Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Apr. 15
“Zaka zaposachedwapa anthu ambiri aona kuti moyo wauzimu ukuloŵa pansi. Kodi inunso mwaona zimenezi? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Salmo 119:105.] Moyo wauzimu ungathandize anthu kupeŵa mavuto ambiri pamoyo wawo. Magazini iyi ikutchula kumene tingapeze zinthu zimene zingatithandize kukhala ndi moyo wauzimu.”
Galamukani! Apr. 8
“Kodi nanunso mwaona kuti anthu ambiri masiku ano akuvutika kuti agone mokwanira? [Yembekezani ayankhe.] Nkhaŵa kapena mavuto ndi zimene zingachititse vuto limeneli. [Ŵerengani Mlaliki 5:12.] Magazini iyi ikufotokoza zimene zimapangitsa kuti anthu azisoŵa tulo ndipo ili ndi mfundo zothandiza zimene tingachepetsere vuto la kusoŵa tulo.”
Nsanja ya Olonda May 1
“Mafunso ena anthu sangathe kuyankha. Monga funso ili. [Ŵerengani Yobu 21:7.] Kodi munayamba mwakhala ndi funso limene mumafuna kufunsa Mulungu? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza momwe anthu a m’madera onse a padziko lapansi apezera mayankho okhutiritsa a mafunso atatu ofunika kwambiri pamoyo.”
Galamukani! Apr. 8
“Kodi si zomvetsa chisoni kuti miyoyo ya achinyamata ambiri yawonongeka ndi mankhwala osokoneza bongo? [Yembekezani ayankhe.] Nthaŵi zambiri mavuto amayamba pamene achinyamata akuyanjana ndi anzawo oipa. [Ŵerengani 1 Akorinto 15:33.] Galamukani! iyi ikufotokoza zimene zimayambitsa achinyamata kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndiponso zimene makolo angachite kuti ateteze ana awo.”