Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/98 tsamba 4
  • Sangalalani ndi Kupereka Umboni Womveka Bwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sangalalani ndi Kupereka Umboni Womveka Bwino
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Lalikirani Mwaluntha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Zitsanzo za Maulaliki a Utumiki wa Kumunda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Kugwiritsira Ntchito Bwino Mabuku Athu Akale
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Chidziŵitso Chochokera kwa Mulungu Chimayankha Mafunso Ambiri
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 1/98 tsamba 4

Sangalalani ndi Kupereka Umboni Womveka Bwino

1 Tonsefe timakonda kuchita zinthu zimene timachita bwino. Marko 7:37 amafotokoza kuti makamu a anthu ponena za Yesu anati: “Wachita Iye zonse bwino.” Nchifukwa chake Yesu ankakondwera pochita chifuniro cha Yehova! (Yerekezerani ndi Salmo 40:8.) Mwa kupenda zitsanzo zotsatirazi, ifenso tingapeze chimwemwe pomvera lamulo la Yesu lakuti “tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni.” (Mac. 10:42) Mu January muno tikugaŵira buku lililonse lamasamba 192 lomwe linafalitsidwa 1985 isanafike limene mpingo ungakhale nalo m’sitoko, kapena brosha la “Tawonani!” Kodi mabuku ameneŵa tingawagaŵire bwanji kuti tichitire umboni womveka bwino?

2 Popeza kuti nthaŵi zambiri anthu amadera nkhaŵa ndi nkhani ya thanzi, munganene izi:

◼ “Ngakhale kuti pakhala kupita patsogolo kwambiri m’zamankhwala, tikuona kuti anthu akuvutikabe kwambiri ndi matenda. Kodi inuyo mukuganiza kuti chifukwa chake nchiyani? [Yembekezerani yankho.] Yesu Kristu anati miliri idzakhala chizindikiro cha masiku otsiriza. (Luka 21:11) Komanso Baibulo limafotokoza kuti nthaŵi ina matenda sadzakhalakonso. [Ŵerengani Yesaya 33:24.] Taonanitu mmene bukuli likutisonkhezerera kukhulupirira chiphunzitso cha Baibulo chimenecho.” Sonyezani mawu ena oyenera a m’buku muli nalolo, ndiyeno ligaŵireni.

3 Ngati mukuchitira umboni wamwamwaŵi chapafupi ndi masitolo, mungapereke moni ndiyeno nkufunsa kuti:

◼ “Kodi inunso mukuona kuti masiku ano zinthu zikukwera mtengo kwambiri moti nkovuta kupeza ndalama zokwanira? [Yembekezerani yankho.] Nanga kodi mukuganiza kuti idzafika nthaŵi pamene mavuto a zachuma adzatheratu?” Yembekezerani Yankho. Kenako msonyezeni Lemba loyenera logwidwa mawu m’buku limene mukugaŵiralo. Pitirizani mwa kunena kuti: “Buku lino likusonyeza mmene Mulungu, mwa Ufumu wake, adzathetsera mavuto amene akupangitsa moyo kukhala wovuta kwambiri lerolino.” Ndiyeno gaŵirani bukulo. Mungamuuze mmene mwakondwera ndi kukambitsiranako, ndiyeno nkumfunsa kuti: “Kodi nkotheka kuti tsiku lina tidzapitirize kukambitsirana nkhani imeneyi?” Mwanjirayi, mungathe kupempha nambala yafoni ya munthuyo kapena keyala yake.

4 Mwina mungapeze mpata woyesa ulaliki uwu wonena za mavuto a dziko, pogwiritsira ntchito brosha la “Tawonani!”

◼ “Kodi inuyo mukuganiza kuti chikuchititsa mavuto a dziko nchiyani? [Yembekezerani yankho, ndiyeno ŵerengani ndime 28 patsamba 15.] Ndiponso chonde onani zimene Baibulo limanena m’buku la Chivumbulutso. [Ŵerengani Chivumbulutso 12:9, chomwe chatchulidwa m’ndime 29.] Chifukwa chimene dziko likusoŵera mtendere nchakuti Mdyerekezi anaponyedwa pansi kudziko lino. Broshali likuyankha mafunso ambiri ofunika, ndipo ndingakondwe kukupatsani ngati mudzaliŵerenga.”

5 Pobwerera kukaona amene anaonetsa chidwi, mungayambe phunziro la Baibulo mwa kugwiritsira ntchito njira iyi:

◼ “Pamene tinacheza poyamba paja, munanena mawu ena amene anandikondweretsa kwambiri. [Tchulani mfundo ina imene munthuyo ananena.] Ndakhala ndikuganiza za mfundo imeneyo, ndipo ndingakonde kukulongosolerani zomwe ndinapeza poifufuza nkhaniyo. [Ŵerengerani pamodzi lemba lina loyenera.] Timachititsa phunziro laulere. Maphunziro ameneŵa athandiza anthu mamiliyoni ambiri kudziŵa ziphunzitso zazikulu za Baibulo panthaŵi yochepa chabe. Kuphunzira kumeneku kungalimbikitse chidaliro chanu chakuti Mulungu adzakwaniritsadi malonjezo ake.” Sonyezani mafunso ena amene adzayankhidwa. Ngati munthuyo wakana phunziro la Baibulo, mfotokozereni kuti tilinso ndi phunziro lina lapadera la mphindi 15 basi mlungu uliwonse kwa milungu 16. Msonyezeni brosha lakuti Mulungu Amafunanji, pitani paphunziro 1, ndi kumfunsa ngati mungamsonyeze mmene timaphunzirira.

6 Kumbukirani Kugwiritsira Ntchito Matrakiti: Mungawagwiritsire ntchito mogwira mtima pamawu anu oyamba kuti mudzutse chidwi cha munthu pa zinthu zaumzimu, kapena mungawasiye ngati anthu akana mabuku.

7 Khalani waluso pantchito yanu, ndipo idzakusangalatsani. Nthaŵi zonse muziganiza za kuchitira umboni womveka bwino, ndipo sangalalani ndi kuchita bwino mbali zonse za utumiki.—1 Tim. 4:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena