Ripoti la Olengeza Ufumu
Anapeza Chifukwa Chosinthira
KODI apandu kapena ngakhale atsogoleri a kagulu angasinthe mkhalidwe wawo? Kodi nchiyani chikawathandiza kutero? Kusintha kokulira m’mkhalidwe nkothekera monga momwe zikuwonedwera m’chochitika cha Saulo wa ku Tariso, amene anasintha kuchokera ku kuzunza Akristu nakhala Mkristu iyemwini. Pambuyo pake anadziŵika monga mtumwi Paulo. (Agalatiya 1:13, 14; 1 Timoteo 1:13) Kusintha kokulira kofananako kukusimbidwa kuchokera ku Kenya.
◻ Mnyamata wina anali chiŵalo chagulu la achifwamba m’gawo la ku Nairobi ndipo anatumizidwa kumadzulo kwa Kenya kukafufuza njira zothekera za kuba m’banki kumeneko. Iye anakakhala m’nyumba ina ndi mwamuna wachikulire ndipo anapeza mulu wa magazine akale a Galamukani! m’nyumba yakeyo. Mnyamatayo anatengeka mtima kambiri ndi kuŵerenga magazine amenewo kotero kuti anaiŵala kotheratu za makonzedwe ake a kukaba m’banki. Pamene anaŵerenga onsewo, anapempha owonjezereka, ndipo mwamuna wachikulireyo anamuuza kuti amodzi akafika pambuyo pa milungu iŵiri iriyonse mwa mtokoma. Kuyambira pamenepo kunka mtsogolo mnyamatayo anakokosa womcherezayo kupita ku positi ofesi tsiku lirilonse kukawona magazine owonjezereka. Pakali pano, iye anapanga chosankha cha kusiya njira zake zoipa, kutsatira zimene anaphunzira m’magazinewo, ndi kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye anafikira pa kuyamba kuwuza anansi ake kuti anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Pambuyo pake, mpainiya wapadera anagwirira ntchito m’gawolo ndipo anadabwa kupeza mnyamatayo akudzinenera kukhala Mboni. Phunziro la Baibulo linayambidwa ndi iye, napeza uchikulire wauzimu, ndipo lerolino ndimpainiya wokhazikika. Chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chinampatsa chifukwa chabwino chosinthira mkhalidwe wake.
◻ Mwamuna winanso mu Argentina anapeza chifukwa chosinthira njira yake yamoyo wachiwawa. Kwa zaka 20, iye anazunza moipitsitsa mkazi wake, yemwe anali Mboni. Chinanenedwa kuti iye anafikira pa kukumba dzenje m’bwalo lake naika mtanda pamwamba pake, ndi cholinga cha kupha munthu yemwe anali kuba nkhuku zake ndi kumufotsera pamenepo. Chifukwa cha mkhalidwe wambanda wa mwamunayo, anansi onse anampeŵa iye.
Woyang’anira wadera anafika panyumba yake. Adakali pamenepo, mtumiki waderayo anafunsira phunziro Labaibulo ndi mwamunayo ndipo anadabwitsidwa pamene mwamuyo anati akakhala wokondwera kuphunzira Baibulo. Mbaleyo anaphunzira broshuwa ya Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! ndi iye. Mwamunayo anapita patsogolo m’chidziŵitso cha Baibulo ndi kumvetsetsa kwauzimu. Iye tsopano amapezekapo pa misonkhano yonse. Amakonda kwambiri misonkhano ndi kuyanjana ndi abale nafika pa kunena kuti, “Kuno ndi kumene ndifuna kumakhala.”
Kusintha mwa mwamuna ameneyu kunali kwakukulu kotero kuti anansi anafunsa mkazi wake ponena za sing’anga yemwe anali kumuchiritsa iye. Pamene mkaziyo analongosola kuti kusinthako kunachitika chifukwa cha kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, mnansi wina anakondweretsedwa kwambiri kotero kuti anapempha Baibulo. Mnansi wina analembetsa magazine athu.
Chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chinapatsa amuna amenewa chifukwa chosinthira njira yawo ya moyo. Icho chingathandize aliyense wokhumba kukhala ndi moyo watanthauzo lokulira tsopano ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko latsopano lolonjezedwa ndi Mulungu.—Yohane 17:3.