Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Apanyumba Opita Patsogolo
1 Nesi wa ku Tanzania, wachichepere wa ku Argentina, ndi mayi wina wa ku Latvia, kodi onseŵa anachitanji? Yearbook ya 1997 (mas. 8, 46, ndi 56) ikuti atatu onsewo anapita patsogolo mwamsanga paphunziro lawo la Baibulo lapanyumba chifukwa chofunitsitsa kuphunzira kangapo mlungu uliwonse m’buku la Chidziŵitso. Ofalitsa alimbikitsidwa kuti ngati kuli kotheka, ayesetse kumaliza mutu wonse wa bukulo paphunziro lililonse. Komabe, ena zimawavuta. Ngakhale kuti zambiri zimadalira pa mikhalidwe ndi luntha la wophunzira aliyense, aphunzitsi aluso apambana mwa kugwiritsira ntchito malingaliro otsatiraŵa.
2 Monga momwe inalongosolera mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996, mufunika kumphunzitsa wophunzira wanu kukonzekera phunzirolo. Kuchiyambi kwenikweni, zingakhale bwino kufotokoza ndi kumsonyeza mmene angachitire zimenezo. Asonyezeni kope lanulanu la buku la Chidziŵitso. Konzekerani phunziro loyamba pamodzi. Athandizeni ophunzirawo kupeza mawu kapena mfundo zazikulu zimene zikuyankha mwachindunji funso losindikiza ndiye kenako zichongeni. Ofalitsa ena angowapatsa ophunzira awo pensulo yochongera. Alimbikitseni kuyang’ana malemba onse pamene akukonzekera phunzirolo. Pomatero, mukhala mukuwaphunzitsanso kukonzekera Phunziro la Buku la Mpingo ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda.—Luka 6:40.
3 Mphunzitsi wabwino amamlankhulitsa wophunzirayo osati kulankhula zochuluka iyeyo. Samalola mfundo zazing’ono kumpatutsa. Kaŵirikaŵiri samawonjezera mfundo zina zapambali. M’malo mwake, amagogomezera mfundo zazikulu za phunzirolo. Enanso apatsa ophunzira mabuku ena kuti awathandize kupeza mayankho a mafunso. Ndiponso, okondwerera angalandire chidziŵitso china chochuluka mwa kupezeka pamisonkhano yampingo.
4 Nthaŵi zina sikufunika kuyang’ana malemba onse osagwidwa mawu m’phunzirolo. Mfundo zina zazikulu mungazilongosole mwa malemba ogwidwa mawu m’ndimemo. Pobwereza, gogomezerani malemba ofunika amene mwakambitsirana ndipo limbikitsani wophunzirayo kuwakumbukira.
5 Kodi Phunzirolo Likhale la Utali Wotani?: Phunzirolo silitofunikira kukhala la ola limodzi basi. Eni nyumba ena amakhala ndi nthaŵi yochuluka ndipo amakonda kuphunzira nthaŵi yaitali. Kapena wophunzirayo angafune kuphunzira kangapo pamlungu. Zimenezo zingawapindulitse amene angathe kutero.
6 Monga momwe Yesaya 60:8 amasonyezera, lero atamandi atsopano a Yehova zikwi mazana ambiri ‘akuuluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda ku mazenera awo’ m’mipingo ya anthu ake. Tonsefe tiyeni tichite mbali yathu pogwira ntchito mogwirizana kwambiri ndi Yehova pamene akufulumiza kusonkhanitsa anthu onga nkhosa.—Yes. 60:22.