Kupulumutsidwa m’Nthaŵi ya Tsoka
SITOLO ina yaikulu yosanjikizana kanayi ku Seoul, Korea, inagumuka mwadzidzidzi, ndipo anthu mazanamazana anasoŵa kotulukira! Antchito yopulumutsa anthu anagwira ntchito usana ndi usiku kuti apulumutse miyoyo ya anthu ambiri amene angathe. Patapita masiku angapo, chiyembekezo choti nkupeza opulumuka enanso amene anakwiriridwa m’mulu wa konkiri ndi zitsulo, chinayamba kuchepa.
Pamene chiyembekezo chonse chinatheratu, kunachitika chinachake chodabwitsa. Kulira kwa munthu wofooka komvetsa chisoni kunamveka pansi pa miyala ndi zitsulo zophwanyikazo. Opulumutsa anafukula ndi manja awo mitima ili m’malere, kuti apulumutse msungwana wazaka 19 zakubadwa, amene anakwiriridwa wamoyo kwa masiku 16. Iye anaunthama mkati mwa njira ya chikepe imene inagwa kotero kuti miyala imene inkagumukayo sinamupsinje. Ngakhale kuti anali atatheratu madzi m’thupi ndi kutemekatemeka, ayi ndithu anaithaŵa imfa!
Masiku ano, mwezi sungapite osamvako za malipoti a tsoka, monga chivomezi, mkuntho wowononga, volokano, ngozi, kapena njala. Ndipo nkhani zochititsa nthumanzi za kupulumutsidwa ndi kupulumuka kwa anthu zimachititsa chidwi anthu mamiliyoni ambiri amene amatsatira nyuzi. Komabe, chenjezo la tsoka limene likudza—tsoka lalikulu koposa m’mbiri ya munthu—angolinyalanyaza. (Mateyu 24:21) Baibulo limafotokoza chochitika chimenecho motere: “Taonani, zoipa zidzatuluka ku mtundu kumka m’mitundu, ndipo namondwe adzauka kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera ku malekezero ena a dziko lapansi kumka ku malekezero ena a dziko lapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndoŵe panthaka.”—Yeremiya 25:32, 33.
Mawu odetsa nkhaŵa! Koma mosiyana ndi masoka achilengedwe kapena ngozi, tsoka limeneli silidzakhala kupha kwachisawawa. Kwenikweni, kupulumuka—kupulumuka kwanu—nkotheka!
Nthaŵi ya Chenjezo
Kuti umvetsetse zimenezi, choyamba uyenera kudziŵa chifukwa chimene tsoka la dziko lonseli lidzabwerera. Kwenikweni, ndilo chothetsera chokha chenicheni cha mavuto a anthu. Lerolino, ndi anthu ochepa amene amadzimva otetezereka ndi osungika. Mosasamala kanthu za kuyesayesa kosamalitsa kwa asayansi, matenda opatsirana akupitirizabe kusakaza anthu padziko lonse. Nkhondo zochitika chifukwa cha kusiyana maganizo kwa zipembedzo, mafuko, ndi zandale zikusakaza miyoyo ya anthu zikwizikwi. Njala ikuwonjezera kuvutika kwa amuna, akazi ndi ana osalakwa. Makhalidwe oipa akuwononga maziko a moyo wa anthu; ngakhale ana asokonezeka.
Mosapita m’mbali konse, ulosi wa Baibulo wolembedwa zaka zoposa 1,900 zapitazo umafotokoza za mkhalidwe wathu. Umanena kuti: “Muyenera kuzindikira kuti masiku otsiriza nthaŵi zidzadzaza ndi zoopsa.”—2 Timoteo 3:1, The New Testament in Modern English, lolembedwa ndi J. B. Phillips; yerekezerani ndi Mateyu 24:3-22.
Kodi zikuoneka zanzeru kwa inuyo kuti Mulungu wachikondi anganyalanyaze mkhalidwe wathu? Baibulo limanena kuti: “Iye ndiye Mulungu (woona, NW) amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; . . . sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Zoonadi, m’malo moti pulaneti lokongolali likhale bwinja ndi okhalamo ake athe psiti, Mulungu adzaloŵererapo. Funso nlakuti, Kodi adzachita motani zimenezo?
Sankhani Moyo!
Baibulo likuyankha motere pa Salmo 92:7: “Pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzawonongeke kosatha.” Mulungu adzathetsa mavuto a dzikoli mwakuchotsa kuipa kwenikweniko. Chosangalatsa nchakuti izi sizikutanthauza kuti anthu onse adzachotsedwa. Salmo 37:34 likutitsimikizira motere: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko: pakudulidwa oipa udzapenya.”
Mawu ameneŵa akusonyeza kuti pali chiyembekezo choti tingapulumuke kupyola tsoka lalikulu koposali limene silinagwerepo mtundu wa anthu. Mulungu watipatsa mwaŵi wosankha. Mawu amene Mose anachenjeza nawo Aisrayeli pamene anali kuyembekezera kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa akugwira ntchito yofananayo lerolino: “Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu.” (Deuteronomo 30:19) Komabe, kodi munthu ‘angasankhe moyo motani’ ndi kupulumuka? Kodi chipulumutso chenicheni chimatanthauzanji?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
PACHIKUTO: Kuphulika: Copyright © Gene Blevins/Los Angeles Daily News
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Yunhap News Agency/Sipa Press