Konzekerani Misonkhano ya Mpingo ndi Kusangalala Nayo
1 Monga gulu la abale, ife mwanzeru timasonkhana nthaŵi zonse kaamba ka misonkhano yathu ya mlungu ndi mlungu. (1 Tim. 4:15, 16) Kodi tingasangalale nayo motani ndiponso kupindula nayo kwambiri?
2 Tiyenera kupatula nthaŵi masiku onse ya kukonzekera misonkhano. Ena angakhoze kutaya nthaŵi yochuluka pa kukonzekera kuposa ena. Komabe, kaya tikhale otanganitsidwa motani, kuli kwanzeru kupeza nthaŵi yokonzekera misonkhano. Kukonzekera pamodzi monga banja nkopindulitsa kwambiri.—Aef. 5:15, 16.
3 Kukonzekera Sukulu Yautumiki Wateokratiki: Yesayesani kutsatira ndandanda ya mlungu ndi mlungu ya kuŵerenga Baibulo. (Yos. 1:8) Pendani nkhani zimene zidzakambidwa, ndipo nyamulani mabuku ofunikira kuti muzitsatira alankhuli. Sinkhasinkhani za mmene mungagwiritsirire ntchito chidziŵitso chimenecho mu utumiki wanu.
4 Kukonzekera Msonkhano Wautumiki: Onani programu yake mu Utumiki Wathu Waufumu. Ŵerengani nkhani zimene zidzakambidwa. Ngati nkhani yotengedwa mu Nsanja ya Olonda kapena m’buku lina ndiyo idzakambidwa, ifuneni ndi kuiŵerenga nayonso. Ngati kudzakhala zitsanzo za maulaliki a utumiki wakumunda, zipendeni pasadakhale kotero kuti mukhale wokonzeka kuzigwiritsira ntchito mu utumiki wanu.
5 Kukonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda: Ŵerengani phunzirolo pasadakhale, mukumachonga mayankho. Kuŵerenga malemba osagwidwa mawu kudzakuthandizani kulimvetsetsa. Kusinkhasinkha mmene phunzirolo likugwirizanirana ndi zimene mukudziŵa kale kudzazamitsa chidziŵitso chanu. Konzekerani kukayankhapo pa phunziro mwa kukonza mayankho achidule pandime imodzi kapena ziŵiri. Imeneyi ndi njira yofunika kwambiri ‘yovomerezera chiyembekezo chathu.’—Aheb. 10:23.
6 Kukonzekera Phunziro la Buku la Mpingo: Choyamba, pendani nkhaniyo; yang’anani mutu wake ndi timitu. Ndiyeno, poŵerenga, pezani mfundo zazikulu. Pendani mavesi a Baibulo ochirikiza mfundozo. Yesani kuyankha mafunso m’mawu anuanu. Mukatsiriza kukonzekera phunzirolo, bwereranimo mwa kusinkhasinkha. Yesani kukumbukira mfundo zazikulu ndi zigomeko zake.—2 Tim. 2:15.
7 Sangalalani Nayo Misonkhano: Kuti musangalale nayo kwambiri misonkhano, mufunikira kusunga nthaŵi kotero kuti muzipezekapo pa pemphero lotsegulira, lopempha mzimu wa Yehova. Ndiponso mumapindula ndi nyimbo za Ufumu zotsitsimula. Ngati mulibe ana kapena chifukwa china chokhalira kumbuyo kwa holo, mwachionekere mudzapeza kuti ngati mukhala kutsogolo, simudzachenjenekedwa kwambiri ndipo mudzapindula nayo kwambiri programuyo. Makolo okhala ndi ana amene angafunikire kutengeredwa kunja msonkhano uli mkati angachepetse kuchenjenetsa ena mwa kukhala pafupi ndi njira ndipo kumbuyo.
8 Yesayesani kupeza Malemba oŵerengedwa. Zimenezi zidzakuthandizani kukumbukira zimene mukumva. Kukambitsirana ndi banja lanu ndi mabwenzi zimene mwaphunzira kudzakhomereza chidziŵitsocho m’maganizo mwanu. Kugwiritsira ntchito malingaliro ameneŵa kudzachititsa misonkhano kukhala yaphindu ndi yosangalatsa, ndipo ‘idzatifulumizadi ku chikondano ndi ntchito zabwino.’—Aheb. 10:24, 25.