Kodi Mukukonzekera Kudzachita Chiyani M’tsogolo?
1 Tonse timaganizira zimene tidzachite m’tsogolo. Amene ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi akudikirira kudzakhala kosatha m’dziko latsopano lolungama la Mulungu. Koma pali zinthu zimene zingachotse chiyembekezo chimenechi m’mitima mwathu. Tikufunika kumenyera nkhondo kuti moyo wathu ukhalebe pa zinthu za Ufumu komanso kuti tisadodometsedwe ndi zilakolako zokopa za thupi.—1 Yoh. 2:15-17.
2 Dzikoli silingamvetse n’komwe zolinga za anthu okonda zinthu zauzimu. (1 Akor. 2:14) Pamene ena akumenyera nkhondo kukhala otchuka, amphamvu kapena achuma, timamenyera nkhondo kupeza chuma chauzimu. (Mat. 6:19-21) Kodi tikakhala ndi maganizo a dzikoli pankhani ya tsogolo lathu, tingakwanitse zolinga zathu zauzimu? Posakhalitsa zinthu za dziko zingatenge malo m’mitima yathu. Kodi tingapeŵe bwanji zimenezi?
3 ‘Valani Ambuye Yesu Kristu’: Njira imodzi yoonera ngati zolinga zathu zili pa zinthu za Ufumu ndiyo kuona zokamba zathu. Kodi nthaŵi zonse timakamba za zinthu zakuthupi ndi zadziko? Ngati ndi choncho, tiyenera kuona ngati mtima wathu ukuchoka pa zinthu zauzimu. Tifunika kuyesetsa kwambiri ‘kuvala Ambuye Yesu Kristu osati kuganizira kuchita zofuna zake za thupi.’—Aroma 13:14.
4 Achinyamata ‘angavale Kristu’ mwa kukonzekera tsiku limene adzayambe utumiki wa nthaŵi zonse. Mnyamata amene ankafuna upainiya wokhazikika anakulira kumene chikhalidwe chinali chakuti anyamata azikhala olemera. Choncho, anatanganidwa kwambiri ndi malonda moti kumisonkhano ndi utumiki amangopita mwamwambo chabe. Atangoyamba kukhulupirira mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 6:33 anasiya ntchito yakalavula gaga imene amagwira, n’kuyamba ntchito ya utumiki wa nthaŵi zonse. Tsopano akutumikira Yehova ndi chikumbumtima chabwino, ndipo mwiniwake akuti ‘ndi mphamvu zake zonse.’
5 Baibulo limati ndi bwino kukonzekera tsogolo lathu. (Miy. 21:5) Chifuniro cha Mulungu chikhaletu choyamba pamene tikuchita zimenezo.—Aef. 5:15-17.