Kodi Nchiyani Chimene Chikuchitika m’Sukulu Lerolino?
“SUKULU Zathu Zili m’Mavuto: Bweretsani Apolisi Tsopano Lino.” umenewo ndiwo unali mutu wa patsamba loyamba la nyuzipepala yaposachedwapa ku New York City. New York City Board of Education ili ndi alonda akeake a sukulu—gulu la antchito 3,200—limene limayang’anira sukulu za mumzinda zoposa 1,000. Tsopano ambiri akufuna kuti apolisi a mumzinda awabweretse m’sukulu kuti azithandiza pa chisungiko. Kodi iwo akufunikadi?
Mutu wina wa mu New York Times unati: “Ofufuza Apeza Kuti 20% ya Ophunzira mu New York City Amanyamula Zida.” Mkulu wa sukulu za mu New York City kuyambira 1990 kufikira 1992, Joseph Fernandez, anavomereza kuti: “Sindinayambe ndaonapo chiwawa chonga chimene tili nacho tsopano m’sukulu za m’mizinda yathu yaikulu. . . . Pamene ndinalandira undindo wa kukhala mkulu wa sukulu mu New York mu 1990 sindinaganize kuti zinthu zidzakhala zoipa chonchi. Suli mkhalidwe wina wongopyola, ndi mkhalidwe wakupha.”
Kodi Ngwoipa Kufikira Pati?
Fernandez anasimba kuti: “M’miyezi yanga khumi yoyamba monga mkulu wa sukulu, mwana wa sukulu mmodzi anali ataphedwa masiku aŵiri alionse—kubayidwa ndi mpeni m’njanje zapansi pa nthaka, kuwomberedwa ndi mfuti pasukulu kapena pamphambano za misewu . . . Sukulu zina zasekondale zili ndi [alonda] khumi ndi asanu kapena khumi ndi asanu ndi mmodzi olonda m’malikole ndi mabwalo.” Anawonjezera kuti: “Chiwawa m’sukulu zathu chili mliri, ndipo njira zapadera zatengedwa. Sukulu za ku Chicago, Los Angeles, Detroit—mizinda yonseyo yaikulu—tsopano zili zofanana pa nkhanza yowopsayo.
“Manyazi ochititsidwa ndi mkhalidwewu ngachionekere kwambiri. M’zaka makumi aŵiri zapitazi tavomereza zosavomerezeka: Sukulu za America kukhala malo ankhondo. Nyumba zochititsa mantha m’malo mwa kukhala malo otsegulirako anthu maso.”
M’sukulu 245 za mu United States muli maofesala olonda, ndipo pa 102 za sukuluzi, maofesala ake amakhala ndi mfuti. Komatu si iwo okha amene ali ndi mfuti. Malinga ndi kufufuza kwa University of Michigan, kukuyerekezeredwa kuti ophunzira a mu United States amanyamula mfuti 270,000 ku sukulu tsiku lililonse, kupatulapo zida zina!
M’malo mwa kuwongokera, mkhalidwewo waipa kwambiri. Ziŵiya zodziŵira zitsulo zobisidwa zogwiritsiridwa ntchito m’sukulu zambiri zalephera kuletsa zida kumabwera. Mumphakasa ya 1994, ziwawa zimene zinachitiridwa lipoti m’sukulu za New York City zinakwera kufika pa 28 peresenti poyerekezera ndi zimene zinachitika m’nyengo yofanana nayo mu chaka chapitacho! “Kwa nthaŵi yoyamba,” ikufotokoza motero Phi Delta Kappan ponena za kufufuza kumene kunachitidwa mu United States, “‘kumenyana, chiwawa, ndi timagulu tachiwawa ta anyamata’ tili pamalo oyamba mofanana ndi ‘kupanda mwambo’ zimene zili vuto lalikulu koposa limene likuyang’anizana ndi sukulu zaboma za kumalo ano.”
Chiwawa cha pasukulu chachititsa mavuto m’sukulu m’maiko ambiri. Ku Canada, Globe and Mail ya Toronto inali ndi nkhani ya mutu wakuti: “Sukulu Zikukhala Malo Angozi.” Ndipo kufufuza kwina ku Melbourne, Australia, kunavumbula kuti pafupifupi 60 peresenti ya ana a sukulu zapulaimale makolo awo amakawasiya kusukulu ndiponso kukawatenga pagalimoto powopera kuti angavulazidwe kapena kubedwa.
Komabe, chiwawa changokhala mbali ina ya vutolo. Pali zinthu zina zimene zikuchitika m’sukulu zathu zimene zikuchititsa nkhaŵa yaikulu.
Nkhani ya Makhalidwe
Ngakhale kuti Baibulo limanena kuti dama—kugonana popanda ukwati—nloipa, lerolino sukulu sizimachirikiza chiphunzitso chanzeru chamakhalidwe chimenecho. (Aefeso 5:5; 1 Atesalonika 4:3-5; Chivumbulutso 22:15) Ndithudi zimenezi zachirikiza mkhalidwe umene Fernandez anaulongosola pamene anati: “Achichepere athu pafupifupi 80 peresenti amachita chisembwere.” Pasukulu ina yasekondale ku Chicago, mtsikana mmodzi mwa atatu alionse anali ndi pathupi!
Sukulu zina zili ndi sukulu zamkaka zosamalira makanda a ophunzira. Ndiponso, makondomu amaperekedwa nthaŵi zonse pa kuyesayesa kosaphula kanthu kuthetsa mliri wa AIDS ndi wa kuchuluka kwa ana apathengo. Ngati kuperekedwa kwa makondomu sikumalimbikitsa kwenikweni ophunzira kuchita chisembwere, ndiye kuti kumawaloleza kutero. Pankhani ya makhalidwe, kodi ophunzirawo ayenera kuganizanji?
Mphunzitsi wina wa payunivesite wanthaŵi yaitali anati pali “chiŵerengero chachikulu cha achinyamata amene amaganiza kuti palibe chabwino kapena choipa, amati makhalidwe abwino amadalira pa zimene umalingalira.” Kodi nchifukwa ninji achichepere amaganiza motere? Mphunzitsiyo anati: “Mwinamwake chinali chifukwa cha zimene anakumana nazo kusukulu yasekondale zimene zinawapangitsa kukhala osadziŵa makhalidwe abwino.” Kodi chotulukapo chake nchotani pamakhalidwe osadziŵika amenewo?
Nkhani ina yaposachedwapa m’nyuzipepala inanena modandaula kuti: “Nthaŵi zina kumaoneka ngati kuti, palibe aliyense amene ali ndi mlandu. Palibiretu.” Inde, zimenezi zimapereka uthenga wakuti chinthu chilichonse chili chololeka! Taonani chitsanzo chosonyeza mmene zimenezi zingakhudziredi ophunzira. M’kalasi ina yapayunivesite pophunzira za Nkhondo Yadziko II ndi kuyamba kwa Chinazi, profesa wina anapeza kuti ochuluka a ophunzira ake sanakhulupirire kuti panali wina aliyense amene anali ndi mlandu kaamba ka Chipululutso cha Anazi! “M’maganizo a ophunzirawo,” mphunzitsiyo anatero, “Chipululutso cha Anazi chinali ngati tsoka lachilengedwe: Chinali chosaletseka ndipo chosapeŵeka.”
Kodi umakhala mlandu wayani pamene ophunzira alephera kusiyanitsa chabwino ndi choipa?
Mkati mwa Nthaŵi Zoŵaŵitsa
Pokhalira mbali sukulu, yemwe kale anali mphunzitsi anati: “Vutoli limayambira m’chitaganya, ndipo sukulu zimangosonyeza mavuto amene alipo kale m’chitaganya.” Indedi, nkovuta kuphunzitsa bwinobwino zimene atsogoleri a m’chitaganya amalephera kuchita.
Mwachitsanzo, mkati mwa nthaŵi imene makhalidwe oipa a akuluakulu a boma la United States anali mitu yankhani, wolemba nkhani m’danga la nyuzipepala wina wotchuka analemba kuti: “Sindikudziŵa mmene aphunzitsi a mumbadwo uno wosuliza zinthu angayeseyesere kuphunzitsa makhalidwe abwino. . . . ‘Taonani zimene zikuchitika ku Washington!’ ngakhale ophunzira achichepere angatsutse. Amadziŵa . . . kuti chinyengo choipitsitsa m’mbiri chachitika m’nyumba yaikulu yoyera ija.”
Baibulo linaneneratu kuti mu “masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Zoonadi zinozo ndi nthaŵi zoŵaŵitsa! Polingalira zimenezi, kodi nchiyani chimene chikuchitidwa kulimbana ndi mavuto m’sukulu lerolino ndi kuthandiza ophunzira kupeza maphunziro abwino? Kodi inuyo monga makolo ndi inunso ophunzira mungachitenji? Nkhani zotsatira zidzafotokoza zimenezi.