Moyo Wapambuyo pa Imfa—Mafunso Osayankhidwa
“ATAFA munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?” (Yobu 14:14) M’zitaganya zonse kwazaka mazana ambiri, anthu akhala akusinkhasinkha pa funso limeneli lofunsidwa ndi kholo Yobu zaka mazana ambiri zapitazo, ndipo pakhala mayankho ambiri olingaliridwa.
Agiriki akale ananena kuti miyoyo ya anthu akufa inapitirizabe kukhala ndi moyo. Iyi inawolotsedwa mtsinje wa Styx kupita kumalo aakulu akunsi kwanthaka otchedwa dziko lakunsi. Kumeneko oweruza anaweruzira miyoyo imeneyo kaya kuchizunzo m’ndende yokhala ndi malinga atali kapena kumtendere m’malo aparadaiso. Anthu ena akale analingalira kuti miyoyo inasanduka kukhala nyenyezi kapena nthanda. Komabe ena anakhulupirira kuti miyoyo inali zounikira ndipo inkakokeredwa kumwezi; mwezi uliwonse pamene mwezi unali wathunthu, inasamutsidwira ku dzuŵa.
Lerolino, nthathi zonena za moyo wapambuyo pa imfa zikuwonjezerekabe. Ahindu ndi Abuddha amakhulupirira kubadwiranso m’thupi lina. Asilamu amaphunzitsa kuti moyo umapulumuka pa imfa ya thupi ndipo pa chiweruzo chotsirizira udzapita kaya kuparadaiso kapena kuhelo. Apurotestante ambiri amaphunzitsidwa kuti miyoyo imapitirizabe kukhalapo pambuyo pa imfa kukasangalala ndi mtendere wakumwamba kapena chizunzo m’moto wa helo. Chikatolika chimawonjezera Limbo ndi purigatoriyo kuchithunzi chimenechi.
M’maiko ena, zikhulupiriro zonena za yolingaliridwa kukhala miyoyo ya akufa ziri nsanganizo yamphamvu ya mwambo wamalowo ndi Chikristu m’dzina lokha. Mwachitsanzo, uli mwambo wa Akatolika ndi Apurotestante Kumadzulo kwa Afirika kuphimba akalirole pamene wina wamwalira kotero kuti palibe amene angayang’ane ndikuwona mzimu wa munthu wakufayo. Masiku makumi anayi pambuyo pa imfa ya wokondedwa, banja ndi mabwenzi adzachita madyerero kusangalalira kukwera kwa moyowo kumwamba. Pambuyo pake, kaŵirikaŵiri pa Krisimasi kapena pa Tsiku la Chaka Chatsopano, achibale amakacheza kumanda ndikuthira moŵa pa lithindapo. Iwo amalankhula kwa wakufayo, akumapempha madalitso ndi kusimba nkhani zapabanja.
Mwachiwonekere, pali kuvomerezana kochepa pakati pa zipembedzo zadziko ponena za chimene kwenikweni chimachitika pambuyo pa imfa. Komabe, pafupifupi onse amavomerezana pamfundo imodzi yaikulu: kusakhoza kufa kwa moyo wamunthu. Ziphunzitso zochuluka zonena za moyo wapambuyo pa imfa zangokhala kusiyanasiyana kwa mutu waukulu umenewu.
Ngakhale kuli choncho, pamakhala mafunso oŵerengeka obukapo: Kodi kwenikweni lingaliro lakuti moyo suumafa limachokera kuti? Kodi limaphunzitsidwa m’Malemba? Ngati ndichoncho, kodi nchifukwa ninji ngakhale zipembedzo zosakhala Zachikristu zimaliphunzitsa? Awa ndimafunso osayenera kunyalanyazidwa. Mosasamala kanthu za chikhulupiriro chanu chachipembedzo, imfa ndiyo chenicheni choyenera kuyang’anizana nacho. Motero nkhanizi zimakuphatikizani mwachindunji. Chotero tikukupemphani kupenda nkhanizi ndi maganizo opanda tsankhu.