Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 8/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chipembedzo Choona Mungachidziwe Bwanji?
    Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • Kodi Pali Uthenga Wabwino Wotani Wokhudza Zipembedzo?
    Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • Kodi Chipembedzo Choona Mungachidziwe Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 8/1 tsamba 16
A Mboni za Yehova a mitundu yosiyanasiyana akucheza mu Nyumba ya Ufumu

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi zipembedzo zonse zimakondweretsa Mulungu?

N’kutheka kuti munamvapo nkhani zosonyeza zinthu zoipa zimene zimachitika m’dzina la chipembedzo. Mwina munamva nkhani zimenezi pa wailesi kapena munawerenga m’nyuzipepala. Zimenezi zikusonyeza kuti si zipembedzo zonse zimene zimakondweretsa Mulungu. (Mateyu 7:15) Izitu ndi umboni wakuti anthu ambiri asocheretsedwa.—Werengani 1 Yohane 5:19.

Komabe, Mulungu amachita chidwi ndi anthu amene amafunitsitsa kuchita zabwino komanso kumulambira m’njira imene iye amafuna. (Yohane 4:23) Mulungu akuthandiza anthu amenewa kuti aphunzire zolondola kudzera m’Mawu ake, Baibulo.—Werengani 1 Timoteyo 2:3-5.

Kodi mungadziwe bwanji chipembedzo choona?

Yehova Mulungu akuphunzitsa choonadi anthu omwe poyamba anali m’zipembedzo zosiyanasiyana ndipo akuthandiza anthuwa kuti akhale ogwirizana komanso okondana. (Mika 4:2, 3) Choncho, chizindikiro china cha chipembedzo choona ndi choti anthu ake amakondana.—Werengani Yohane 13:35.

Yehova Mulungu akuphunzitsa choonadi anthu osiyanasiyana ndipo akuthandiza anthuwa kuti akhale ogwirizana.—Salimo 133:1

Zinthu zimene anthu a m’chipembedzo choona amakhulupirira zimachokera m’Baibulo. Anthuwa amayesetsa kutsatira zimene amaphunzira m’Baibulo pa moyo wawo. (2 Timoteyo 3:16) Iwo amauza anthu dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Ndipo amathandiza anthu kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto padzikoli. (Danieli 2:44) Iwo amatengera chitsanzo cha Yesu ndipo ‘amaonetsa kuwala’ pochitira zabwino anthu. (Mateyu 5:16) Akhristu oona amadziwikanso chifukwa amapita kunyumba za anthu n’kumakawauza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Werengani Mateyu 24:14; Machitidwe 5:42; 20:20.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 15 m’buku ili lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena