Kodi Adzamva Bwanji Ngati Sitibwererako?
1 “Adzamva bwanji wopanda wolalikira?” (Aroma 10:14) Zoonadi, kodi adzazindikira bwanji tanthauzo la choonadi ngati sitipanga maulendo obwereza ogwira mtima? Kulikonse kumene tinali okhoza kukambitsirana ndi mwininyumba ponena za uthenga wa Ufumu kumayenerera ulendo wobwereza. Mwezi uno tingakhoze kubwerera kwa amene tinakambitsirana nawo poyamba tili ndi mfundo zowonjezereka za Malemba zochokera m’brosha lililonse limene tinagaŵira, ndi limene lingakuloŵetseni mwachipambano m’phunziro la Baibulo.
2 Ngati munagaŵira brosha lakuti “Kodi Mulungu Amatisamaliradi?,” mungakhoze kuyambitsa makambitsirano amene angakuloŵetseni m’phunziro la Baibulo mwanjira iyi. Posonyeza chithunzithunzi pa masamba 2-3, mungafunse kuti:
◼ “Kodi mungakonde kukhala ndi moyo m’dziko limene mtsogolo mosungika muli motsimikizirika kwa inu ndi banja lanu? [Yembekezerani yankho. Ndiyeno tembenukirani ku ndime 1 ndi 2 za Chigawo 1.] Tonsefe tili ndi chikhumbo chimenechi, ngakhale kuti ambiri amakayikira kuti sizidzatheka konse. Kwa Mulungu, amene akulonjeza kukwaniritsa zimenezi, zimenezi nzotheka.” Ŵerengani Yesaya 32:17, 18 m’Baibulo lanu. Pitirizani, kulongosola kuti pali anthu padziko lonse amene ali ndi chisangalalo kale ndi mtendere wamaganizo umene umadza ndi chiyembekezo chotsimikizirika kaamba ka mtsogolo. Kambitsiranani malingaliro a Malemba a m’ndime 4 ya Chigawo 2, ndiyeno fotokozani mmene phunziro la broshalo lingathandizire mwininyumba kuphunzira zambiri. Pangani makonzedwe obwererako mwamsanga kudzapitiriza kukambitsiranako,
3 Pamene mubwererako mutagaŵira kabuku kakuti “Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?,” mwinamwake mawu onga awa angakhale ogwira mtima:
◼ “Paulendo wanga wapapitawo, tinakambitsirana za funso lakuti, Kodi kuli Mulungu amene amasamala? Kodi muganiza kuti Mulungu amasamaladi za ife kwakuti akhoza kuthetsa kuvutika ndi chiwawa? [Munthuyo atayankha, tembenukirani pa ndime 32 ndi kupitiriza.] Mulungu walonjeza kuti dziko loipali liloŵedwe m’malo ndi dziko latsopano lokhalidwa ndi anthu abwino amene adzakhala okhoza kukhala ndi moyo mwamtendere. [Ŵerengani Salmo 37:11.] Inu ndi inenso tingasangalale ndi moyo m’dziko latsopano limenelo ngati tikhulupirira Baibulo ndi kugwiritsira ntchito uphungu wake.” Fotokozani programu yathu yothandiza anthu kuphunzira Baibulo.
4 Pamene mupanga ulendo wobwereza mutagaŵira brosha lakuti “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano,” mungayambe mwa kusonyeza chithunzithunzi pachikuto ndiyeno kufunsa funso:
◼ “Kodi muganiza kuti kukhala ndi moyo m’dziko langwiro kudzakhala kotani? [Yembekezerani ndemanga za mwininyumba.] Zimene mukuona m’chithunzithunzichi sizongoyerekezera chabe; nzozikidwa pa malonjezo otsimikizirika onenedwa m’Baibulo. [Ŵerengani Chivumbulutso 21:4 ndi Salmo 37:11, 29.] Ndingakonde kukulongosolerani za mmene inu ndi banja lanu mungalandirire dalitso limeneli.” Ngati mwininyumba asonyeza chikondwerero, pitirizani makambitsiranowo, ndipo mpempheni kuphunzira naye Baibulo.
5 Pamene tipeza anthu oona mtima amene akufunafuna choonadi, timasonyeza chikondi chathu chenicheni mwa kubwerera kukawathandiza kuchitapo kanthu pa zimene amva. Timagwiritsira ntchito choonadi chopatulika choikiziridwa kwa ife kaamba ka dalitso losatha la ife eni ndi la awo otimva.—1 Tim. 4:16.