Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/96 tsamba 7
  • Makambitsirano Aubwenzi Angafike Pamtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makambitsirano Aubwenzi Angafike Pamtima
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Makambirano Olimbikitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Mmene Tingayambire Ulaliki Wamwamwayi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Mmene Mungakulitsire Luso la Kucheza ndi Anthu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Mmene Mungayambire Kucheza ndi Anthu Kuti Muwalalikire Mwamwayi
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 6/96 tsamba 7

Makambitsirano Aubwenzi Angafike Pamtima

1 Kukambitsirana kunganenedwe kuti ndiko “kupatsana maganizo kwapakamwa.” Kuyambitsa makambitsirano aubwenzi pankhani yokhudza anthu ena kungakope chidwi chawo ndipo kungatithandize kuwafika pamtima ndi uthenga wa Ufumu. Zokumana nazo zasonyeza kuti kuli kogwira mtima kwambiri kuloŵetsa anthu m’kukambitsirana komasuka ndi kwaubwenzi kuposa kungowalalikira.

2 Mmene Mungayambire Kukambitsirana Kwaubwenzi: Kukhala kwathu okhoza kukambitsirana ndi ena sikutanthauza kuti tiyenera kupereka malingaliro ndi malemba ena olinganizidwa mochititsa chidwi kwambiri. Kumangofuna kuloŵetsa winayo m’kukambitsirana nafe. Mwachitsanzo, pamene tikambitsirana mwaubwenzi ndi mnansi wathu woyandikana naye makomo, timakhala omasuka. Sitimaganiza za mawu otsatira koma timangoyankha mwachibadwa zimene akunena. Kusonyeza chikondwerero chenicheni pa zimene akunena kungamlimbikitse kupitiriza kukambitsirana nafe. Ziyenera kukhalanso choncho pochitira umboni kwa ena.

3 Nkhani zonga upandu, mavuto a achichepere, nkhani zakumaloko, mikhalidwe yapadziko, kapena ngakhale mkhalidwe wa mphepo zingagwiritsiridwe ntchito kuyambitsa makambitsirano aubwenzi. Nkhani zimene zimakhudza mwachindunji miyoyo ya anthu nzogwira mtima kwambiri podzutsa chikondwerero chawo. Pamene kukambitsirana kuyambika, tikhoza bwino lomwe kukuloŵetsa mu uthenga wa Ufumu.

4 Kukhala ndi kukambitsirana komasuka sikumatanthauza kuti kukonzekera pasadakhale nkosafunika. Iko nkofunika. Komabe, sitifunikira kupanga autilaini yatsatanetsatane kapena kuloŵeza ulaliki, zimene zingachititse kukambitsirana kukhala kosamasuka kapena kosasinthira ku mikhalidwe imene ilipo. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 9:20-23.) Njira yabwino koposa yokonzekerera ndiyo kusankha mutu wa Lemba umodzi kapena iŵiri, ndi cholinga cha kuzikapo makambitsirano. Kupenda nkhani zopezeka m’buku la Kukambitsirana kudzakhala kothandiza pazimenezi.

5 Mikhalidwe Yofunika ya Kukambitsirana Kwaubwenzi: Pamene tikambitsirana ndi ena, tiyenera kukhala aubwenzi ndi oona mtima. Kumwetulira ndi maonekedwe achisangalalo zingathandize kusonyeza mikhalidwe imeneyi. Tili ndi uthenga wabwino koposa m’dziko; ndi wokopa kwambiri kwa anthu oona mtima. Ngati aona kuti chikondwerero chathu pa iwo chikusonkhezeredwa ndi chikhumbo choona mtima cha kugaŵana nawo uthenga wabwino, pamenepo angasonkhezereke kumvetsera.—2 Akor. 2:17.

6 Kukambitsirana ndi ena kuyenera kukhala chinthu chosangalatsa. Chotero, tiyenera kukhala okoma mtima ndi osamala popereka uthenga wa Ufumu. (Agal. 5:22; Akol. 4:6) Yesani kusiya munthu winayo ali ndi chithunzi chabwino. Mwa njira imeneyi, ngakhale ngati tilephereka kumfika pamtima panthaŵi yoyamba, iye angakhale womvetsera kwambiri nthaŵi ina pamene Mboni ina ikambitsirana naye.

7 Kuyambitsa kukambitsirana kwaubwenzi sikumalira kuloŵeza ulaliki wocholoŵana. Kumangofuna kudzutsa chidwi pankhani yokhudza munthu. Titakonzekera pasadakhale, tidzakhala okonzeka kukambitsirana ndi anthu mwaubwenzi. Tiyeni tiyeseyese kufika pamtima anthu amene timakumana nawo mwa kuwagaŵira uthenga wabwino koposa umene ulipo, wa madalitso osatha a Ufumu.—2 Pet. 3:13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena