Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/01 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira April 9
  • Mlungu Woyambira April 16
  • Mlungu Woyambira April 23
  • Mlungu Woyambira April 30
  • Mlungu Woyambira May 7
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 4/01 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira April 9

Nyimbo Na. 93

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Lengezani chiŵerengero cha anthu amene anapezeka pa Chikumbutso pampingowo. Pemphani omvetsera kusimba zimene anthu opezeka pa mwambowu kwanthaŵi yawo yoyamba ananena.

Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Phatikizanipo mfundo zimene amazilingalira posankha nyumba zochitiramo phunziro la buku.—Onani Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 1983.

Mph. 20: “‘Tanganidwani Kwambiri’ ndi Utumiki Wanu.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Monga ndime 3-5 zafotokozera, pemphani ofalitsa aŵiri kapena atatu asimbe zimene anakumana nazo pothandiza ena.

Nyimbo Na. 80 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 16

Nyimbo Na. 145

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kwatsala mapeto a mlungu aŵiri okha kuti April athe, chotero limbikitsani aliyense kulalikira mweziwu usanathe.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: “Ulaliki Wosavuta Umagwira Mtima.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo malingaliro a mu nkhani yakuti, “Tiyeni ‘Tinene Mfundo Yathu Mwachidule!’” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa July 1999, tsamba 4. Onetsani mwachidule chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri za ulaliki wosavuta.

Nyimbo Na. 146 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 23

Nyimbo Na. 163

Mph. 5: Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: “Kodi Mukukonzekera Kudzachita Chiyani M’tsogolo?” Nkhani. Phatikizanipo mfundo zoyenera za mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2000, masamba 18-21.

Mph. 25: “Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira.” Woyang’anira wotsogolera akambe nkhaniyi. Ŵerengani kalatayi. Limbikitsani onse kuti chaka chino atsimikize kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.

Nyimbo Na. 202 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 30

Nyimbo Na. 215

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a muutumiki wakumunda a April. Ochititsa Phunziro la Buku ayenera kuonetsetsa kuti aliyense m’gulu lawo wapereka malipoti kuti onse akhale atasonkhanitsidwa pofika pa May 6.

Mph. 15: “Chitirani Umboni mwa Kukhala Mnansi Wabwino.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Tchulani njira zina zimene khalidwe lathu lingachitire umboni.—Onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 1997, tsamba 18, ndime 16.

Mph. 20: Apainiya Akuthandiza Ena. Nkhani komanso kufunsa yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Pendani pulogalamu ya Apainiya Athandiza Ena mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 1998, patsamba 4. Simbani zinthu zolimbikitsa zimene zachitika pampingopo. Funsani mpainiya amene wathandiza munthu wina ndiponso wofalitsa amene wathandizidwa. Sonyezani momwe onseŵa apindulira mwa kuyenda limodzi mu utumiki. Pemphani ena kupindula ndi makonzedwe ameneŵa m’miyezi ikudzayi.

Nyimbo Na. 216 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 7

Nyimbo Na. 84

Mph. 10: Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: “Zinthu Zonse Zitheka ndi Mulungu.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

Mph. 20: Kodi Banja Lathu Lingasonyeze Motani Khalidwe Loyera? Mkulu akambirane ndi banja lake nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1996, masamba 17-20. Pendani njira zomwe tingasonyezere khalidwe loyera panyumba, kwa achibale, mu mpingo ndi kwa anansi, kusukulu ndi kuntchito.

Nyimbo Na. 70 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena