Ulaliki Wosavuta Umagwira Mtima
1 N’chifukwa chiyani nthaŵi zambiri anthu amakonda kumvetsera uthenga wa Ufumu kwa ana? Chifukwa chimodzi n’chakuti amanena zosavuta kumva. Ofalitsa ena amaganiza kuti kulalikira mogwira mtima kumafuna kulankhula mwaluso. Komabe, zimene zakhala zikuchitika zikusonyeza kuti ulaliki wosavuta ndiponso womveka ndi umene umakhala wogwira mtima.
2 Polengeza Ufumu wa Mulungu Yesu anali kufeŵetsa ulaliki wake, sanali kupita m’mbali ndipo anaphunzitsa ophunzira ake kuchita zimenezo. (Mat. 4:17; 10:5-7; Luka 10:1, 9) Ankakopa chidwi cha omvetsera ake ndi kuwafika pamtima mwa kugwiritsa ntchito mawu, mafunso ndi mafanizo osavuta. (Yoh. 4:7-14) Tingachite bwino kutengera chitsanzo chake ndi kulalikira zosavuta kumva.
3 Tikufunika kulengeza ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ (Mat. 24:14) Kugwiritsa ntchito Ufumu monga mutu wanu wa nkhani kudzathandiza ulaliki wanu kukhala wosavuta. Lankhulani nkhani zokhudza omvetsera anu. Akazi amakonda kwambiri nkhani za banja m’malo mwa zandale. Nkhani ya ntchito ndi chitetezo cha banja imawakhudza kwambiri abambo. Achinyamata amafuna kudziŵa za tsogolo lawo; okalamba amafuna za thanzi labwino ndi zachitetezo. Anthu amachita chidwi kwambiri ndi nkhani zochitika m’dera lawo osati kutali. Mukakambirana nkhani zokhudza nonsenu, yambani kukambirana madalitso amene anthu omvera adzalandira mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu. Mawu osavuta ndi osankhidwa bwino ochepa chabe kudzanso lemba, angakhale abwino kwambiri podzutsa chidwi cha omvetsera anu.
4 Mungayambe kukambirana motere:
◼ “Mungavomereze kuti anthu akuzunzika ndi matenda ambiri osachiritsika. Koma kodi mukudziŵa kuti Mulungu walonjeza kuti achotsa matenda onse ndi imfa posachedwapa?” Yembekezani yankho, ndiyeno ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4.
5 Mogwiritsa ntchito ulaliki womveka ndi wosavuta kumva, mufiketu maganizo ndi mitima ya anthu ambiri m’gawo lanu, kuwathandiza kudziŵa Yehova ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.—Yoh. 17:3.