Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w11 1/1 tsamba 30-31
  • Muziyamikira Zinthu Zopatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muziyamikira Zinthu Zopatulika
  • Nsanja ya Olonda—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Yesu Achiritsa Anthu Mozizwitsa
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Yesu Anagometsa Anthu ndi Mawu Ake
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Mose Anapatsidwa Ntchito Yapadera
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2011
w11 1/1 tsamba 30-31

Zoti Achinyamata Achite

Muziyamikira Zinthu Zopatulika

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera mumtima mwawo.

Amene akutchulidwa kwambiri m’nkhaniyi: Isaki, Rabeka, Yakobo ndi Esau.

Chidule cha Nkhaniyi: Esau anagulitsa ukulu wake kwa Yakobo amene anabadwa naye mapasa.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI GENESIS 25:20-34.

Kodi Yakobo ndi Esau ankaonetsa makhalidwe otani ngakhale pamene anali m’mimba mwa mayi awo?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Yakobo ndi Esau ankaoneka bwanji ali anyamata?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Yakobo ndiponso Esau ankamva bwanji mumtima mwawo pamene ankakambirana zimene zili mu vesi 30 mpaka 33?

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.

Gwiritsani ntchito zinthu zofufuzira zimene muli nazo kuti mudziwe mwayi umene munthu ankakhala nawo chifukwa chokhala mwana wamwamuna woyamba kubadwa. N’chifukwa chiyani zimenezi zinali zofunika? Kodi kugulitsa mwayi umenewo ndi mbale ya mphodza kunatanthauza chiyani?

․․․․․

2 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI GENESIS 27:1-10, 30-38.

Kodi mukuganiza kuti mawu a Esau ankamveka bwanji pamene ankalankhula atazindikira kuti m’bale wake walandira madalitso amene mwana woyamba kubadwa ankalandira?

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.

Kodi Rabeka ndi Yakobo analakwa pokonza zoti Yakobo alandire madalitso m’malo mwa Esau? N’chifukwa chiyani mwayankha choncho? (Zokuthandizani: Werengani Genesis 25:23, 33.)

․․․․․

3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA . . .

Kuipa kofuna kudzisangalatsa nthawi yomweyo.

․․․․․

MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO MFUNDOZI.

Kodi ndi zinthu zopatulika ziti zimene inuyo mwapatsidwa?

․․․․․

Kodi mungachite chiyani posonyeza kuti mumayamikira zinthu zopatulika?

․․․․․

4 M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI MTIMA KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

Ngati mulibe Baibulo, uzani a Mboni za Yehova, kapena kawerengeni Baibulo lachingerezi pa adiresi ya pa Intaneti iyi: www.jw.org.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena