Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Apr. 15
“Kulikonse anthu amafuna moyo wabwino, monga kupeza ntchito yabwino ndi kukhalabe pantchitoyo. Koma kodi mumadziŵa kuti kulipo kumene mungapeze moyo wabwino, umene mungakhale nawo kwamuyaya? [Ŵerengani Salmo 16:8, 9.] Nsanja ya Olonda iyi ifotokoza kumene tingapeze moyo wabwino weniweni.”
Galamukani! May 8
“Anthu ambiri masiku ano akuchoka m’zipembedzo zodziŵika n’kumalambira Mulungu m’njira yawoyawo. Kodi mukuganiza bwanji za nkhani imeneyi? [Muyembekezeni ayankhe.] Baibulo limasonyeza kuti kalambiridwe kathu ndi nkhani yofunika kwambiri kwa Mulungu. [Ŵerengani Yohane 4:24.] Galamukani! iyi ikufotokoza njira yabwino yopezera zosoŵa zanu zauzimu.”
Nsanja ya Olonda May 1
“Kodi mukudziŵa munthu wina amene akudwala kwambiri kapena wolumala? Anthu ngati ameneŵa amafunika kuwalimbikitsa si choncho nanga? Koma kodi tinganene chiyani powalimbikitsa? Baibulo lili ndi mawu olimbikitsa. [Ŵerengani Yesaya 35:5, 6.] Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza chifukwa chake tiyenera kukhulupirira kuti ulosi umenewu udzakwaniritsidwa.”
Galamukani! May 8
“Chaka chathachi, anthu asokoneza mtendere kwambiri kusiyana ndi zaka za m’mbuyomo. Kodi mukuganiza kuti maboma a anthu angabweretse mtendere padziko lonse? [Akayankha, ŵerengani Yesaya 2:4.] Galamukani! iyi ikufotokoza chifukwa chake tiyenera kukhulupirira kuti posachedwapa padzakhala mtendere padziko lonse.”