Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 4/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 4/1 tsamba 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi anthu adzakhala ndi moyo wotani m’tsogolo?

Banja likupereka mphatso kwa mayi wachikulire wa mtundu wina

Kodi imfa ya yesu idzathandiza bwanji kuti anthu onse azikondana?

N’zodziwikiratu kuti asayansi apitirizabe kupanga zinthu zamakono zomwe zisinthe mmene timachitira zinthu ndi ena. Koma kodi zimenezi zidzathandiza kuti anthu padzikoli ayambe kuchita zinthu moganizirana? Ayi. Anthu ambiri m’dzikoli ndi odzikonda komanso adyera. Koma cholinga cha Mulungu n’choti anthu adzakhale osangalala padzikoli.—Werengani 2 Petulo 3:13.

Baibulo limanena kuti m’tsogolomu anthu padziko lonse adzakhala ogwirizana komanso okondana kwambiri. Anthu adzakhala otetezeka chifukwa palibe adzawachitire zoipa.—Werengani Mika 4:3, 4.

Kodi Mulungu adzathetsa bwanji kudzikonda?

Mulungu analenga anthu opanda mtima wodzikonda. Koma chifukwa chosamvera Mulungu, Adamu yemwe anali munthu woyamba, anataya mwayi wokhala wangwiro. Anthufe tinatengera mtima wodzikonda kuchokera kwa Adamu, yemwe ndi kholo lathu. Komabe Mulungu adzagwiritsa ntchito Yesu kuti athandize anthu kukhalanso angwiro.—Werengani Aroma 7:21, 24, 25.

Kuti zimenezi zidzatheke, Yesu anatifera kuti alipire kusamvera kwa Adamu. (Aroma 5:19) Imfa ya Yesu idzathandiza kuti anthu onse okhala padzikoli asamadzachite zoipa chifukwa cha mtima wodzikonda.—Werengani Salimo 37:9-11.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 5 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena