Chifukwa Chake Amagwiritsira Ntchito Zotsala za Akufa Polambira
NAPLES, Italiya. Tayerekezerani kuti muli kumeneko m’zaka zoyambirira za zana la 18 m’Nyengo Yathu ino. M’nyumba yolambirira kumeneko, George Berkeley, wanthanthi wa ku Ireland akuimirira patsogolo pa chotsala cha wakufa chotchuka chachipembedzo. Iye akuyang’ana mokaikira umene umawoneka kukhala mwazi womasungunuka wa “San Gennaro,” Januarius, “woyera mtima” Wachikatolika.
Naples wasintha pang’ono m’chochitika chimenechi. Mwachitsanzo, mosasamala kanthu za mphepo yoipa panthaŵi ina m’zaka zaposachedwapa, tchalitchicho chinadzazanso ndi anthu, ndipo chowoneka kukhala chozizwitsa chinachitika. Chotsala cha wakufacho ndi ligubo lotsogozedwa ndi kadinala yemwe ndi bishopu wamkulu zinalandiridwa ndi kuwomba manja kwachisangalalo. Inde, iyi inali imodzi ya nthaŵi zambiri zimene mwazi wa “San Gennaro” unawonekera kukhala ukusungunuka. Zozizwitsa zoloŵetsamo chotsala cha wakufa chachipembedzo chimenechi zasimbidwa kukhala zikuchitika chiyambire m’zaka za zana la 14.
Malinga ndi mwambo Wachikatolika, chotsala cha wakufa (m’Chingelezi lotembenuzidwa kuchokera ku liwu Lachilatini lakuti relinquere, lotanthauza “kusiya kumbuyo”) ndicho chinthu chosiidwa ndi munthu wolingaliridwa kukhala woyera mtima. Monga momwe Dizionario Ecclesiastico imanenera, zotsala za akufa ndizo “m’lingaliro lenileni la liwulo, thupi kapena mbali ya thupi ndi phulusa la Woyera Mtima, m’lingaliro lachisawawa ndichinthu chimene chinakhudza thupi la woyera mtimayo ndipo motero chiri choyenera kupembedzedwa.”
Kuvomereza kwa Apapa
Mwinamwake, ambiri amalemekeza zotsala za akufa zachipembedzo chifukwa cha zowonekera kukhala zozizwitsa zogwirizana nazo. Mwachiwonekere kuvomereza kwa apapa ndiko chinthu china chimene chimakupangitsa kukhala kotchuka.
Apapa osachepera pa anayi m’zaka 70 zapitazo aika chisamaliro chadera pa zotsala za akufa. Chofalitsidwa Chachikatolika chimavumbula kuti mofanana ndi amene iye anamloŵa m’malo, Pius XI, Papa Pius XII “anasunga zotsala za woyera mtima wa ku Lisieux.” Paul VI “anasunga chala cha mtumwi [Tomase] pa desiki m’chipinda chake chophunzirira,” ndipo John Paul II “akusunga, m’chipinda chake, zidutswa za . . . zotsala za wakufa” za “Woyera Mtima Benedict” ndi “Woyera Mtima Andrew.”—30 giorni, March 1990, tsamba 50.
Polingalira za kuvomereza kwa apapa koteroko, nkosadabwitsa kuti anthu ofuna kumapembedza zotsala za akufa mwamtseri ndi poyera akuwonjezereka. Koma kodi kupembedza zotsala za akufa zachipembedzo kumamkondweretsa Mulungu?
[Chithunzi patsamba 3]
Mosungiramo zotsala za akufa zachipembedzo
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy of The British Museum