Thandizani Awo Amene Ali Opanda Chikhulupiriro
1 Masiku ano, kuonedwa monga wophunzira ndi wopita patsogolo m’kulingalira kwafala kwambiri. Mafilosofi aumunthu ndi ziphunzitso zokopa zikukwezedwa, pamene nzeru yaumulungu yozikidwa pa Mawu a Mulungu, Baibulo, ikunyalanyazidwa. Anthu oona mtima amene akufuna kudziŵa zenizeni ndi choonadi chomveka adzakonda mwaŵi wa kupenda buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Buku limeneli lingathandize awo amene alibe chikhulupiriro. (Aheb. 11:6) Tsimikizirani kupanga maulendo obwereza kwa onse amene ali ofunitsitsa.
2 Mungayambe kukambitsirana kwanu motere:
◼ “Ndikhulupirira kuti mukudziŵa kuti anthu ena amachirikiza lingaliro lakuti Baibulo linangopangidwa ndi munthu. Sakhulupirira kuti Baibulo lili Mawu a Mulungu. Kodi mukuziona bwanji zimenezo? [Yembekezerani yankho.] Kaya anthu akhale ndi zikhulupiriro zotani, Baibulo limasonyeza lokha kuti lili lodalirika ndi loona. Tatengani pulaneti lathu la dziko lapansi monga chitsanzo. Zaka mazana ambiri anthu anakhulupirira kuti dziko lapansi linali lathyathyathya ndi kuti linali loyedzekeka pa chinthu china; koma tsopano tidziŵa kuti limenelo linali lingaliro lopanda nzeru losemphana ndi zenizeni. Komabe, anthu asanayambitse malingaliro onama amenewo, Baibulo linali litatchula kale kuti dziko lapansi linali ‘lolenjekeka pachabe.’ Ŵerengani ndime 2 patsamba 99, ndiyeno kambitsiranani Yobu 26:7.
3 Kapena mungatsatire njira iyi paulendo wobwereza:
◼ “Si kwachilendo kukumana ndi anthu amene sakhulupirira Mawu a Mulungu, Baibulo. Kodi muganiza kuti nchifukwa ninji anthu ambiri ataya chikhulupiriro mwa Mulungu? [Yembekezerani yankho.] Ambiri amati ataya chikhulupiriro chawo chifukwa cha kuwonjezeka kowopsa kwa chiwawa ndi nsautso padziko. Iwo amalingalira kuti ngati Mulungu wamphamvuyonse aliko, nchifukwa ninji sakuthetsa kuvutika konseku? Awo amene sakhoza kupeza yankho lokhutiritsa la funsolo kaŵirikaŵiri safuna Baibulo. Koma pali umboni wochuluka wakuti Mulungu ndiye mlembi wa Baibulo ndi kuti amafunira anthu zabwino. M’Baibulo, walonjeza kusandutsa dziko lapansi malo achimwemwe ndi mtendere.” Pitirizani kukambitsiranako mwa kugwiritsira ntchito Salmo 37:9-11.
4 Baibulo lanu lili m’manja, mungayambe kukambitsirana mwa kunena kuti:
◼ “Tafikanso kudzakusonyezani chifukwa chake phunziro la Baibulo lili lothandiza masiku ano. Anthu ochuluka ali ndi Baibulo, koma ndi oŵerengeka chabe amene amapeza nthaŵi ya kuliŵerenga. Ena mosabisa amatiuza kuti salidaliranso kwambiri Baibulo. Kodi mukuziona bwanji zimenezo? [Yembekezerani yankho.] Umboni wina wakuti Baibulo lili Mawu ouziridwa a Mulungu ndiwo kukwaniritsidwa kwa maulosi ake.” Sonyezani Malemba m’ndime 3 patsamba 135.
5 Mwina wina angakonde kumvetsera lingaliro lotsatirali:
◼ “Timaona ubwino ndi mphamvu ya Baibulo pamene tilingalira za aja amene adziŵa uphungu wake ndi kuugwiritsira ntchito. Nkhani yabwino yotsatirayi ili chitsanzo choyenera.” Ŵerengani nkhaniyo m’ndime 5 ndi 6 patsamba 177. Fotokozani mmene bukuli limaperekera mayankho okhutiritsa pa mafunso ofunika onena za Baibulo.
6 Tingakhale dalitso kwa ena mwa kugwiritsira ntchito bukuli kuwathandiza kupeza maziko olimba a chikhulupiriro m’Mawu a Mulungu, Baibulo.