Bwererani kwa Aja Amene Anasonyeza Chidwi
1 Potulutsa buku latsopano lakuti, Knowledge That Leads to Everlasting Life, mlankhuli pamsonkhano wachigawo anafotokoza kuti “ophunzira oona mtima ayenera kukhala okhoza kupeza chidziŵitso chokwanira mwa kuliphunzira kuti atenge kaimidwe kumbali ya Yehova ndi kubatizidwa.” Bukulo lakonzedwera kuphunzitsa choonadi mofulumira. Mwachidule limapereka chidziŵitso cholunjika chimene chingasonkhezere ophunzira kupita patsogolo. Limasonyeza choonadi mwa njira yabwino popanda kutaya nthaŵi pa ziphunzitso zonyenga. Kuti tipambane pa kugwiritsira ntchito chiŵiya chatsopanochi, tiyenera kupanga maulendo obwereza kwa aja amene anasonyeza chidwi.
2 Ngati munalankhula ndi munthu amene analibe chikhulupiriro mwa Mulungu komano anasonyeza chidwi, mungayambe mwa kutsegula bukulo pa chithunzithunzi chimene chili patsamba 4 ndi 5 ndi kunena kuti:
◼ “Pamene ndinali pano tsiku lija, tinayang’ana pa chithunzithunzi ichi cha malo okongola. Mawu ake akufunsa kuti, ‘Kodi muyenera kuchitanji kuti muwapeze?’ Kodi mungayankhe motani? [Yembekezani yankho.] Baibulo limasonyeza bwino lomwe chofunika chimodzi chachikulu. [Ŵerengani Yohane 17:3.] Chidziŵitso nchofunika kwambiri pa chikhulupiriro chathu mwa Mulungu. Njira yabwino koposa imene tingaphunzirire zimene tiyenera kudziŵa ndi yakuphunzira Baibulo mwa dongosolo.” Pitani pamutu 1 ndi kusonyeza mfundo zina zolimbikitsa m’ndime 1 mpaka 5. Fotokozani mmene phunziro la Baibulo limachitikira, ndipo muuzeni kuti mudzabweranso kudzakambitsirana zowonjezereka.
3 Ngati mwabwererako kukapitiriza makambitsirano anu ponena za chifukwa chake Mulungu amalola kuvutika, munganene kuti:
◼ “Nthaŵi ija ndinali pano, tinakambitsirana za [chochitika chakutichakuti]. Panabuka funso lakuti nchifukwa ninji Mulungu amalola kuvutika kwambiri motere m’dziko. Kodi munagamulapo chiyani? [Yembekezani yankho.] Kuli kolimbikitsa kudziŵa kuti Mulungu sindiye amachititsa mikhalidwe yoipa imeneyo.” Tsegulani patsamba 71-2 m’buku lakuti Knowledge That Leads to Everlasting Life, ndipo kambitsiranani mfundo zina za Malemba zofotokozedwa m’ndime 3 mpaka 5. Muuzeni kuti mudzabweranso kudzafotokoza chifukwa chake tingakhale otsimikiza kuti kuvutika kumene Mulungu walola kudzatha posachedwapa.
4 Ngati mukubwerera kwa kholo limene likudera nkhaŵa za mavuto a banja, munganene zotsatirazi:
◼ “Ndikudziŵa kuti inuyo, monga kholo, mumafuna kuti ana anu akule bwino kwambiri. Popeza kuli kosatheka kuwatetezera pa chilichonse chimene chili choipa, muyenera kuwaphunzitsa mmene angachitire ndi mavuto a moyo. Kodi muganiza mungachite motani zimenezo? [Yembekezani yankho.] Chimodzi cha zinthu zofunika koposa chimene kholo lingapereke ndicho chiphunzitso.” Tsegulani patsamba 145-6 m’buku la Knowledge, ndipo sonyezani uphungu wa Baibulo wogwira ntchito, kugogomezera kufunika kwake ndi mmene kuutsatira kungakhalire dalitso. Liuzeni kuti mudzabweranso kudzasonyeza mmene bukuli lingagwiritsidwire ntchito kuphunzira zambiri ponena za kupeza moyo wa banja wachimwemwe.
5 Ngati mukubwerera kumene munagwiritsira ntchito ulaliki wachidule, mukhoza kunena kuti:
◼ “Sikunali kufuna kwa Mulungu kuti tizikalamba ndi kufa. Iye anafuna kuti tikhale ndi moyo kosatha padziko lapansi laparadaiso.” Sonyezani chithunzithunzi chimene chili patsamba 188-9. Ŵerengani ndime 11 patsamba 184. Pangani makonzedwe a ulendo wina wobwereza.
6 Ndithudi, buku latsopano limeneli lili chogaŵira china chochokera kwa Yehova ‘chofulumiza’ ntchito yakututa m’masiku ano otsiriza. (Yes. 60:22) Tikaligwiritsira ntchito mwaluso, tingapereke chidziŵitso chimene chingathandize wina kupeza moyo wosatha.