Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 8/8 tsamba 3-4
  • Sukulu Zili M’mavuto

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sukulu Zili M’mavuto
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiwawa m’Sukulu
  • Makolo—Khalani Ochirikiza a Mwana Wanu
    Galamukani!—1994
  • Kufunafuna Maphunziro Abwino
    Galamukani!—1996
  • Kodi Nchiyani Chimene Chikuchitika m’Sukulu Lerolino?
    Galamukani!—1996
  • Mavuto a Uphunzitsi
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 8/8 tsamba 3-4

Sukulu Zili M’mavuto

Makolo amatumiza ana awo kusukulu kuti akaphunzire zambiri zoposa chabe kuŵerenga, kulemba, ndi masamu. Iwo amayembekezera sukulu kupereka maphunziro okwanira, amene amakonzekeretsa achichepere kukula kukhala achikulire amene makolo anganyadire. Koma kaŵirikaŵiri chiyembekezo chawo sichimakwaniritsidwa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti sukulu padziko lonse zili m’mavuto.

M’MAIKO ambiri kusoŵa kwa ndalama ndi aphunzitsi omwe kumaika paupandu maphunziro a ana. Mwachitsanzo, mu United States monse, kutsika kwa zandalama kwa m’zaka zaposachedwapa kunakakamiza sukulu zina kukonzanso ‘mabuku ophunzirira akale, kulola pulasitala wa siling’i kumatuka, kuchepetsa maprogramu a umisiri wa zinthu ndi maseŵero, kapena kutsekedwa kwa masiku ambiri pa nthaŵi ina,’ akutero magazini a Time.

Mu Afirika, magwero a zamaphunziro alinso osakwanira. Malinga ndi kunena kwa Daily Times ya ku Lagos, m’dziko la Nigeria ali ndi mphunzitsi 1 kwa ophunzira 70 alionse, “ndi kuthekera kwamphamvu kwakuti mmodzi mwa aphunzitsi atatu alionse ngwosayeneretsedwa.” Mu South Africa—kuwonjezera pa kupereŵera kwa aphunzitsi—kuchulukitsitsa kwa ana m’makalasi ndi chipolowe cha ndale zachititsa chimene South African Panorama imatcha “chipwirikiti m’sukulu za anthu akuda.”

Ndithudi, sukulu yokhala ndi aphunzitsi okwanira ndi ziŵiya zokwanira simatsimikiziritsa maphunziro achipambano. Mwachitsanzo, mu Austria, pafupifupi chigawo chimodzi mwa zitatu za azaka 14 akusimbidwa kuti sangathe kulemba masamu okhweka. Mu Britain, mlingo wa ophunzira amene akupambana m’masamu, sayansi, ndi chinenero cha dzikolo “uli wotsalira kwambiri kuposa wa ophunzira a mu Germany, France ndi Japan,” ikutero The Times ya ku London.

Mu United States, aphunzitsi amadandaula kuti ngakhale kuti ophunzira amapeza mamalikisi apamwamba m’mayeso, ambiri amakhalabe osakhoza kulemba chimangirizo chabwino, kulemba masamu, kapena kukonza ndemanga zachidule za mfundo zazikulu za maphunziro osiyanasiyana kapena nkhani. Monga chotulukapo chake, akuluakulu a zamaphunziro padziko lonse akupendanso makosi a sukulu ndi njira zogwiritsiridwa ntchito zonse kupenda kupita patsogolo kwa wophunzira.

Chiwawa m’Sukulu

Malipoti amasonyeza mlingo wowopsa ndi wowonjezereka wa chiwawa m’sukulu. Mu Germany, msonkhano wa aphunzitsi unauzidwa kuti 15 peresenti ya ana asukulu ali “okonzekera kuchita chiwawa—ndipo 5 peresenti samazengereza ngakhale kuchita machitachita ankhanza kwambiri, kwakuti angaponde chidyali munthu wosadzitetezera wogona pansi.”—Frankfurter Allgemeine Zeitung.

Nkhani za anthu osiyanasiyana za kuchitira nkhanza kopambanitsa zimadetsa nkhaŵa yaikulu. Kugwiriridwa chigololo kwa mtsikana wazaka 15 ndi achichepere anayi m’chimbudzi cha pa sukulu yasekondale ku Paris kunachititsa ophunzira kupita m’makwalala kukaonetsera poyera kupempha chitetezo champhamvu pasukulu. Makolo amadera nkhaŵa ndi kuwonjezereka kwa kuukira kwa kugonana, kulanda, ndi chiwawa cha maganizo. Zochitika zotero sizimachitika ku Ulaya kokha koma zikukhala zofala kwambiri padziko lonse.

Unduna wa Zamaphunziro wa ku Japan ukusimba za kuwonjezeka kwa chiwawa choyambukira ponse paŵiri ophunzira a makalasi apansi ndi apamwamba a sukulu yasekondale. Nyuzipepala ya ku South Africa ya The Star, pansi pa mutu wakuti “Ophunzira Onyamula Mfuti Alanda Sukulu,” inayerekezera zochitika za m’makalasi ambiri a ku Soweto ndi zija za “Wild West” mu United States mkati mwa zaka za zana la 19. Ngakhale mbiri yachiwawa ya ku New York City yafika, mogwirizana ndi mawu a The Guardian ya ku London, “pa mlingo watsopano ndi chilengezo choperekedwa ndi kampani ya zachitetezo cha kuwonjezereka kwa maoda a zovala za ana asukulu zosaloŵa zipolopolo.”

Britain nayenso akuvutika ndi mliri wa chiwawa m’sukulu. “M’zaka 10 zapitazo,” akutero mkulu wina wa gulu lochirikiza zofuna za aphunzitsi, “taona chikhoterero chomakula cha kutenga zida. Icho chayambukiranso a misinkhu yaing’ono ndipo chikufalikira kuyambira kwa amuna mpaka akazi.”

Pamenepo, nkosadabwitsa kuti makolo angapo amasankha kuchotsa ana awo kusukulu ndi kuwaphunzitsira panyumba. Awo amene amapeza zimenezi kukhala zosathandiza kaŵirikaŵiri amadera nkhaŵa za chiyambukiro choipa chimene sukulu ili nacho pa ana awo, ndipo amakayika kuti angathetse motani zimenezi. Kodi nchiyani chimene makolo angachite kuthandiza ana awo kulimbana ndi mavuto amene amakumana nawo kusukulu? Ndipo kodi makolo angagwirizane motani ndi aphunzitsi kutsimikizira kuti ana akulandira zabwino koposa kusukulu? Nkhani zotsatira zikupereka mayankho a mafunso ameneŵa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena