Mmene Banja Limachitira Zinthu Pamodzi Kuti Onse Azitengamo Mbali Mokwanira—Pa Misonkhano ya Mpingo
1 Mabanja achikristu ayenera kumvera lamulo losonkhana pamodzi pamisonkhano ya mpingo. (Aheb. 10:24, 25) Mogwirizana, onse akhoza kuikonzekera, kupezekapo, ndi kutengamo mbali m’misonkhano. Mikhalidwe ya banja imasiyanasiyana, koma pali zinthu zimene mwamuna wachikristu, mkazi wokhulupirira, kapena kholo losakwatira angachite pochirikiza mgwirizano wa banja pankhani zauzimu, mosasamala kanthu za chiŵerengero cha ana m’banjamo ndi zaka zawo.—Miy. 1:8.
2 Khalani ndi Nthaŵi Yokonzekera: Am’banjamo ayenera kuchitira zinthu pamodzi kuti aliyense athe kukonzekera bwino misonkhano ya mpingo. Ambiri amakonzekera pamodzi nkhani ya Phunziro la Nsanja ya Olonda ya mlungu uliwonse. Ena amakonzekera Phunziro la Buku la Mpingo kapenanso kuŵerenga Baibulo malinga ndi ndandanda ya mlungu umenewo monga banja. Cholinga chawo chimakhala kuti adziŵiretu mfundo zazikulu asanapite kumisonkhano. Mwanjira imeneyi, onse amapindula kwambiri ndi zimene ali kumva ndipo amakhala okonzeka kutengamo mbali ngati pali mwayi woti atero.—1 Tim. 4:15.
3 Konzekerani Kutengamo Mbali: Aliyense m’banja ayenera kukhala ndi cholinga cholengeza chiyembekezo chake kwa ena mwa kuyankha pamisonkhano. (Aheb. 10:23) Kodi wina m’banjamo akufunikira thandizo kapena chilimbikitso kuti achite zimenezi? Nanga kodi ndi thandizo lotani limene aliyense akufunikira pokonzekera nkhani za m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase? Akazi amayamikira pamene amuna awo aonetsa chidwi kapenanso kuwathandiza kupeza fanizo loyenera ngakhale chochitika chimene angagwiritse ntchito pokamba nkhani. Makolo sayenera kuganiza kuti iwo ndiwo ayenera kuwakonzera ana awo ang’ono nkhani. Kuchita zimenezi zingapatse mwanayo ulesi wosafuna kuphunzira. Koma makolo angawathandize ana ang’ono ndi kuwamvetsera pamene akuyeserera mokweza.—Aef. 6:4.
4 Linganizani Zokapezekapo: Ana angaphunzitsidwe kuyambira ali aang’ono kukonzeka mwamsanga ndi kukhaliratu okonzeka kupita kumisonkhano panthaŵi yake. Am’banja ayenera kuthandizana posamalira ntchito zapanyumba kuti pasakhale kuchedwa.—Onaninso malingaliro ena m’buku la Chimwemwe cha Banja, masamba 112, ndi Achichepere Akufunsa, masamba 316-17.
5 Onse makolo ndi ana ayenera kulingalira mawu a Yoswa wa m’nthaŵi zakale, amene anati: “Koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.” Choncho tsimikizani kuchitira zinthu pamodzi kuti nonse muzitengamo mbali mokwanira m’misonkhano ya mpingo.—Yos. 24:15.