Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 3/15 tsamba 25-28
  • Kodi Ndibwino Kuti mwana Wanu Apite ku Sukulu Yaboding’i?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndibwino Kuti mwana Wanu Apite ku Sukulu Yaboding’i?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maphunziro ndi Umoyo Wauzimu
  • Chisonkhezero cha Ophunzira Anzawo
  • Chisonkhezero cha Aphunzitsi
  • Kuletsa Kuyendayenda
  • Kusiyana ndi Ena
  • Thayo la Makolo
  • Kodi Zilipo Njira Zina?
  • Mfungulo Zopezera Maphunziro Abwino
    Galamukani!—1996
  • Makolo—Khalani Ochirikiza a Mwana Wanu
    Galamukani!—1994
  • Sukulu Yopambana Yapadziko Lonse
    Galamukani!—1996
  • Sukulu Zili M’mavuto
    Galamukani!—1994
Nsanja ya Olonda—1997
w97 3/15 tsamba 25-28

Kodi Ndibwino Kuti mwana Wanu Apite ku Sukulu Yaboding’i?

YEREKEZERANI kuti mukukhala m’tauni yaing’ono m’dziko lomatukuka. Muli nawo ana angapo opita kusukulu yapulaimale, koma akafika zaka 12, adzafunikira kupita kusukulu yasekondale. Kudera kwanuko, sukulu zasekondale zilibe malo, zilibe ziŵiya zokwanira, ndipo zilibe aphunzitsi okwanira ndi ophunzitsa bwino. Nthaŵi zina sukuluzo zimatsekedwa kwa milungu ingapo ngakhale miyezi chifukwa cha masitalaka.

Munthu wina akupatsani kabuku kolongosola za sukulu yaboding’i ya mumzinda. Mukuona zithunzi za ophunzira achimwemwe ndi ovala bwino, akuphunzira m’makalasi, m’malaboletale, ndi m’malaibulale okhala nazo ziŵiya zabwino ndi zokwanira. Ophunzirawo akugwiritsira ntchito makompyuta ndipo pomapuma amangoti phee m’nyumba zawo zogonamo zaukhondo ndi zokongola. Muŵerenga kuti chimodzi cha zolinga za sukuluyo ndicho kuthandiza ophunzirawo “kupeza magiredi apamwamba opambana omwe angathe.” Muŵerenganso kuti: “Ophunzira onse ayenera kutsatira malamulo a khalidwe longa lija lofunikira m’banja, la ulemu, kudzichepetsa, kulemekeza makolo ndi achikulire, kugwirizana, kulolera, chifundo, kuona mtima ndi kukhulupirika.”

Mukupezamo mawu a mnyamata wina wosangalala onena kuti: “Makolo anga anandipatsa mwaŵi weniweni wa kuloŵa sukulu yabwino koposa.” Mtsikana wina akuti: “Sukulu njotsitsimula ndi yosangalatsa. Kunoko kuphunzira kumakoma kwabasi.” Kodi mungatumize mwana wanu mnyamata kapena mtsikana kusukulu yaboding’i yotero?

Maphunziro ndi Umoyo Wauzimu

Makolo onse osamala ana awo amafuna kuwayalira maziko olimba m’moyo, ndipo kuti achite zimenezo, maphunziro abwino amakhala ofunika. Kaŵirikaŵiri maphunziro akusukulu amatsegula khomo la mwaŵi wantchito mtsogolo ndipo amathandiza achichepere kudzakhala achikulire okhoza kudzisamala ndi kudzasamalanso mabanja awo mtsogolo.

‘Ngati sukulu yaboding’i imapereka maphunziro abwino limodzi ndi chiphunzitso cha khalidwe labwino, nkuuphonyeranji nanga mwaŵi umenewo?’ mungafunse motero. Kuti ayankhe funso limenelo, makolo achikristu ayenera kulingalira mwapemphero mfundo imodzi yofunika kwambiri​—umoyo wauzimu wa ana awo. Yesu Kristu anafunsa kuti: “Munthu apindulanji akadzilemezera dziko lonse, natayapo moyo wake?” (Marko 8:36) Kunena zoona, zimenezo sizingampindule kalikonse. Chifukwa chake, asanaganize zotumiza ana awo ku sukulu yaboding’i, makolo achikristu ayenera kulingalira za mmene zimenezi zidzakhudzira ziyembekezo za ana awo za moyo wosatha.

Chisonkhezero cha Ophunzira Anzawo

Sukulu zaboding’i zina zingakhale ndi miyezo yapamwamba ya maphunziro. Koma bwanji za miyezo ya makhalidwe ya aja oloŵa sukuluyo kapena ngakhale ena oyendetsa sukuluyo? Ponena za mtundu wa anthu omwe adzachuluka ‘masiku otsiriza’ ano, mtumwi Paulo analemba kuti: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.”​—2 Timoteo 3:1-5.

Kuwonongeka kwa makhalidwe ndi umoyo wauzimu kumeneku kuli vuto la padziko lonse, kupangitsa kukhala kovuta kuti Mboni za Yehova zitsatire mapulinsipulo a Baibulo. Ophunzira omwe amabwera kunyumba tsiku ndi tsiku amapeza kuti ngakhale kuyanjana kwawo kochepako ndi am’kalasi anzawo akunja kungakhale ndi chisonkhezero choipa champhamvu pa umoyo wawo wauzimu. Kulimbana ndi chisonkhezerocho kungakhale nkhondo yeniyeni kwa ana amene ali Mboni, ngakhale kuti tsiku ndi tsiku makolo awo amawapatsa chichirikizo, uphungu ndi chilimbikitso.

Nangano mkhalidwe uli motani kwa ana omwe amatumizidwa kutali ndi kwawo kusukulu zaboding’i? Iwo amalekanitsidwa, amamanidwa chichirikizo chauzimu chanthaŵi zonse cha makolo awo achikondi. Popeza kuti amakhala ndi am’kalasi anzawo maola onse 24 patsiku, chisonkhezero chakuti agwirizane ndi ambiri chimakhala champhamvu kwambiri pa maganizo ndi mitima yawo yanthete kuposa chomwe chimakhala pa ophunzira omwe amakhala kunyumba. Wophunzira wina anati: “Waboding’i amakhala pangozi yogwera m’khalidwe loipa kuchokera mmaŵa mpaka usiku.”

Paulo analemba kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Makolo achikristu asanyengedwe ndi kuganiza kuti ana awo sadzawonongeka mwauzimu ngati nthaŵi zonse ayanjana ndi aja osatumikira Mulungu. M’kupita kwa nthaŵi, chikumbumtima cha ana aumulungu chingakhale cholotchedwa ku makhalidwe achikristu ndipo angataye chiyamikiro chonse cha zinthu zauzimu. Nthaŵi zina zimenezi sizimaonekera kwa makolo kufikira ana awo atachoka pasukulu yaboding’i. Pamenepo kumakhala mmbuyo mwa alendo kuti awongolere zinthu.

Chitsanzo cha zimenezi ndi chochitika cha Clement. Iye akuti: “Ndisanapite kusukulu yaboding’i, ndinakonda kwambiri choonadi ndipo ndinkapita mu utumiki wakumunda ndi abale. Ndinakonda kwambiri kuyankha paphunziro la Baibulo lathu la banja ndi pa Phunziro la Buku la Mpingo. Komabe, nditangopita kusukulu yaboding’i ndili ndi zaka 14, ndinasiyiratu choonadi. Pazaka zonse zisanu zimene ndinakhala kusukulu yaboding’i, sindinapitepo kumisonkhano. Chifukwa cha mayanjano oipa, ndinayamba anamgoneka, kusuta, ndi kumwa kwambiri.”

Chisonkhezero cha Aphunzitsi

Pasukulu iliyonse pangakhale aphunzitsi a makhalidwe oipa amene amagwiritsira ntchito molakwa malo awo a ulamuliro. Ena amakhala ankhanza ndi aukali, pamene ena amachita chisembwere ndi ophunzira awo. M’sukulu zaboding’i zochita zawo aphunzitsi otero kaŵirikaŵiri zimangotha choncho osanenedwa.

Komabe, aphunzitsi ambiri amayesa moona mtima kuphunzitsa ana kuti akakhale othandiza anthu, kuti akakhale bwino m’dziko, kuti akadziŵe kukhala ndi anthu. Komano apa mpamene pali vuto lina kwa ana amene ali Mboni. Sinthaŵi zonse pamene makhalidwe a dziko amagwirizana ndi mapulinsipulo achikristu. Pamene aphunzitsi amalimbikitsa ophunzira kugwirizana ndi dziko, Yesu anati otsatira ake sayenera kukhala “a dziko lapansi.”​—Yohane 17:16.

Bwanji ngati pabuka mavuto kwa ana pamene atsatira mapulinsipulo a Baibulo? Ngati iwo amaloŵa sukulu yakumaloko ndipo amakhala kunyumba, angakambitsirane nkhanizo ndi makolo awo. Makolonso angalangize ana awo ndiponso mwina kukakambitsirana ndi mphunzitsi. Chotulukapo nchakuti, mavuto ndi malingaliro olakwa kaŵirikaŵiri amathetsedwa msanga.

Kusukulu zaboding’i zinthu zimakhala zosiyana. Ophunzira oterowo nthaŵi zonse amayang’aniridwa ndi aphunzitsi awo. Ngati ana achirimika pa mapulinsipulo achikristu, amatero popanda chichirikizo cha tsiku ndi tsiku cha makolo awo. Nthaŵi zina, ana amakhoza kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu m’mikhalidwe yotero. Koma kaŵirikaŵiri samatero. Nthaŵi zambiri mwana amangogonja pachifuniro cha mphunzitsi.

Kuletsa Kuyendayenda

Kusiyana ndi kumayunivesite, kumene ophunzira kaŵirikaŵiri ali nawo ufulu wa kubwera ndi kupita nthaŵi iliyonse imene afuna, pasukulu zaboding’i amaletsa ana kuyendayenda. Pasukulu zambiri zimenezi samalola ophunzira kuchoka m’sukulumo kusiyapo pa Sande, ndipo ena samalola ndi pa Sande pomwe. Eru wazaka 11, wophunzira pasukulu yaboding’i akunena kuti: “Oyang’anira sukulu samatilola konse kutuluka kuti tipite kumisonkhano, ngakhale ku utumiki wakumunda. Pasukulupo pamachitika mapemphero a Akatolika ndi Asilamu basi. Wophunzira aliyense ayenera kusankha pa ziŵirizo, apo phuluzi amatsutsidwa mwamphamvu ndi aphunzitsi ndi ophunzira anzake. Ophunzira amakakamizidwanso kuimba nyimbo yafuko ndi nyimbo za tchalitchi.”

Pamene makolo alembetsa ana awo m’sukulu zotero, kodi amakhala akuwauzanji ana awo? Angakhale akuwauza kuti maphunziro akusukulu ali ofunika kuposa misonkhano yakulambira ndi kukhala ndi phande m’ntchito yopanga ophunzira​—kuti amaposa ngakhale kusunga umphumphu kwa Mulungu.​—Mateyu 24:14; 28:19, 20; 2 Akorinto 6:14-18; Ahebri 10:24, 25.

Pasukulu zina zaboding’i, ophunzira amene ali Mboni amakhoza kuphunzira Baibulo pamodzi, koma ngakhale zimenezi zimakhala zovuta kaŵirikaŵiri. Wachichepere wina wotchedwa Blessing, wazaka 16, akunena izi ponena za sukulu yaboding’i imene anapitako: “Tsiku lililonse otchedwa Akristuwo amakumana kuti apemphere. Ife Mboni timayesa kuwachonderera kuti tiziphunzira, koma akuluakulu amatiuza kuti chipembedzo chathu nchosaloleka. Kenako amayesa kutikakamiza kuti tipemphere pamodzi nawo. Tikakana, amatipatsa chilango. Kukanena kwa aphunzitsi kumangoipitsiratu zinthu. Iwonso amatitcha maina osiyanasiyana ndi kuuza ophunzira akuluakuluwo kutilanga.”

Kusiyana ndi Ena

Pamene ophunzira pasukulu yaboding’i adziŵika poyera kuti ndi Mboni za Yehova, zimenezo zimawathandiza. Aphunzitsi angawapatule m’machitachita achipembedzo chonyenga owombana ndi chikhulupiriro cha Mboni. Ophunzira anzawo angaleke kuyesa kuwaloŵetsa m’machitachita ndi m’nkhani zosayenera. Angaloledwe kulalikira kwa ophunzira anzawo ndi aphunzitsi omwe. Ndiponso, awo omwe amatsatira mapulinsipulo achikristu samawaganizira kuti angachite zoipa zazikulu ndipo nthaŵi zina amapatsidwa ulemu ndi aphunzitsi ndi ophunzira anzawo.

Komabe, si nthaŵi zonse pamene zinthu zimawayendera bwino. Kukhala osiyana ndi ena kaŵirikaŵiri kumapangitsa achichepere kuzunzidwa ndi kusekedwa ndi ophunzira ndiponso ndi aphunzitsi omwe. Yinka, mnyamata wazaka 15 yemwe ali kusukulu yaboding’i, akuti: “Kusukulu, akakudziŵa kuti ndiwe Mboni ya Yehova, amafuna kukukhaulitsa. Pakuti amadziŵa umoyo wathu wauzimu ndi makhalidwe athu, amatitchera misampha kuti atikole.”

Thayo la Makolo

Palibe mphunzitsi, sukulu, kapena koleji iliyonse imene ingachite ntchito ya kuphunzitsa ana kukhala atumiki odzipatulira a Yehova. Imeneyo si ntchito yawo ndipo si thayo lawo. Mawu a Mulungu amanena molunjika kuti makolo eniwo ndiwo ayenera kusamalira zosoŵa zauzimu za ana awo. Paulo analemba kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Kodi makolo angagwiritsire ntchito motani uphungu waumulungu umenewu ngati ana awo ali kutali kusukulu yaboding’i kumene amalola kuwachezera kamodzi kapena kaŵiri kokha pamwezi?

Mikhalidwe imasiyana kwambiri, koma makolo achikristu amayesayesa kuchita mogwirizana ndi mawu ouziridwa aŵa: “Ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.”​—1 Timoteo 5:8.

Kodi Zilipo Njira Zina?

Kodi makolo angachitenji ngati aoneka kuti ali ndi zosankha ziŵiri chabe​—sukulu yaboding’i kapena sukulu yapafupi yosoŵa zofunikira? Ena omwe akhala mumkhalidwe umenewu alinganiza maphunziro apambali kuti awonjezere pa maphunziro a ana awo apasukulu yapafupi. Makolo ena amapatula nthaŵi yophunzitsa okha ana awo.

Nthaŵi zina makolo amapeŵa mavuto mwa kukonzekera pasadakhale zamtsogolo pamene ana awo adzafika msinkhu wopita kusekondale. Ngati muli ndi ana aang’ono kapena mukukonzekera kukhala ndi ana, mungaone ngati kudera kwanuko kuli sukulu yasekondale yoyenera. Ngati kulibeko, mwina kungakhale kotheka kusamukira kumene ili pafupi.

Monga momwe makolo amadziŵira bwino, pamafunikira luso, kuleza mtima, ndi nthaŵi yochuluka kuti wina aphunzitse ana kukonda Yehova. Ngati zimenezi nzovuta pamene mwana ali panyumba, koposa kotani nanga ngati mwanayo akukhala kutali! Popeza kuti izi zimakhudza moyo wosatha wa mwanayo, makolo ayenera kulingalira mwamphamvu ndi mwapemphero kuona ngati kuli kofunikira kuika mwana pangozi mwa kumpereka m’manja mwa sukulu yaboding’i. Kungakhale kusaona patali komvetsa chisoni ngati wina alepa umoyo wauzimu wa mwana wake kaamba ka mapindu a sukulu yaboding’i! Zimenezi zingakhale monga kuthamangira m’nyumba yokolera moto kuti apulumutse kanthu kakang’ono monga mphete​—basi nkupsera momwemo.

Mawu a Mulungu amati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” (Miyambo 22:3) Kuli bwino kupeŵa mkhalidwe woipa koposa kudzauwongolera pambuyo pake. Kungakhale kwanzeru kulingalira zimenezo ngati mudzifunsa kuti, ‘Kodi mwana wanga apite kusukulu yaboding’i?’

[Bokosi patsamba 28]

Mboni Zachichepere Zikusimba za Sukulu Yaboding’i

“Kusukulu yaboding’i, ana amene ali Mboni amamanidwa mayanjano auzimu. Ndi malo oipitsitsa osonkhezera kwambiri kuchita zolakwa.”​—Rotimi, yemwe anapita kusukulu yaboding’i pazaka 11 mpaka 14.

“Kupezeka kumisonkhano yachikristu kunali kovuta kwambiri. Ndinangopitako pa Sande pokha, ndipo ndinkachita kuzemba pamene ophunzira enawo anali pamzere woloŵa m’tchalitchi. Sindinali wachimwemwe konse, pakuti kunyumba ndinali nditazoloŵera kupita kumisonkhano yampingo, ndipo ndinkapita mu utumiki wakumunda pa Loŵeruka ndi pa Sande. Umoyo wa kusukulu sunali womangirira. Zambiri zinandipita.”​—Esther, yemwe ankakwapulidwa nthaŵi zonse ndi aphunzitsi chifukwa chokana kutenga mbali m’mapemphero atchalitchi.

“Kuchitira umboni kwa ophunzira anzanga kunali kovuta pasukulu yaboding’i. Nkovuta kukhala wosiyana ndi ena. Ndinafuna kutsatira khamu. Mwinamwake ndikanakhala wolimba mtima koposerapo ngati ndikanapita kumisonkhano ndi kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda. Koma ndinangochita zimenezo pamene ndinali patchuthi, katatu kokha pachaka. Ngati uli ndi nyali yopanda mafuta, imayamba kuzima. Nzimene zinali kuchitika kusukulu.”​—Lara, yemwe anali kusukulu yaboding’i kuchokera zaka 11 mpaka 16.

“Popeza kuti tsopano sindilinso kusukulu yaboding’i, ndine wachimwemwe kuti ndikhoza kupezeka pamisonkhano yonse, kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda, ndi kusangalala ndi lemba la tsiku ndi tsiku pamodzi ndi banja lonse. Ngakhale kuti kukhala kusukulu kunali ndi maubwino ena, palibe chilichonse chimene chingakhale chofunika koposa unansi wanga ndi Yehova.”​—Naomi, yemwe anakambirana ndi atate wake ndi kuwakhutiritsa kuti amchotse pasukulu yaboding’i.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena