Nyimbo 84
Ntchito Zazikulu ndi Zodabwitsa za Mulungu
1. Mulungu Wamphamvuyonse,
Ntchito zanu nzazikulu!
Pansi mwezi ndi nyenyezi
Zimakudziŵikitsani.
2. Njira zanu nzolungama,
Woweruza wathu Mfumu!
Chilengedwe chitamanu,
Bwanji athu sayamika?
3. Ndani sadzakuwopani
Ndi kukuza dzina lanu?
Muli Wokhulupirika, Mulungu
Wammwambamwamba.
4. Malamulowo ngambiri!
Asonyeza chilungamo!
Mitundu idze kwa inu
Ndikudzalambira inu.