Kusanthula Mbali za Ngale ya Mtengo Wake ya Mulungu—Baibulo!
MU 1867 mlimi wa ku South Africa wotchedwa Schalk van Niekerk ankapenyerera ana akuseŵera ndi miyala. Mwala wina woŵala kwenikweni ndi wokongola unamchititsa chidwi. “Mungautenge, ngati mwaukonda,” amayi ŵa anawo anatero. Komabe, van Niekerk anatumiza mwalawo kwa akatswiri a miyala ya mtengo wapatali kuti ukasanthulidwe. Anawo sanadziŵe kuti anali kuseŵera ndi diamond yaikulu yogulidwa ndi ndalama zokwanira £500!
Kodi nkotheka kuti nanunso muli ndi chinthu cha mtengo wake popanda kuchizindikira? Mwachitsanzo, ambiri ali ndi Baibulo, popeza kuti ndilo logulidwa koposa yanthaŵi zonse, lopezeka lathunthu kapena mbali yake m’zinenero zoposa 1,900. Komabe, anthu ambiri sanaliŵerenge Baibulo ndipo nchifukwa chake amadziŵa zochepera ponena za zamkati mwake.
Baibulo limanena kuti “adaliuzira Mulungu” ndipo chotero ndilo Mawu a Mulungu. (2 Timoteo 3:16; yerekezerani ndi 1 Atesalonika 2:13.) Ndilo chuma cha anthu chamtengo wapatali koposa. Kupyolera mwa ilo, timaphunzira mmene tingapezere moyo wabwino koposa tsopano ndipo, chofunika koposa, mmene tingapezere moyo wosatha! (Yohane 17:3, 17) Kodi china chirichonse chingakhale chamtengo wapatali kuposa zimenezo?
Komabe, kuti munthu amvetsetse ngale imeneyi ndi mbali zake zonse, afunikira kukhala wozoloŵerana nalo. Poyamba, ichi chingawonekere kukhala chovutirapo. Ndiiko komwe, Baibulo ndiunyinji wa mabuku 66 osiyanasiyana. Kodi nchiyani chimene mabuku amenewo ali nacho? Kodi pali chifukwa chirichonse cha dongosolo m’limene iwo amawonekera? Ngati nditero, kodi ndimotani mmene munthu angapezere mawu apadera m’Baibulo?
Kukhala wozoloŵerana ndi Baibulo kuli chitokoso. Koma mofanana ndi mwala wamtengo wake weniweni, Baibulo liri logwirizana ndi ladongosolo. Tingawone zimenezo ngati tilingalira mwachidule zamkati mwake.
Malemba Achihebri—Osonya kwa Kristu
Mwachisawawa Baibulo nlogaŵidwa kupanga “Chipangano Chakale” ndi “Chipangano Chatsopano.” Komabe, aŵa ndi maina olakwika, opereka lingaliro lakuti “Chipangano Chakale” nchachikale ndipo nchosafunika kwenikweni. Dzina loyenerera kaamba ka chigawo chimenecho cha Malemba ndilo Malemba Achihebri, popeza kuti chigawo chimenechi poyamba chinalembedwa kwakukulukulu m’chinenero cha Chihebri. “Chipangano Chatsopano” chinalembedwa m’Chigiriki m’zaka za zana loyamba C.E.; chotero, icho moyenerera chimatchedwa Malemba Achikristu Achigiriki.
Bukhu loyamba la Baibulo, Genesis, limayamba kufotokoza zaka zamakedzana kalelo pamene Mulungu alenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo pambuyo pake ayamba kukonzekeretsa dziko lapansi kuti likhalidwe ndi anthu. Okwatirana aŵiri oyambirira aumunthu alengedwa angwiro; komabe, iwo asankha njira ya uchimo, yokhala ndi zotulukapo zatsoka kwa ana awo. Chikhalirechobe, monga ngale yowonedwa m’kuunika kwachizimezime, Baibulo limapereka chiyembekezo chonyezimira kwa anthu ochimwa: “mbewu” imene pomalizira pake idzathetsa ziyambukiro za uchimo ndi imfa. (Genesis 3:15) Kodi Mbewu imeneyi idzakhala yani? Genesis ayamba kudziŵikitsa mzera wa Mbewu yomadzayo, kulunjikitsa chidwi pa miyoyo ya ena a makolo okhulupirika a Mbewu imeneyo, monga ngati Abrahamu, Isake, ndi Yakobo.
Ndiyeno Eksodo amafotokoza kubadwa kwa Mose. M’mbali zambiri, moyo wa Mose umachitira chithunzi uja wa Mbewu yomadzayo. Pambuyo pa miliri khumi, Israyeli ayamba ulendo waukulu wotchedwa Eksodo kutuluka m’Igupto ndipo akhazikitsidwa monga mtundu wosankhika wa Mulungu pa Phiri la Sinai. Levitiko, monga momwe dzinalo likusonyezera, amakhazikitsa malamulo a Mulungu kaamba ka unsembe Wachilevi m’Israyeli. Numeri akusimba zochitika pamene Aisrayeli anaŵerengedwa ndi zochitika mkati mwa ulendo wa Israyeli m’chipululu. Ndipo tsopano, wokonzekera kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Israyeli alandira machenjezo omalizira a Mose. Uwu ndiwo mutu wankhani wa Deuteronomo. Akusonya kwa Mbewu yomadzayo, Mose alimbikitsa mtunduwo kumvetsera kwa ‘mneneri amene Mulungu adzautsa.’—Deuteronomo 18:15.
Mabuku ambiri yakale atsatira. Aŵa m’mbali yokulira ali m’dongosolo lotsatizana bwino. Yoswa amafotokoza kugonjetsedwa ndi kugaŵidwa kwa Dziko Lolonjezedwa. Oweruza akusimba zochitika zosangalatsa za zaka zotsatirapo pamene Israyeli alamulidwa ndi mzera wa oweruza. Rute akusimba za mkazi wowopa Mulungu, yemwe akhala ndi moyo mkati mwa nyengo ya Oweruza ndi yemwe akhala ndi mwaŵi wokhala kholo lachikazi la Yesu Kristu.
Komabe, nyengo yakulamulira kwa oweruza ifika kumapeto. Samueli Woyamba akusimba za ulamuliro watsoka wa mfumu yoyamba ya Israyeli, Sauli, monga kwawonedwera ndi mneneri Samueli. Samueli Wachiŵiri akufotokoza kulamulira kwachipambano kwa Davide, woloŵa m’malo wa Sauli. Ndiyeno Mafumu Woyamba ndi Wachiŵiri akutitenga kuchokera ku kulamulira kwaulemerero kwa Solomo mpaka kutengeredwa ku Babulo muukapolo kochititsa chisoni kwa mtundu wa Aisrayeli mu 607 B.C.E. Mbiri Yoyamba ndi Yachiŵiri ibwerezanso mbiriyi monga yawonedwera kuyambira pachimake cha kubwerera kwa mtunduwo kuchoka muukapolo. Pomalizira pake, Ezara, Nehemiya, ndi Estere akufotokoza mmene Aisrayeli abwezeretsedwera ku dziko lawo ndi mbiri yawo yotsatirapo.
Mabuku andakatulo akutsatira, okhala ndi ndakatulo zabwino koposa zimene zalembedwa. Yobu apereka chithunzithunzi chochititsa chidwi cha umphumphu pansi pa kuvutika ndi mphotho yake. Bukhu la Masalmo liri ndi nyimbo za chitamando kwa Yehova ndi mapemphero kaamba ka chifundo ndi chithandizo. Zimenezi zatonthoza atumiki a Mulungu osaŵerengeka. Kuwonjezerapo, Masalmo ali ndi maulosi ochuluka omwe amatiunikira mowonjezereka ponena za Mesiya wakudzayo. Miyambo ndi Mlaliki amavumbula mbali za nzeru yaumulungu kupyolera m’miyambi yachidule yomvekera bwino, pamene kuli kwakuti Nyimbo ya Solomo ndindakatulo yachikondi yoposa yokhala ndi tanthauzo lalikulu laulosi.
Mabuku 17 otsatira—kuchokera Yesaya mpaka Malaki—kwakukulukulu ngaulosi. Onse, kusiyapo Maliro, ali ndi maina a wolemba. Ambiri a maulosi ameneŵa akhala ndi kukwaniritsidwa kwawo kodabwitsa. Iwo amasonyanso ku zochitika zomalizira m’tsiku lathu ndi mtsogolo.
Chotero Malemba Achihebri amasonyeza kusiyanasiyana kodabwitsa kwa mtundu ndi kalembedwe. Komabe, onse ali ndi mutu wankhani umodzi. Maulosi awo, mizera ya makolo, ndi zochitika zosangalatsa zimanyezimira ndi nzeru yeniyeni ndi tanthauzo laulosi.
Malemba Achikristu Achigiriki—Mbewu Iwonekera
Zaka zikwi zinayi zapita kuyambira pamene munthu anachimwa. Mwadzidzidzi, padziko lapansi pawonekera Mbewuyo yoyembekezeredwa kwanthaŵi yaitali, Mesiyayo, Yesu! Malemba Achikristu Achigiriki ali ncholembedwa cha munthu wofunikayu m’mbiri ya anthu m’mabuku anayi osiyana koma ochirikizana, otchedwa Mauthenga Abwino. Iwo ndi Mateyu, Marko, Luka, ndi Yohane.
Nzamtengo wapatali chotani nanga zolembedwa zinayi zimenezi za Uthenga Wabwino kwa Akristu! Zimasimba zozizwitsa zochititsa nthumanzi za Yesu, mafanizo ake atanthauzo, Ulaliki wake wa pa Phiri, chitsanzo chake cha kudzichepetsa, chifundo chake ndi kumvera kotheratu kwa Atate wake, chikondi chake kaamba ka “nkhosa,” ndipo pomalizira pake imfa yake yansembe ndi kuukitsidwa kwaulemerero. Phunziro la Mauthenga Abwino limakulitsa mwa ife chikondi chakuya kaamba ka Mwana wa Mulungu. Koposa zonse, timayandikira pafupi ndi uyo amene anatuma Kristu—Yehova Mulungu. Zolembedwa zimenezi nzoyenera kuŵerengedwa mobwerezabwereza.
Machitidwe a Atumwi amayambira pamene Mauthenga Abwino amathera. Amasimba zaka zoyambirira za mpingo Wachikristu kuchokera masiku a Pentekoste mpaka kuikidwa m’ndende kwa Paulo ku Roma mu 61 C.E. M’bukhu limeneli, timaŵerenga za Stefano, Mkristu wophedwera chikhulupiriro woyambirira, kutembenuzidwa kwa Saulo, yemwe pambuyo pake akhala mtumwi Paulo, kulandiridwa kwa Akunja otembenuzidwa, ndi maulendo aulaliki osangalatsa a Paulo. Zolembedwa zimenezi ponse paŵiri nzosangalatsa ndi zokulitsa chikhulupiriro.
Tsopano otsatira ndimakalata makumi aŵiri mphambu imodzi. Oyambirira 14, olembedwa ndi Paulo, ngotchedwa ndi maina a Akristu kapena mipingo yowalandira; otsalawo atchedwa ndi maina a owalemba—Yakobo, Petro, Yohane, ndi Yuda. Ha, ndimachenjezo ochuluka chotani nanga ndi chilimbikitso zimene makalataŵa ali nazo! Iwo amamveketsa bwino chiphunzitso ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi. Amathandiza Akristu kukhala olekana ndi malo oipa mmene iwo ayenera kukhalamo. Iwo amagogomezera kufunika kwa kukulitsa chikondi chaubale ndi mikhalidwe ina yaumulungu. Iwo amakhazikitsa chitsanzo kaamba ka kulinganiza koyenera kwa mpingo, pansi pa chitsogozo cha amuna achikulire mwauzimu.
Monga momwe Malemba Achihebri amathera ndi ulosi, momwemonso amatero Malemba Achigiriki. Chibvumbulutso, cholembedwa ndi mtumwi Yohane pafupifupi 96 C.E., chimasonkhanitsa pamodzi maulosi onse ndi mutu wankhani waukulu wa Baibulo—kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova kupyolera mu Ufumu wake Waumesiya. Mpambo wa masomphenya usonyeza mwazithunzithunzi kuwonongedwa kwa magulu achipembedzo, ankhondo, ndi andale zadziko a dongosolo loipa la Satana. Izi ziloŵedwa mmalo ndi mzinda wokhala likulu la boma la Kristu, limene lipereka chisamaliro kulamulira zochitika za dziko lapansi. Pansi pa kulamulira kwa Ufumu umenewu, Mulungu akulonjeza ‘kupukuta misozi . . . ndipo sipadzakhalanso imfa.’—Chibvumbulutso 21:4.
Pamenepo, kodi pali kukaikira kulikonse kuti Baibulo liri ngale yosalakwa, yosonyeza kuunika kwaumulungu? Ngati simunaliŵerenge lonse, bwanji osayamba kutero tsopano? Mudzakopedwa ndi kugwirizana kwake, kuunikiridwa ndi kuŵala kwake, kukhudzidwa ndi kukongola kwake, ndi kusangalatsidwa ndi uthenga wake. Ilo liridi ‘chininkho . . . changwiro . . . chotsika kwa Atate wa mauniko.’—Yakobo 1:17.
[Tchati pamasamba 28, 29]
NDANDANDA YA MABUKU A BAIBULO
Yosonyeza wolemba, malo kumene linalembedwera, nthaŵi yomaliza kulemba, ndi nthaŵi yokutidwa ndi zochitika za m’bukhulo.
Maina a olemba mabuku ena ndi malo kumene analembedwera ngosatsimikizirika. Madeti ambiri ngoyerekezera, chizindikiro cha a. chimatanthauza “pambuyo pa,” b. chimatanthauza “isanakhale,” ndi c. chimatanthauza “pafupifupi.”
Mabuku a Malemba Achihebri (B.C.E.)
Bukhu Wo(O)lemba Malo Olembera Kulemba Nthaŵi
Kunamalizidwa Yokutidwa
Genesis Mose Chipululu 1513 “Pachiyambi”
mpaka 1657
Eksodo Mose Chipululu 1512 1657-1512
Levitiko Mose Chipululu 1512 Mwezi 1 (1512)
Numeri Mose Chipululu/
Zigwa za
Moabu 1473 1512-1473
Deuteronomo Mose Zigwa za
Moabu 1473 Miyezi 2 (1473)
Yoswa Yoswa Kanani c. 1450 1473-c. 1450
Oweruza Samueli Israyeli c. 1100 c. 1450-c. 1120
Rute Samueli Israyeli c. 1090 Zaka 11 za kulamuulira kwa
oweruza
1 Samueli Samueli;
Gadi; Natani Israyeli c. 1078 c. 1180-1078
2 Samueli Gadi; Natani Israyeli c. 1040 1077-c. 1040
1 Mafumu Yeremiya Yerusalemu/
Yuda 580 c. 1040-911
2 Mafumu Yeremiya Yerusalemu/
Igupto 580 c. 920-580
2 Mbiri Ezara Yerusalemu (?) c. 460 1037-537
Ezara Ezara Yerusalemu c. 460 537-c. 467
Nehemiya Nehemiya Yerusalemu a. 443 456-a. 443
Estere Moredekai Susani, Elamu c. 475 493-c. 475
Yobu Mose Chipululu c. 1473 Zoposa zaka 140
pakati pa 1657
ndi 1473
Masalmo Davide ndi ena c. 460
Miyambo Solomo;
Aguri;
Lemueli Yerusalemu c. 717
Mlaliki Solomo Yerusalemu b. 1000
Nyimbo ya
Solomo Solomo Yerusalemu c. 1020
Yesaya Yesaya Yerusalemu a. 732 c. 778-a. 732
Yeremiya Yeremiya Yuda/Igupto 580 647-580
Maliro Yeremiya Pafupi ndi
Yerusalemu 607
Ezekieli Ezekieli Babulo c. 591 613-c. 591
Danieli Danieli Babulo c. 536 618-c. 536
Hoseya Hoseya Samariya
(Dera) a. 745 b. 804-a. 745
Yoweli Yoweli Yuda c. 820 (?)
Amosi Amosi Yuda c. 804
Obadiya Obadiya c. 607
Yona Yona c. 844
Mika Mika Yuda b. 717 c. 777-717
Nahumu Nahumu Yuda b. 632
Habakuku Habakuku Yuda c. 628 (?)
Zefaniya Zefaniya Yuda b. 648
Hagai Hagai Yerusalemu 520 Masiku 112 (520)
Zekariya Zekariya Yerusalemu 518 520-518
Malaki Malaki Yerusalemu a. 443
Mabuku a Malemba Achikristu Achigiriki (C.E.)
Bukhu Wo(O)lemba Malo Olembera Kulemba Nthaŵi
Kunamalizidwa Yokutidwa
Mateyu Mateyu Palestina c. 41 2 B.C.E.–
33 C.E.
Marko Marko Roma c. 60-65 29-33 C.E.
Luka Luka Kaisareya c. 56-58 3 B.C.E.–
33 C.E.
Yohane Mtumwi Efeso, kapena
Yohane chapafupi c. 98 Pambuyo pa
mawu oyambirira,
29-33 C.E.
Machitidwe Luka Roma c. 61 33-c.
61 C.E.
Aroma Paulo Korinto c. 56
1 Akorinto Paulo Efeso c. 55
2 Akorinto Paulo Makedoniya c. 55
Agalatiya Paulo Korinto
kapena
Antiokeya
wa ku Suriya c. 50-52
Aefeso Paulo Roma c. 60-61
Afilipi Paulo Roma c. 60-61
Akolose Paulo Roma c. 60-61
1 Atesalonika Paulo Korinto c. 50
2 Atesalonika Paulo Korinto c. 51
1 Timoteo Paulo Makedoniya c. 61-64
2 Timoteo Paulo Roma c. 65
Tito Paulo Makedoniya (?) c. 61-64
Filemoni Paulo Roma c. 60-61
Ahebri Paulo Roma c. 61
Yakobo Yakobo
(mbale
wa Yesu) Yerusalemu b. 62
1 Petro Petro Babulo c. 62-64
2 Petro Petro Babulo (?) c. 64
1 Yohane Mtumwi
Yohane Efeso, ka.
chapafupi c. 98
2 Yohane Mtumwi
Yohane Efeso, ka.
chapafupi c. 98
3 Yohane Mtumwi
Yohane Efeso, ka.
chapafupi c. 98
Yuda Yuda
(mbale
wa Yesu) Palestina (?) c. 65
Chibvumbulutso Mtumwi
Yohane Patmo c. 96