Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Apr. 15
“Anthu ena amaganiza kuti zonse zimene zimachitika pamoyo wa munthu, kuphatikizapo masoka, chimakhala chifuniro cha Mulungu. Kodi munaganizapo zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri amalidziŵa pemphero ili. [Ŵerengani Mateyu 6:10b.] Kodi chifuniro cha Mulungu polenga dziko lapansi n’chotani, ndipo kodi ndi liti pamene chidzakwaniritsidwe chonse? Magazini iyi ikupereka yankho la m’Baibulo.”
Galamukani! May 8
“Masiku ano, anthu ena amadziona kuti alibe chiyembekezo chilichonse. Kodi inuyo nthaŵi zina mumaonanso choncho? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Aroma 15:4.] Anthu ambiri amazindikira kufunika kokhala ndi chiyembekezo. Musangalala kuona zifukwa zisanu ndi ziŵiri za m’Malemba zokhalira ndi chiyembekezo zimene zili mu Galamukani! iyi.”
Nsanja ya Olonda May 1
“Poyesa kusintha anthu kuti akhale abwinopo, atsogoleri ena achipembedzo amaloŵerera m’ndale. Komabe, taonani zimene Yesu anachita anthu akufuna kumulonga ufumu. [Ŵerengani Yohane 6:15.] Yesu anaika mtima wake pachinthu chimene chikathandize ena kosatha. Magazini iyi ikufotokoza za chinthu chimenecho.”
Galamukani! May 8
“Anthu ambiri amakumana ndi mavuto kuntchito. Ena amavutitsidwa ndi anzawo akuntchito. Kodi mukudziŵa kuti Baibulo lili ndi malangizo amene angatithandize kulimbana ndi mavuto ngati amenewo? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Miyambo 15:1.] Magazini iyi ili ndi mfundo zothandiza pankhani ya zimene tingachite kuti tikhalebe pamtendere ndi ena kuntchito.”