Thandizani Ena Kuphunzira Choonadi
1 Yesu anadza kudziko lapansi kudzachitira umboni za choonadi. Kuti choonadicho chilalikidwe kwa ena, iye anaphunzitsa ophunzira ake kukhala aphunzitsi. Anali ndi chidaliro chachikulu za chipambano chawo m’kuphunzitsa ena kwakuti anawatcha kuti ‘alangizi apoyera.’ (Mat. 13:52, NW) Iye anayerekeza aliyense wa iwo ndi munthu wophunzira wokhala ndi nkhokwe yeniyeni yotengamo chuma. Ophunzira a Yesu lerolino amagwiritsira ntchito zofalitsa kufulumizira ntchito ya kulalikira Ufumu. Mwachitsanzo, mipingo yambiri ili ndi mabrosha ndi timabuku tosiyanasiyana togwiritsira ntchito kuthandiza ena kukhala ophunzira. Kodi ndimotani mmene ziŵiya zamtengo wapatali zimenezi zingagwiritsiridwire ntchito?
2 Brosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? limalongosola mwatsatatetsatane kuti dziko latsopano lopanda mavuto lili pafupi. Kodi tingalidziwikitse motani? Malingaliro ake angapezeke m’buku la Kukambitsirana pansi pa mutu waung’ono wakuti “Kuvutika,” kuyambira pa tsamba 222, kapena mungakonde mawu oyamba a pa tsamba 11 pansi pa mutu waung’ono wakuti “Chisalungamo/Kuvutika.”
3 Munganene kuti:
◼ “Kodi munayamba mwadabwa kuti, Kodi Mulungu amasamaladi za chisalungamo ndi kuvutika zimene anthu akukumana nazo?” Yembekezerani yankho. Ŵerengani Salmo 72:12-14. Ndiyeno tembenukirani pa tsamba 22 la brosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? ndi kukambitsirana pamitu ya malembo akuda m’Chigawo 10, ndiponso tanthauzo la chithunzithunzi pa tsamba 23. Ngati broshalo likanidwa, bwanji osagaŵira trakiti, monga ngati lakuti Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo kapena Moyo m’Dziko Latsopano la Mtendere?
4 Pogaŵira kabuku kakuti “Pali Zina Zambiri ku Moyo!,” munganene kuti:
◼ “Kwa ambiri mkhalidwe wa moyo wafikira kukhala wosakondweretsa ndi wotopetsa. Kodi muganiza kuti nchiyani chimene chikufunika kupangitsa moyo kukhala watanthauzo? [Lolani mwininyumba kufotokoza lingaliro lake.] Baibulo limasonyeza kuti Mulungu ali ndi zinthu zabwino kwambiri zotiyembekezera. Onani zimene akunena pano pa Chivumbulutso 21:4, 5.” Ngati kuli koyenera, pitirizani makambitsiranowo ndi mfundo za m’ndime 42 za kabukuko.
5 Pogwiritsira ntchito brosha lakuti “Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!,” wofalitsa wachichepere angafunse kuti:
◼ “Kodi mungakonde kukhala ndi moyo mu paradaiso wa padziko lapansi motere? [Sonyezani chikuto cha kumaso ndi kumbuyo, ndipo yembekezerani yankho.] Banja langa ndi ine tikuyembekezera kudzakhala mmenemo chifukwa cha zimene Baibulo limanena pano pa Yohane 17:3.” Ngati chikondwerero chasonyezedwa lembalo litaŵerengedwa, gaŵirani broshalo kuti munthuyo aŵerenge.
6 Ngati mukugwiritsira ntchito timabuku tina kapena mabrosha mu utumiki wanu mwezi uno, mungakonze mawu anu oyamba ndi maulaliki mogwirizana ndi malingaliro amene aperekedwawo. Kumbukirani kukhala achidule ndi kunena ndemanga zabwino ndi zomangirira kuti musonkhezere chikondwerero cha eninyumba.
7 Yehova watipatsa choonadi. Tiyenera kugwiritsira ntchito mipata yoikidwa kwa ife ya kuchigaŵana ndi ena, mumpangidwe wosindikizidwa ndi m’makambitsirano athu omwe ndi anthu amene timakumana nawo. Mwanjira imeneyi timadzisonyezadi kukhala alangizi apoyera kaamba ka phindu losatha la ena.—Mateyu 28:19, 20.