Mmene Kudziwa Choonadi Kungakuthandizireni
Mulungu, amene nthawi zonse amanena zoona, akukupatsani mwayi woti mukhale ndi chiyembekezo cha “moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
KODI MUYENERA KUCHITA CHIYANI?
Phunzirani zimene Mawu a Mulungu omwe ndi choonadi amanena.—Yohane 17:3, 17.
Sankhani kumvera Mulungu.—Deuteronomo 30:19, 20.
Muzitsatira malangizo a Mulungu, omwe ndi othandiza.—Yakobo 1:25.
A Mboni za Yehova padziko lonse lapansi akupindula chifukwa chophunzira choonadi cha m’Baibulo. Iwo ndi okonzeka kukuuzani zimene amaphunzirazo.
Kuti mudziwe zambiri, onani kabuku kakuti, Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Kabukuka ndi kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova ndipo kakupezekanso pa www.jw.org/ny.