposa anthu 450, Edmund Hillary wa ku New Zealand ndi Tenzing Norgay, m’Nepalese Sherpa, mwachipambano anagonjetsa zowopsya za kuterera kwa madzi owundana, chifunga chopatsa khungu, ndi kusoweka kwa mpweya wopuma kuti afike pamwamba pa chonulirapo chawo cha utali wa mamailo asanu ndi theka.
Kufika pamwamba pa mapiri atali ndithudi chiri chokwaniritsa chapadera. Komabe sichingafanane ndi chimene Yesu analongosola kwa ophunzira ake: “Ndikuwuzani inu motsimikizirika, ngati chikhulupiriro chanu chinali ngati mbewu ya mpiru munganene kwa phiri iri, ‘Choka apa pita uko’, ndipo lidzasuntha; palibe chimene chidzakhala chosatheka kwa inu.” Tangolingalirani, osati kukwera koma kusuntha phiri!—Mateyu 17:20; The JerusalemBible.
Nchiyani chomwe chinasonkhezera Yesu kunena chimenechi kwa ophunzira ake? Iwo anali atangolephera kuchiritsa mnyamata wogwidwa ndi chiwanda. Yesu anagogomezera chifukwa chimene iwo analepherera: Iwo anafunikira chikhulupiriro chowonjezereka. (Mateyu 17:14-20) Iye anayerekeza chikhulupiriro ku mbewu ya mpiru, chinachake chimene iwo anali ozoloŵerana nacho bwino. Ngakhale kuti iri pakati pa “zazing’ono koposa,” mbewu ya mpiru pambuyo pa miyezi yoŵerengeka ya kukula ingakhale chomera chonga mtengo. (Mateyu 13:31, 32) Chotero, Yesu anali kugogomezera kuthekera kokulira kumene chikhulupiriro chochepera chingakhale nacho pamene chakulitsidwa ndi kuleledwa moyenerera—chomwe chiwoneka chosatheka chingakhale chotheka.
Koma pambuyo pa kukulitsa chikhulupiriro choterocho, ndi mtundu wotani wa mapiri umene ophunzira a Yesu akakhoza kusuntha? Mongadi mmene phiri lenileni lingakhalire lotsekereza, zokhumudwitsa zonga phiri zingatsekereze kupita kwathu patsogolo mu utumiki wa Yehova. Nchiyani chimene “mapiri” amenewo angakhale ndipo ndimotani mmene “tingasunthire” iwo?
Mtumwi Paulo ali chitsanzo cha Mkristu yemwe anayang’anizana ndi zokhumudwitsa zambiri. Pa 2 Akorinto 6:4-10 ndi 2 Akorinto 11:23-28, mungaŵerenge za kukumanizana kwake ndi kusala kudya, kumenyedwa, kuikidwa m’ndende, kuswekedwera chombo, ndi unyinji wa matsoka ena. M’kuwonjezera ku zinthu izi, panalinso “munga m’thupi” wophiphiritsira umenewo, mwinamwake vuto lina ndi kuwona kwake. (2 Akorinto 12:7; Machitidwe 14:15) Kodi chinali chothekera motani kwa iye kulaka zotsekereza zonga mapiri zoterozo ndipo mwachipambano kukwaniritsa chifuniro cha Mulungu kaamba ka iye? “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo,” analemba tero Paulo. Uku nkunena “kuti ukulu woposa mphamvu ukhale wa Mulungu wosachokera kwa ife.” (Afilipi 4:13; 2 Akorinto 4:7) Chotero, Paulo anali ndi chikhulupiriro chotheratu mu kuthekera kwa Yehova kwa kumulimbikitsa iye mu nthaŵi yovuta kwambiri. Iye anali ndi chikhulupiriro.
Kusuntha Mapiri Lerolino
Kodi chiri chikhumbo chanu kuwonjezera utumiki wanu kwa Yehova? Mofanana ndi mazana a zikwi omwe agwirizana ndi mathayo omakulakula a olalikira a nthaŵi zonse (apainiya), nanunso mungakumve kufulumira kwa nthaŵi ndipo mosamalitsa mungakhale mukulingalira za kufutukula utumiki wanu. Ngakhale kuli tero, kodi chokhumudwitsa chowoneka kukhala chosalakika monga phiri lalikulu chiri kutsogolo kwanu? Ngati ndi tero, kodi inu mungasunthe mapiri? Zikwi zachita chimenecho m’zoyesayesa zawo za kuwonjezera utumiki wawo kwa Yehova. Pano pali kokha zochepera za zokumana nazo zawo.
