Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Dec. 15
“Ikafika nthaŵi ino chaka chilichonse, anthu ambiri amakumbukira Yesu Kristu, omukhulupirira ndi osam’khulupirira omwe. Ena amati sanali munthu weniweni. Nanga inuyo mumaganiza bwanji? [Akayankha, ŵerengani Mateyu 16:15, 16.] Ndikukhulupirira kuti mukasangalala kuŵerenga nkhani iyi yonena za ‘Yesu Weniweni’ ndiponso kuona momwe zochita zake zikukukhudzirani panopo ndi mmene zidzakukhudzireni m’tsogolo.”
Galamukani! Jan. 8
“Kodi simukuvomereza kuti tifunika chakudya chabwino ndi chodalirika kuti titeteze moyo wathu? [Muyembekezeni ayankhe.] Onani zimene Mulungu analonjeza anthu ake kalelo m’nthaŵi za m’Baibulo. [Ŵerengani Levitiko 26:4, 5.] Galamukani! imafotokoza zinthu zimene zikudetsa nkhaŵa masiku ano pankhani ya zimene timadya. Imanenanso za nthaŵi imene Mulungu adzatipatsa chitetezo padziko lonse.”
Nsanja ya Olonda Jan. 1
“Kodi mumadabwa chifukwa chake anthu ena savutika kupeza zinthu zofunika pamoyo wa munthu pomwe ena amavutika zedi kuti azipeze? Baibulo limanena za nkhani imeneyi. [Ŵerengani Yobu 34:19.] M’magazini iyi afotokoza momwe Mulungu adzathetsere kusankhana magulu.”
Galamukani! Jan. 8
“Tonse tikudziŵa za tsokali limene lagwedeza dziko lonse. Kuyambira pamene zimenezi zinachitika, anthu ambiri afuna chilimbikitso ndi chithandizo chachikulu. Nkhani ino mwa zina, ikufotokoza zimene Mboni za Yehova zakhala zikuchita pothandiza anthu opulumuka pa tsoka limeneli ndi anthu othandiza ovulala ndiponso anthu amene abale awo anamwalira pa tsokali.”