Kodi Ndinu Munthu Wamanyazi?
1 Si zachilendo kuona mwana wamng’ono akutisuzumira ali kuseri kwa amayi kapena abambo ake. Kwa ana aang’ono n’kwachibadwa kuchita manyazi. Ngakhale kuuchikulire, ambiri mwachibadwa ndi amanyazi. Ngati manyazi akulepheretsani kuchita nawo utumiki, kodi mungachite chiyani?
2 Kugonjetsa Manyazi: Ndi bwino kusamalira “munthu wobisika wamtima.” (1 Pet. 3:4) Limbitsani kukonda kwanu Yehova ndi anansi anu. Khulupirirani ndi mtima wonse kuti kukwaniritsa ntchito yolalikira ndi imodzi mwa njira zabwino kwambiri yosonyezera chikondi chodzimana. Khalani ndi chizoloŵezi chabwino chochita phunziro laumwini ndi kupezeka pamisonkhano. Pempherani nthaŵi zonse makamaka kuti Yehova akuthandizeni. Kum’khulupirira kwambiri kudzalimbitsa chidaliro chanu ndipo ‘kudzakulimbitsani mtima koposa kulankhula mawu a Mulungu mopanda mantha.’—Afil. 1:14.
3 Kulimbana ndi malingaliro odziona kukhala wosanunkha kanthu. Zikuoneka kuti Timoteo analinso ndi vuto lomweli. Paulo anam’limbikitsa Timoteo kuti “munthu asapeputse ubwana [wake],” ndipo anam’kumbutsa kuti “Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu.” (1 Tim. 4:12; 2 Tim. 1:7) Yehova anam’gwiritsira ntchito Timoteo kwambiri, adzakugwiritsiraninso ntchito ngati muyesetsa kupita patsogolo mom’dalira kwambiri.—Sal. 56:11.
4 Kulingalira mawu a m’Baibulo, monga opezeka pa Mateyu 10:37, kunathandiza mlongo amene anali wamantha kwakuti ankaopa mwamuna wake amene anali wotsutsa. Chifukwa cha khama, utumiki sunalinso wom’vuta, ndipo kenako mwamuna wake, mayi ake, ndi abale ake onse anaphunzira choonadi.
5 N’kofunika Kukonzekera: Kulimba mtima kwanu kudzawonjezereka ngati mukonzekera utumiki wanu mokwanira. Sankhani chitsanzo cha ulaliki wosavuta m’buku la Kukambitsirana kapena m’makope a m’mbuyomo a Utumiki Wathu wa Ufumu, uphunzireni bwinobwino, ndipo uyeserereni. M’malo mochita mantha ndi zopanda pake, lingalirani zinthu zabwino. Yendani ndi ena kuti mulimbe mtima. Kumbukirani kuti anthu ambiri amene mukawapeza m’makomo ndi amantha ngati inu nomwe. Aliyense akufunikira uthenga wa Ufumu.
6 Ngati ndinu wamanyazi, osataya mtima. Mukadzipereka, Yehova adzakuthandizani kuti mukhale mlaliki wauthenga wabwino wogwira mtima. Ndipo mudzapeza chimwemwe mu utumiki wanu.—Miy. 10:22.