Mawu a Mulungu Ndi Choonadi
1. Kodi ndi zinthu zofunika zotani zimene zili m’Baibulo?
1 “Chiŵerengero cha mawu anu ndicho choonadi,” analemba choncho wamasalmo. (Sal. 119:160) M’Mawu ake ouziridwa, Yehova amayankha mokhutiritsa mafunso ofunika kwambiri m’moyo. Amatonthoza ndi kupereka chiyembekezo kwa anthu amene akuvutika. Ndipo amatisonyeza zimene tingachite kuti tiyandikane naye. Mzimayi wina poyamikira anati: “Kuphunzira choonadi cha m’Baibulo kuli ngati kutuluka m’malo a m’dima wandiweyani n’kuloŵa m’chipinda chowala bwino.” Kodi mumayesetsa kuuza ena choonadi cha Mawu a Mulungu paliponse pamene mwapeza mpata?
2. Kodi Baibulo limasintha bwanji moyo wa munthu kuti ukhale wabwino?
2 Baibulo Limasintha Miyoyo Komanso Limakopa Anthu Padziko Lonse: Choonadi cha m’Baibulo chili ndi mphamvu imene imakhudza mitima ndiponso imasintha miyoyo. (Aheb. 4:12) Mzimayi wina wachitsikana wotchedwa Rosa anayamba kuchita uhule komanso kumwa mowa mwauchidakwa ndi kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo. Iye anati: “Tsiku lina, pamene ndinkaona kuti palibenso chabwino chilichonse m’moyo wanga, anthu aŵiri Amboni, mwamuna ndi mkazi wake anandilankhula n’kundiuza mmene Baibulo lingatithandizire kuthetsa mavuto athu. Ndinayamba kuphunzira Mawu a Mulungu, ndipo ndinaona kuti anali osangalatsa kwambiri. Pasanathe mwezi umodzi, ndinaona kuti ndapeza mphamvu zondithandiza kuti ndiyambe kukhala moyo watsopano wa makhalidwe abwino. Chifukwa chakuti tsopano ndinali ndi cholinga m’moyo wanga, panalibenso chifukwa chomwera mowa kapena kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo kuti azindithandiza. Ndipo chifukwa chofunitsitsa kukhala bwenzi la Yehova, ndinayesetsa kukhala mogwirizana ndi zimene iye amafuna. Ndikadapanda kupeza nzeru zothandiza zimene zili m’Mawu a Mulungu, ndikukhulupirira kuti ndikanakhala pano nditadzipha.”—Sal. 119:92.
3. Kodi n’chifukwa chiyani sitiyenera kupeŵa kugaŵana uthenga wa m’Baibulo ndi anthu ena?
3 Mosiyana ndi mabuku ambiri masiku ano, Baibulo limakopa anthu a ‘mtundu uliwonse, fuko, ndi manenedwe.’ (Chiv. 7:9) Cholinga cha Mulungu n’choti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Tim. 2:4) Choncho sitiyenera kungoganiza kuti munthu wina sangamvetsere uthenga wabwino mwa kungoona moyo wake ayi. M’malomwake, tizigaŵanaY uthenga wa Ufumu ndi anthu onse, ndipo tizitero mwa kuŵerenga Baibulo lenilenilo paliponse pamene tingathe kutero.
4. Kodi tingagwiritsire ntchito bwanji Baibulo polalikira?
4 Ŵerengani Malemba: Timapeza mipata yambiri yoti n’kugwiritsira ntchito Baibulo mu utumiki. Mukamagaŵira magazini, muziyesetsa kuŵerenga lemba limene amaliika pa zomwe munganene pogaŵira magazini. Anthu ena akamagaŵira buku logaŵira mwezi umenewo, amaona kuti n’zothandiza kuŵerenga lemba limene alisankha mosamala akamayamba kukambirana ndi munthu. Mukamachita maulendo obwereza, muziŵerenga lemba la m’Baibulo limodzi kapena angapo nthaŵi iliyonse kuti mum’thandize mwininyumbayo kudziŵa zinthu molondola pang’onopang’ono. Mukamachititsa phunziro la Baibulo, muzitsindika kwambiri mfundo za m’malemba ofunika m’nkhaniyo. Ngati simuli mu utumiki, muzikhala ndi Baibulo pafupi kuti muthe kuligwiritsira ntchito ngati mpata wolalikira mwamwayi utapezeka.—2 Tim. 2:15.
5. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kugwiritsira ntchito Baibulo mu utumiki wathu?
5 Tiyeni tithandize ena kupindula ndi mphamvu yosintha miyoyo ya Mawu a Mulungu a choonadi mwa kugwiritsira ntchito Baibulo paliponse pamene tapeza mpata wabwino mu utumiki wathu.—1 Ates. 2:13.