Kugaŵira Buku la Knowledge That leads To Everlasting Life
1 Tinakondwera pamene buku latsopano, lakuti Knowledge That Leads to Everlasting Life, linatulutsidwa! Ilo lakonzedwa kuthandiza anthu kupeza mwamsanga chidziŵitso cholongosoka cha choonadi. M’December tidzakhala ndi mpata woyamba wogaŵira bukuli m’gawo lathu. Kodi tidzanenanji kuti tidzutse chidwi?
2 Nawu ulaliki umene ungakope munthu amene chikhulupiriro chake mwa Mulungu chazirala:
◼ “Anthu ambiri anakula ali ndi chikhulupiriro mwa Mulungu, koma tsopano apeza kuti chikhulupiriro chawo sichilinso monga poyamba. Kodi muganiza nchiyani chachititsa zimenezo? [Yembekezani yankho.] Chikhulupiriro chathu mwa Mulungu chimalimba mwa kupenda zozizwitsa za chilengedwe. [Ŵerengani Salmo 19:1.] Mwini malamulo oyendetsa zinthu zakumwamba zimenezi watipatsanso chitsogozo chofunika. [Ŵerengani Salmo 19:7-9.] Mavesi ameneŵa amagogomezera kufunika kwake kwa kuphunzira zimene tingathe ponena za Mulungu ndi zifuno zake. [Sonyezani chithunzithunzi chimene chili patsamba 4 ndi 5, ndipo ŵerengani mawu ake.] Ngati mufuna kupindula ndi chidziŵitso chapadera chimenechi, ndidzakusiyirani bukuli pachopereka cha K800.00.”
3 Mukuganizira za nkhani ya chochitika chaposachedwapa yovutitsa maganizo, munganene kuti:
◼ “Muyenera kuti mwamva za [tchulani chochitikacho]. Kodi munaganizapo zakuti kaya Mulungu amaonadi chisalungamo ndi kuvutika zimene timaona kapena ngakhale zimene zimatichitikira? [Yembekezani yankho.] Baibulo limatitsimikiza kuti Mulungu amatikonda ndi kuti adzatithandiza panthaŵi ya tsoka.” Ŵerengani zigawo za Salmo 72:12-17. Tsegulani bukulo patsamba 70, ndi kufotokoza kuti bukuli, Knowledge That Leads to Everlasting Life, limapereka yankho pafunso limene ambiri afunsa lakuti, Kodi nchifukwa ninji Mulungu amalola kuvutika? “Yankho la Baibulo pafunso limenelo lidzakutonthozani mtima kwambiri. Ndidzakusiyirani bukuli kuti muliŵerenge nokha.”
4 Mutakumana ndi kholo, mungakambitsirane za banja motere:
◼ “Makolo ambiri amavomereza kuti nkovuta kwambiri kuyesa kukhala ndi moyo wa banja wachimwemwe. Malinga ndi kuona kwanu, kodi zopinga zake zazikulu nzotani? [Yembekezani yankho.] Ambirife timayesetsa ndithu, ndipo nthaŵi zambiri timayamikira thandizo limene lingatipezetse zotulukapo zabwino. Baibulo limapereka uphungu wabwino koposa. [Ŵerengani zigawo za Akolose 3:12, 18-21.] Baibulo limanena zambiri pankhaniyi, monga zimene mutu 15 wa bukuli wakuti ‘Kumanga Banja Lolemekeza Mulungu’ ukufotokoza. Ukulongosola uphungu woperekedwa m’Baibulo wosonyeza mmene tingathetsere mavuto muukwati ndi mmene tingachitire ndi mavuto a ana athu. Ndikhulupirira kuti mudzakonda kuliŵerenga.”
5 Ngati mukufuna zachidule, mungayese zotsatirazi:
◼ “Kodi munaganizapo za chifukwa chake timakalamba ndi kufa? Mutu 6 m’bukuli ukufotokoza chochititsa imfa ndi mmene Mulungu adzachichotsera. Baibulo limatiuza kuti Mulungu walonjeza moyo wosatha kwa amene amamkonda. [Ŵerengani Yohane 17:3.] Ngati mungakonde kuŵerenga za zimenezi, bukuli lidzakupatsani chidziŵitso chochuluka.”
6 Ngati takonzekera bwino, tingakhoze kugwiritsira ntchito bukuli ‘kutsegulira Malembo’ kwa ena mwa njira imene idzawasangalatsa kwambiri!—Luka 24:32.