Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w10 5/1 tsamba 14-15
  • Khalani Olimba Mtima Potsatira Zimene Mumakhulupirira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Olimba Mtima Potsatira Zimene Mumakhulupirira
  • Nsanja ya Olonda—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Yesu Sanagonje Poyesedwa
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Yesu Achiritsa Anthu Mozizwitsa
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Chiwembu Chibwerera Eni Ake
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2010
w10 5/1 tsamba 14-15

Zoti Achinyamata Achite

Khalani Olimba Mtima Potsatira Zimene Mumakhulupirira

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera mumtima mwawo.

Amene Akutchulidwa Kwambiri M’nkhaniyi: Yeremiya, Ebedi-Meleki, mfumu Zedekiya

Chidule cha Nkhaniyi: Yeremiya akutsutsidwa kwambiri ndi anthu a ku Yuda pamene akulengeza uthenga wa Mulungu wakuti Ayudawo asalimbane ndi magulu ankhondo a Akasidi.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI YEREMIYA 38:1-5.

Kodi mukuganiza kuti Yeremiya ankamva bwanji mumtima mwake pamene ankalengeza uthenga wa Mulungu kwa Ayuda?

․․․․․

Mukaona mawu amene Yeremiya ananena polengeza chenjezo la Yehova, kodi mukuganiza kuti ankamva bwanji mumtima mwake?

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.

Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chinamulimbitsa mtima Yeremiya kuti alengeze uthenga umenewu?

․․․․․

2 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI YEREMIYA 38:6-13.

Kodi mukuganiza kuti Yeremiya anaponyedwa m’dzenje lakuya ndiponso lalikulu motani? Nanga mukuganiza kuti munkamveka fungo lotani?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti pamene Yeremiya anayamba ‘kumira m’thope’ ankaganiza zotani? (Werenganinso vesi 6.)

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.

Pogwiritsa ntchito mabuku osiyanasiyana, fufuzani zinthu zina zimene poyamba simumazidziwa zokhudza zitsime zimene anthu ankagwiritsira ntchito m’nthawi za Baibulo.

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chinalimbitsa mtima Ebedi-Meleki kuti apulumutse Yeremiya? (Werenganinso vesi 7-9.)

․․․․․

Poyamba, Zedekiya anamvera zonena za akalonga koma atamva zonena za Ebedi-Meleki anasinthanso maganizo nthawi yomweyo. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Zedekiya ankangoyendera zonena za ena? (Werenganinso vesi 5 ndi 10.) Kodi zimenezi zikusonyeza kuti iye anali wotani? Nanga mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani ankangosinthasintha maganizo?

․․․․․

Pa anthu amene atchulidwa m’nkhaniyi, kodi ndi anthu awiri ati amene anasonyeza kuti ankachita zinthu motsimikiza? Nanga ndi munthu uti amene sanasonyeze khalidwe limeneli? N’chifukwa chiyani mwayankha choncho?

․․․․․

3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA . . .

Kulimba mtima.

․․․․․

Kuchita zinthu motsimikiza.

․․․․․

Mmene Yehova amatetezera anthu amene amamumvera mopanda mantha.

․․․․․

Kodi kukhala otsimikiza pa zimene mumakhulupirira kungakuthandizireni bwanji kuchita zoyenera ngakhale muli pampanipani?

․․․․․

4 M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI MTIMA KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

NGATI MULIBE BAIBULO, MUNGAWERENGE LA PA INTANETI PA WEBUSAITI YATHU YA www.jw.org.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena