Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 10/1 tsamba 5
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Amafuna Kuti Tizipemphera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Amafuna Kuti Tizipemphera?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu amafuna kuti tikhale anzake.
  • Mulungu amafunitsitsa kutithandiza.
  • Tinalengedwa ndi mtima wofuna kulambira Mulungu.
  • Kodi Mulungu Amamva Mapemphero Anu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kuyandikira kwa Mulungu m’Pemphero
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 10/1 tsamba 5

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUPEMPHERA N’KOTHANDIZADI?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amafuna Kuti Tizipemphera?

Mulungu amafuna kuti tikhale anzake.

Anthu omwe ndi mabwenzi amagwirizana kwambiri ngati amalankhulana. Nayenso Mulungu amafuna kuti tizilankhula naye m’pemphero kuti tikhale anzake apamtima. Ndipo amanena kuti: “Mudzaitanira pa ine komanso mudzabwera ndi kupemphera kwa ine ndipo ine ndidzakumvetserani.” (Yeremiya 29:12) Mukamapeza nthawi yolankhula ndi Mulungu, ‘mudzamuyandikira ndipo iyenso adzakuyandikirani.’ (Yakobo 4:8) Ndipotu Baibulo limati: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.” (Salimo 145:18) Nthawi zonse tikamayesetsa kulankhulana ndi Mulungu, m’pamenenso timakhala anzake apamtima.

“Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.”—Salimo 145:18

Mulungu amafunitsitsa kutithandiza.

Nthawi ina Yesu ananena kuti: “Ndani pakati panu amene mwana wake atamupempha mkate, iye angamupatse mwala? Kapena atamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? Chotero ngati inuyo, . . . mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapereka zinthu zabwino kwa onse om’pempha!” (Mateyu 7:9-11) Mulungu amafuna kuti muzipemphera kwa iye chifukwa “amakuderani nkhawa” ndipo amafuna kukuthandizani. (1 Petulo 5:7) Amafuna kuti muzimufotokozera mavuto anu. Baibulo limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6.

Tinalengedwa ndi mtima wofuna kulambira Mulungu.

Akatswiri ena ananena kuti anthu ambiri padzikoli amaona kuti kupemphera n’kofunika. Anati ngakhale anthu omwe sakhulupirira kuti kuli Mulungu komanso amene amakayikira zoti kuli Mulungu, nawonso amapemphera.a Zimenezi zimasonyeza kuti anthufe tinalengedwa ndi mtima wofuna kulambira Mulungu. Ndipotu Yesu anati: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyu 5:3) Choncho kupemphera ndi njira ina imene timalambirira Mulungu.

Ndiye kodi tingapeze phindu lanji tikamapemphera kwa Yehova?

a M’chaka cha 2012, bungwe lina linachita kafukufuku ku United States. Bungweli linapeza kuti anthu 11 pa anthu 100 alionse omwe sakhulupirira kuti kuli Mulungu kapena omwe amakayikira zoti kuli Mulungu, amapemphera kamodzi pa mwezi.

Kodi Tinganene Chiyani Popemphera?

Baibulo limasonyeza kuti tikhoza kunena zinthu zosiyanasiyana popemphera. Mwachitsanzo tikhoza:

  • Kuulula Machimo “Ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa.”—Salimo 32:5.

  • Kumuyamikira “Ndi bwino kuyamika inu Yehova.”—Salimo 92:1.

  • Kumutamanda “Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse. Ndidzamutamanda ndi pakamwa panga mosalekeza.”—Salimo 34:1.

  • Kumupempha Kuti Atitsogolere “Ndiyendetseni m’njira ya malamulo anu, pakuti ndikukondwera ndi njira imeneyi.”—Salimo 119:35.

  • Kupempha Kuti Mulungu Atipatse Mphamvu “Ndicheukireni ndi kundikomera mtima. Patsani mtumiki wanu mphamvu.”—Salimo 86:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena