Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 7/1 tsamba 25-27
  • Mawu a Mulungu Amachita “Zozizwitsa”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mawu a Mulungu Amachita “Zozizwitsa”
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kufunafuna Kwanga Anthu a Mulungu
  • Kulalikira m’Tauni Yakwathu
  • “Zozizwitsa” Zochitidwa ndi Mawu a Mulungu
  • Kuyandikira kwa Mulungu Kunandithandiza Kulaka
    Galamukani!—1993
  • Yehova Wandipatsa Nyonga
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • ‘Ndidzadumpha Ngati Nswala’
    Galamukani!—2006
  • Ndakhala Wokhulupirika kwa Mulungu kwa Zaka Zoposa 70
    Galamukani!—2009
Nsanja ya Olonda—1996
w96 7/1 tsamba 25-27

Mawu a Mulungu Amachita “Zozizwitsa”

YOSIMBIDWA NDI THÉRÈSE HÉON

Tsiku lina mu 1965, ndinaloŵa m’malo ena a malonda ndi kusonyeza makope a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa eni malondawo. Pamene ndinali kubwerera, ndinamva kuphulika. Chipolopolo chinaomba pansi pafupi ndi mapazi anga. “Ndimo mochitira ndi Mboni za Yehova,” mmodzi wa amalondawo anatonza motero.

CHOCHITIKA chimenecho chinandiwopsa​—koma osati kwakuti nkuleka utumiki wanthaŵi yonse. Choonadi cha Baibulo chimene ndinali nditaphunzira chinali chamtengo wapatali kwambiri kwakuti sindingalole chilichonse kundisiyitsa utumiki wanga. Tandilolani ndifotokoze chifukwa chimene ndikunenera choncho.

Nditabadwa mu July 1918, makolo anga anakakhala ku Cap-de-la-Madeleine, mudzi waung’ono ku Quebec, Canada, wodziŵika monga Malo a Zozizwitsa. Alendo ambiri ankabwera kuno kudzalambira fano la Namwali Mariya. Ngakhale kuti zozizwitsazo zochitidwa ndi Mariya sizingatsimikiziridwe, Mawu a Mulungu achita zozizwitsa zenizeni m’moyo wa anthu ambiri pamene mudziwo wakula kukhala tauni ya anthu oposa 30,000.

Pamene ndinali ndi zaka pafupifupi 20, atate wanga anaona chikondwerero changa pankhani zachipembedzo ndipo anandipatsa Baibulo. Pamene ndinayamba kuliŵerenga, ndinadabwa kwambiri kuphunzira kuchokera pa Eksodo chaputala 20 kuti kulambira mafano kumatsutsidwa kwambiri. Nthaŵi yomweyo ndinataya chidaliro pa ziphunzitso za Tchalitchi cha Katolika ndipo ndinaleka kupita ku Misa. Sindinafune kulambira mafano. Ndikukumbukirabe Atate akunena kuti, “Thérèse, kodi supita kutchalitchi?” “Ayi,” ndinayankha motero, “Ndikuŵerenga Baibulo.”

Kuŵerenga Baibulo kunapitirizabe kukhala mbali ya moyo wanga ngakhale pamene ndinakwatiwa mu September wa 1938. Popeza mwamuna wanga, Rosaire, kaŵirikaŵiri ankagwira ntchito usiku, ndinapanga chizoloŵezi cha kuŵerenga Baibulo pamene anali kuntchito. Posapita nthaŵi ndinadziŵa kuti Mulungu ayenera kukhala ali ndi anthu, ndipo ndinayamba kuwafunafuna.

Kufunafuna Kwanga Anthu a Mulungu

Chifukwa cha zimene ndinali nditaphunzira kutchalitchi, pamene ndinali wamng’ono, ndinkachita mantha kupita kukagona kuwopa kuti ndingadzukire ku helo. Kuti ndithetse mantha oterowo, ndinali kudziuza kuti Mulungu wachikondi sangalole chinthu chankhanza chotero kuchitika. Mwachidaliro, ndinapitirizabe kuŵerenga Baibulo, kufunafuna choonadi. Ndinali ngati mdindo wa ku Aitiopiya amene ankaŵerenga koma osamvetsetsa.​—Machitidwe 8:26-39.

Cha mu 1957, mlongo wanga André ndi mkazi wake, amene ankakhala m’nyumba yapansi pa nyumba yathu, anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ndinauza mlamu wanga kuti azindichenjeza mwa kugogoda padenga pamene Mboni zibwera kudzalalikira panyumbayo. Chotero ndinkadziŵa kuti sindiyenera kutsegula chitseko. Tsiku lina anaiŵala kundichenjeza.

Tsikulo ndinatsegula chitseko ndipo ndinaonana ndi Kay Munday, mpainiya, monga momwe atumiki anthaŵi yonse a Mboni za Yehova amatchedwera. Analankhula nane ponena za dzina la Mulungu, akumafotokoza kuti Mulungu ali ndi dzina laumwini, Yehova. Atapita, ndinafufuza m’Baibulo langa kuti nditsimikizire kuti zimene ananena zinali kuchirikizidwadi ndi mawu a m’Baibulo. Kufufuza kwanga kunandisangalatsa kwambiri.​—Eksodo 6:3, Douay Version, mawu a mtsinde; Mateyu 6:9, 10; Yohane 17:6.

Pamene Kay anabweranso, tinakambitsirana za chiphunzitso cha Katolika cha Utatu, chimene chimati Mulungu ndi anthu atatu mwa Mulungu mmodzi. Pambuyo pake ndinasanthula Baibulo langa mosamala kuti ndidzikhutiritse kuti silimaphunzitsa Utatu. (Machitidwe 17:11) Phunziro langa linanditsimikizira kuti Yesu si wamkulu monga Mulungu. Iye analengedwa. Anali ndi chiyambi, pamene kuli kwakuti Yehova alibe. (Salmo 90:1, 2; Yohane 14:28; Akolose 1:15-17; Chivumbulutso 3:14) Nditakhutiritsidwa ndi zimene ndinali kuphunzira, ndinali wofunitsitsa kupitiriza makambitsirano a Baibulo.

Tsiku lina mu 1958, pamene kunali chimphepo chachipale chofeŵa cha mu November, Kay anandiitanira kumsonkhano wadera umene unaliko madzulo amenewo m’holo ya lendi. Ndinalandira chiitanocho ndipo ndinasangalala ndi programuyo. Pambuyo pake, pokambitsirana ndi Mboni imene inadza kwa ine, ndinafunsa kuti, “Kodi Mkristu woona ayenera kulalikira kunyumba ndi nyumba?”

“Inde,” anatero, “uthenga wabwino uyenera kulengezedwa, ndipo Baibulo limanena kuti kufikira anthu panyumba zawo kuli njira yofunika kwambiri ya kulalikira.”​—Machitidwe 20:20.

Mmene ndinasangalalira nanga ndi yankho lake! Zinanditsimikiziritsa kuti ndapeza anthu a Mulungu. Akananena kuti, “Ayi, sikofunika,” ndikanakayikira zakuti ndapeza choonadi, popeza ndinadziŵa zimene Baibulo limanena ponena za kulalikira kunyumba ndi nyumba. Kuchokera panthaŵi imeneyo, ndinapita patsogolo mwauzimu mwamsanga.

Pambuyo pa msonkhano wadera umenewo, ndinayamba kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova imene inkachitidwira m’tauni yapafupi ya Trois-Rivières. Kay ndi mnzake, Florence Bowman, ndiwo okha anali Mboni zimene zinali kukhala ku Cap-de-la-Madeleine panthaŵiyo. Tsiku lina ndinanena kuti, “Maŵa ndidzapita nanu kukalalikira.” Iwo anasangalala kuti ndinawaperekeza.

Kulalikira m’Tauni Yakwathu

Ndinkaganiza kuti aliyense adzalandira uthenga wa Baibulo, koma mwamsanga ndinazindikira kuti si mmene zinthu zinalili. Pamene Kay ndi Florence anatumizidwa kwina, ndinali ndekha m’tauniyo amene ndinali kulalikira choonadi cha Baibulo kunyumba ndi nyumba. Mopanda mantha, ndinapitirizabe kulalikira ndili ndekha kwa pafupifupi zaka ziŵiri mpaka ubatizo wanga pa June 8, 1963. Tsiku lomwelo ndinalembetsa utumiki umene panthaŵiyo unkatchedwa kuti upainiya wapatchuthi.

Ndinapitirizabe monga mpainiya wapatchuthi kwa chaka chimodzi. Ndiyeno, Delvina Saint-Laurent analonjeza kuti ngati ndidzakhala mpainiya wokhazikika iye adzayamba kumabwera ku Cap-de-la-Madeleine ndi kugwira nane ntchito kamodzi pamlungu. Chotero ndinadzaza fomu yanga yaupainiya. Komabe, mwachisoni, kutatsala milungu iŵiri yokha kuti ndiyambe utumiki wanthaŵi yonse, Delvina anamwalira. Kodi ndikanachitanji? Chabwino, ndinali nditadzaza kale fomu ndipo sindinafune kuibweza. Chotero mu October 1964, ndinayamba ntchito yanga ya muutumiki wanthaŵi yonse. Kwa zaka zotsatirapo zinayi, ndinkayenda ndekha kunyumba ndi nyumba.

Kaŵirikaŵiri Akatolika odzipereka a ku Cap-de-la-Madeleine anali aukali. Ena anaitana apolisi pofuna kundiletsa kulalikira. Tsiku lina, monga momwe ndinatchulira poyamba, wamalonda wina anayesa kundiwopseza mwa kuwombera ku mapazi anga. Eya, zimenezi zinachititsa zolankhulalankhula zambiri m’tauni. Wailesi yakanema yakumaloko inatcha zimenezo kukhala mkupiti wolimbana ndi Mboni za Yehova. Chochitika chonsecho chinachititsa ulaliki wabwino. Komabe, zaka khumi pambuyo pake, wachibale wa wamalonda amene anali atawombera kwa ine anakhala Mboni.

“Zozizwitsa” Zochitidwa ndi Mawu a Mulungu

Kwa zaka zonsezi, ndaona chopinga cha kutsutsa choonadi cha Baibulo chili kutha pang’onopang’ono ku Cap-de-la-Madeleine. Cha ku ma 1968, Mboni zina zinasamukira kuno, ndipo anthu a kuno anayamba kulandira choonadi cha Baibulo. Kwenikweni, podzafika kuchiyambi cha m’ma 1970, panali chiwonjezeko chachikulu cha ophunzira Baibulo. Zinadzafika penapake pamene ndinayenera kupempha Mboni zina kuti zizichititsa maphunziro a Baibulo angapo amene ndinali kuchititsa kuti ndipitirizebe kukhala ndi phande muutumiki wa kunyumba ndi nyumba.

Tsiku lina mtsikana wina analandira buku lothandizira kuphunzira Baibulo la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Mnzake panthaŵiyo anali mwamuna wina wotchedwa André, mpandu wooneka mwanyankhalala amene anagwirizana nafe m’makambitsiranowo. Kukambitsirana ndi André kunadzutsa chikondwerero chake, ndipo phunziro la Baibulo linayambidwa. Mwamsanga pambuyo pake anayamba kulankhula ndi mabwenzi ake ponena za zimene ankaphunzira.

Panthaŵi ina, ndinali kuphunzira Baibulo ndi apandu anayi, mmodzi wa iwo amene sankalankhulalankhula koma ankamvetsera kwambiri. Dzina lake anali Pierre. Tsiku lina cha ku ma 2 koloko mmaŵa, ineyo ndi mwamuna wanga tinamva kugogoda pachitseko. Taganizirani chochitikachi: Apandu anayi anali ataima pamenepo ndi mafunso kwa ine. Mwamwaŵi, Rosaire sanadandaule konse za kuchezeredwa kotero kwamwadzidzidzi.

Poyamba amuna anayiwo ankabwera kumisonkhano. Komabe, André ndi Pierre ndiwo okha amene analimbikira. Anagwirizanitsa moyo wawo ndi miyezo ya Mulungu ndipo anabatizidwa. Kwa zaka zoposa 20 tsopano, amuna onse aŵiriwo atumikira Yehova mokhulupirika. Pamene anayamba kuphunzira, ankadziŵika bwino chifukwa cha zochita zawo zaupandu ndipo apolisi ankawalonda. Nthaŵi zina apolisi ankabwera kudzawafunafuna pambuyo pa limodzi la maphunziro athu a Baibulo kapena mkati mwa msonkhano wa mpingo. Ndili wachimwemwe kuti ndinalalikira “anthu a mitundu yonse,” ndipo ndinadzionera ndekha mmene Mawu a Mulungu amachititsira kusintha kumene kumaonekadi kukhala kozizwitsa.​—1 Timoteo 2:4, NW.

Sindikanakhulupirira pamene ndinayamba utumiki wanga ndikanauzidwa kuti mu Cap-de-la-Madeleine mudzakhala Nyumba ya Ufumu ndi kuti idzadzazidwa ndi anthu a Yehova. Chondikondweretsa nchakuti mpingo umodzi waung’onowo m’tauni yapafupi ya Trois-Rivières wakula kukhala mipingo yomapita patsogolo isanu ndi umodzi imene imakumana m’Nyumba za Ufumu zitatu, kuphatikizapo imene ili ku Cap-de-la-Madeleine.

Ndakhala ndi chimwemwe cha kuthandiza pafupifupi anthu 30 kufika pa kudzipatulira ndi ubatizo. Tsopano, pamsinkhu wazaka 78, ndinganenedi kuti ndili wokondwa kuti ndinapatulira moyo wanga kwa Yehova. Komabe, ndiyenera kuvomereza kuti ndakhala ndi nthaŵi zina za kumva kukhala wolefulidwa. Kuti ndilimbane ndi nthaŵi zimenezi mwachipambano, nthaŵi zonse ndimatsegula Baibulo langa ndi kuŵerenga ndime zina zimene zimanditsitsimutsa kwambiri. Sindingalole tsiku kutha popanda kuŵerenga Mawu a Mulungu. Makamaka lemba lolimbikitsa kwambiri ndilo Yohane 15:7, pamene limati: “Ngati mukhala mwa ine, ndi mawu anga akhala mwa inu, pemphani chimene chilichonse muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.”

Ndili ndi chiyembekezo cha kuona Rosaire m’dziko latsopano limene layandikira kwambiri. (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4) Atatsala pang’ono kufa mu 1975, anali kupita bwino patsogolo kulinga ku ubatizo. Panthaŵi ino, ndili wotsimikiza kulimbikira muutumiki wanthaŵi yonse ndi kupitirizabe kusangalala m’ntchito ya Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena