Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Feb. 15
“Kodi munafunsapo momwe mungatsogolere bwino moyo wanu ndiponso momwe mungasankhire bwino zinthu zofunika kwambiri? [Muyembekezeni ayankhe.] Ena mwa malangizo amene angakuthandizeni kuchita zimenezo, monga Lamulo la Chikhalidwe, amapezeka m’Baibulo. [Ŵerengani Mateyu 7:12.] Kodi ndi mfundo zachikhalidwe za Mulungu zina ziti zimene zingatithandize mwachindunji? Mudzapeza yankho m’magazini iyi.”
Galamukani! Mar. 8
“Mwina mwaona kuti masiku ano malo antchito ambiri aopsa zedi. Magazini iyi ili ndi malingaliro othandiza a momwe tingatetezere malo antchito. Ikusonyezanso kuti maganizo abwino amene timakhala nawo pantchito amakhudza thanzi lathu. Chonde mukaiŵerenge.”
Nsanja ya Olonda Mar. 1
“Ambirife tikuda nkhaŵa kuti kaya m’tsogolo muli zotani chifukwa cha zimene zikuchitika masiku ano. M’pemphero lotchuka, Yesu Kristu ananena chifukwa chake tingayembekeze tsogolo labwino. [Ŵerengani Mateyu 6:9, 10.] Anthu akuchitanso zolakwa zimene anthu akale ankachita. Koma nthaŵi imeneyo, amene anali kutumikira Mulungu anali ndi tsogolo labwino. Magazini iyi ikusonyeza momwe ifenso tingakhalire ndi tsogolo labwino.”
Galamukani! Mar. 8
“Baibulo limagogomezera kufunika kwa maphunziro abwino. [Ŵerengani Miyambo 2:10, 11.] Ambirife timadziŵa kuti n’kofunika kuti ana azikhala ndi aphunzitsi odziŵa bwino ntchito yawo. Galamukani! iyi ikufotokoza kufunika kwa ntchito ya aphunzitsi, momwe tingasonyezere kuyamikira zimene amachita, ndiponso zimene makolo angachite pothandiza aphunzitsi pantchito yawo yovutayi.”