Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Popeza kuti Akristu samabetchera ndalama, kodi iwo angalandire matikiti amwaŵi kapena kutengamo mbali m’machitachita amwaŵi mwa amene angapate mphoto?
Limeneli ndifunso lomwe labuka mobwerezabwereza, chotero linayankhidwa kale m’zofalitsa zathu. M’zinenero zina, tinapanga maindex a mabuku athu, monga ngati Watch Tower Publications Index 1930-1985 (ndi ina yofanana nayo ya zaka za 1986-1990). Ngati Mkristu ali ndi maindex amenewo m’chinenero chake, iwowo angagwiritsiridwe ntchito kupeza msanga mayankho okhutiritsa.
Tidzagwiritsira ntchito funso limene lafunsidwa pamwambapa monga chitsanzo. Poyang’ana mu Index ya 1930-1985 pansi pa mutu wakuti “Questions From Readers” (Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga), munthu amapeza mutu waung’ono wakuti “‘drawings,’ may Christian accept ticket for?” (‘machitachita amwaŵi,’ kodi Mkristu angalandire tikiti yake?) Woŵerengayo akuuzidwa kuyang’ana chigawo cha “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu The Watchtower ya February 15, 1973, tsamba 127.a Mboni zambiri zili ndi voliyumu (kapena kope limodzilimodzi) ya The Watchtower ya 1973, kapena ingapezeke m’laibulale ya Nyumba Zaufumu zambiri.
Nkhani yosindikizidwa mu 1973 inasonyeza kuti Akristu moyenerera amapeŵa kubetchera kulikonse kapena machitachita amwaŵi ophatikizapo kugula matikiti amwaŵi (monga ngati matikiti a raffle) kapena kubetchera ndalama kuti apeze mwaŵi wakupata mphotho. Kunena mwachidule, timapeŵa kutchova juga, kumene kumasonyezadi umbombo.—1 Akorinto 5:11; 6:10; Aefeso 4:19; 5:3, 5.
Sitolo kapena bizinesi ingagwiritsire ntchito machitachita amwaŵi monga njira yosatsira malonda. Zokha zimene munthu ayenera kuchita ndizo kulembetsa dzina kapena kutumiza fomu kapena tikiti, popanda kugula kanthu kalikonse. Machitachita amwaŵiwo angokhala mbali ya njira yosatsira malonda; amalinganizidwa kukhala njira yopanda tsankho yodziŵira amene adzalandira mphotho. Akristu ena angalingalire kuti akhoza kulandira mphotho ya m’machitachita amwaŵi amene samaphatikizapo kubetchera, monga momwe angalandirire zinthu zaulere kapena mphatso zina zimene bizinesi kapena sitolo ingagwiritsire ntchito m’programu yake yakusatsa malonda.
Komabe, Akristu ena angakane chinthu chilichonse cha mtundu umenewu, posafuna kukhumudwitsa kapena kusokoneza ena ndiponso pofuna kupeŵeratu chisonkhezero chilichonse cha kudalira wotchedwa kuti Mulungu Wamwaŵi. Monga momwe lemba la Yesaya 65:11 limasonyezera, atumiki a Mulungu samadzigwirizanitsa ndi “mulungu wamwaŵi” kapena “mulungu wa Choikidwiratu.” (NW) Iwo sangakonde kulengezedwa kumene kumayembekezeredwa kwa opambanawo. Awo amene amalingalira mwanjirayi sayenera konse kusuliza Mkristu kapena Akristu amene chikumbumtima chawo chimawalola kutengamo mbali m’machitachita amwaŵi oterowo.—Yerekezerani ndi Aroma 14:1-4.
[Mawu a M’munsi]
a Nkhani yofananayo yaikidwa pansi pa mitu yakuti “Advertising” (Kusatsa Malonda), “Business” (Bizinesi) ndi “Gambling” (Kutchova Juga), chotero kusinthasintha kwa Index kumathandiza munthu kupeza chidziŵitsocho.