Mmene Mungafalitsire Buku la Yandikirani kwa Yehova
◼ Baibulo lanu lili kumanja, nenani kuti: “Anthu ambiri okhulupirira Mulungu amafuna kuyandikana naye kwambiri. Kodi mumadziŵa kuti Mulungu amatipempha kuyandikira kwa iye? [Ŵerengani Yakobo 4:8.] Buku ili lakonzedwa kuti litithandize kuyandikira kwa Mulungu pogwiritsira ntchito Baibulo lathulathu.” Ŵerengani ndime 1 patsamba 16.
◼ Baibulo lanu lili kumanja, nenani kuti: “Lerolino, m’dziko muli kupanda chilungamo. Zinthu zili mmene afotokozera apa. [Ŵerengani Mlaliki 8:9b.] Ena amadabwa ngati Mulungu zimam’khudza n’komwe. [Ŵerengani ziganizo ziŵiri zoyambirira m’ndime 4 patsamba 119.] Mutu umenewu ukufotokoza chifukwa chake Mulungu walola kupanda chilungamo kwakanthaŵi.”