Mlongo wachichepere wina yemwe anayenera kumaliza maphunziro kuchokera ku sukulu yake mopambana onse m’kalasi yake anakhumba kuchita upainiya, koma kusoweka kwa ntchito kunali phiri lake. Iye akulongosola kuti:
“Kulingalira kwanga koipa kwenikweni kwa kuika zikaikiro ponena za kuchita kwanga upainiya kunakhala chokhumudwitsa kwa ine choti ndichilake. Popeza ndinali wodera nkhaŵa ndi kupeza ntchito ndisanayambe kuchita upainiya, sindinali kuika chikhulupiriro changa chotheratu ndi chidaliro mwa Yehova ndi kuthekera kwake kwa kupereka kaamba ka awo amene amaika kulambira iye choyamba. Ndinapitiriza kulingalira, ‘Choyamba ndipeze ntchito, kenaka ndidzaika chifunsiro changa cha upainiya.’ Sindinali kuchita upainiya; ndinalidi kutaya nthaŵi ya mtengo wapatali. Ngakhale kuli tero, mmodzi wa akulu a mu mpingo analoza ku icho kuti ku utali umene ndidzadikirira kuyamba kuchita upainiya, ukakhala ubwino umene ntchito za nthaŵi zonse zikawoneka, popeza ndinalibe china chirichonse chondiletsa ine kulandira izo.”
Nchiyani chimene iye anachita? “Ndinapemphera kwa Yehova mowona mtima kaamba ka mzimu wake woyera kulangiza ndi kutsogoza machitidwe anga ndi kulingalira.” Pambuyo pa kumaliza maphunziro mlongo ameneyu anachita upainiya wothandizira, ndipo kenaka analowa mu utumiki wa upainiya wokhazikika. Mwamsanga pambuyo pake, anapeza ntchito yoyenera ya kuthupi yomwe inalola ndandanda yake ya upainiya.
Mkulu wina, amene mkazi wake anali mu utumiki wa upainiya ndi amene anali ndi ana aŵiri ofunika kuwalera, anadzimva kuti anayenera kuchita zambiri koposa kokha kuchirikiza banja lake mwa za ndalama. Kwa openyerera ena, mikhalidwe yomuletsa iye kuchita utumiki wa upainiya inawoneka kukhala yosalakika, ndipo komabe iye anakhumba kufutukula utumiki wake. Nchiyani chomwe chinafunikira kusintha?
“Ndikulingalira kuti chokhumudwitsa chachikulu koposa chomwe ndinafunikira kuchilaka ndithudi chinali inemwini,” iye akutero. “Utumiki wa m’munda unali chinachake chimene nthaŵi zonse ndinasangalala nacho, ndipo kulankhula ndi awo a mu utumiki wa nthaŵi zonse ndi kuwona madalitso awo, ndinapeza mzimu wabwino umene iwo anasonyeza kukhala woyambukira. Ndikadziwona inemwini mu utumiki wa nthaŵi zonse tsiku lina. Vuto la kulingalira kwanga linali lakuti kuchita upainiya kunakhala chinachake chimene ndinali kokha kulingalira ponena za icho. Koma ndinali ndisanadzipatse inemwini deti pa limene ndikakonda kukhala ndi chonulirapocho chitazindikiridwa.”
Pambuyo pa kulingalira kwa pemphero, mbale ameneyu anayamba kugwirira ntchito kulinga ku chonulirapo chake cha utumiki wa nthaŵi zonse. Iye anafikira woyang’anira wake pa ntchito, kulongosola zolinga zake, ndi kufunsa kuloledwa kugwira ntchito maora ocheperapo mlungu uliwonse. Malinga ndi kukhudzidwa kwa lamulo la kampaniyo, mtundu wa ndandanda imene iye anafuna unali wosalingalirika.
Iye akupitiriza kuti: “Woyang’anira wanga pa ntchito anatha kukambitsiranako mwa kunena kuti mwachidziŵikire sindikalandira ndandanda yomwe ndinali kufunsira. Ndinali wotsimikizira kuti ngati chosankhacho chinali kudalira kotheratu kwa iye, yankholo likakhala ayi. Ndipo chotero chivomerezocho chikabwera kokha mwa njira ya kuchirikiza kwa Yehova. Mlungu umodzi ndi theka pambuyo pake, chivomerezo cha ndandanda yanga yatsopano chinabwera kuchokera ku bungwe lopanga malamulo. Pambuyo pa kuyamikira woyang’anira wanga wa ntchito, ndinapita ku galimoto yanga, kuyendetsa kudutsa nyumba zingapo, kuima kumbali kwa msewu, ndi kulongosola chithokozo changa ndi chiyamikiro kwa Yehova. Inde, chonulirapo changa cha utumiki wa nthaŵi zonse chikakhala chenicheni.”
Ndimotani mmene mlongo wokwatiwa “anasunthira” phiri lake? Iye akulongosola kuti: “Ndiri ndi ana anayi ndi mwamuna wosakhuluprira. Pamene ndinayamba kulingalira za kuchita upainiya, ndinali ndi zokhumudwitsa zochulukirapo. Kwa chinthu chimodzi, mwamuna wanga anali wosalembedwa ntchito kwa kanthaŵi, popeza kuti ntchito yake inali ya pa nyengo, ndipo ndiali kugwira ntchito kwa kanthaŵi kuthandidza ndi zolipirira. Chotero ndinanena kwa inemwini kuti ngakhale ngati ndinali ndi chikhumbocho, sindikanatha kuchita upainiya chifukwa cha mikhalidwe yanga. Ngakhale kuli tero, pano ndi pamene ndinayenera kuwongolera kulingalira kwanga. Ndinazindikira kuti ngati ndikanapitiriza kulingalira kuti sindikanatero, sindikaika kuyesayesa kulikonse kwa kuyesera kuchita tero. Funso lotsatira lofunika kwambiri lomwe ndinafunikira kuyankha linali, Ndi kuti kumene ndikapeza mphamvu ya kuchita upainiya? Ndinapeza yankho pa Afilipi 4:13. Sindinapemphere kokha kwa Yehova ponena za nkhaniyo koma ndinayamba kudalira mowonjezerekawonjereka pa iye. Ndinatenganso masitepi ogwira ntchito kulinga ku kufikira chonulirapo changa cha kukonza ndandanda yabwino ndi kulembetsa monga mpainiya wothandizira. Pamene nthaŵi inapita, Yehova anapitiriza kutsegula njira kaamba ka ine kulowa utumiki wa upainiya. Mwamuna wanga anali wokhoza kubwerera ku ntchito, ndipo ndinakhoza kuchepetsa ntchito yanga ya pa kanthaŵi ku tsiku limodzi pa mlungu. Pasanapite nthaŵi yaitali pambuyo pa ichi, ndinakhala mpainiya wokhazikika.”
M’kuwonjezerapo, mwaŵi wa kupezeka pa sukulu ya Utumiki wa Upainiya unatseguka kwa iye, yomwe inatsimikizira kukhala thandizo lokulira mu utumiki wake. “Ndikungofuna kuwuza aliyense yemwe akulingalira ponena za kuchita upainiya kupemphera kwa Yehova ndi kuika icho m’manja mwake,” iye akutero. “Ndipo pangani kuyesayesa, ndipo iye adzakudalitsani inu chifukwa cha kuyesera.”—Salmo 37:5.
Kodi zokumana nazo zimenezi sizikuthandizani inu kuwona mmene chikhulupiriro pamene chichitidwa chingathandizire Mkristu kulaka zokhumudwitsa zonga mapiri? Chotero, ngati chiri chikhumbo chanu cha kuchita upainiya, santhulani mikhalidwe yanu. Lankhulani kwa ena omwe akuchita upainiya, ndipo phunzirani kuchokera ku zokumana nazo zawo. Tengani masitepi okhoza kugwira ntchito kulinga ku kufikira chonulirapo chanu. Ndipo pamwamba pa zonse, pempherani kwa Yehova ponena za chikhumbo chanu; kenaka dalirani pa iye kudalitsa zoyesayesa zanu. Inde, nanunso mungasunthe mapiri!