Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/05 tsamba 1
  • Yamikani Yehova Chifukwa cha Chifundo Chake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yamikani Yehova Chifukwa cha Chifundo Chake
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amadalitsa Khama Lathu Loyesetsa Kuti Tipezeke pa Chikumbutso
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • “Kondani Yehova, Inu Nonse Okondedwa”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Thandizani Ena Kupindula ndi Dipo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Chifukwa Chake Timapezeka pa Chikumbutso
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 2/05 tsamba 1

Yamikani Yehova Chifukwa cha Chifundo Chake

Imfa ya Kristu Tidzaikumbukira pa March 24

1. Kodi Yehova anationetsa bwanji chifundo chake?

1 Wamasalmo anafuula kuti: “Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwiza zake za kwa ana a anthu!” (Sal. 107:8) Chifundo cha Mulungu sichingothera pa kukhala ndi mtima wachisoni kwa anthu. Mfundo imeneyi anaimveketsa bwino m’mawu awa osonyeza kuyamikira akuti: “Chifundo chanu, Mulungu, chinandichirikiza.” (Sal. 94:18) Ndithudi, Yehova anaonetsa chifundo chapadera kwambiri chimenechi pamene anapereka Mwana wake wobadwa yekha m’malo mwathu.—1 Yoh. 4:9, 10.

2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikuyamika Yehova?

2 Pamene Chikumbutso cha imfa ya Kristu chikuyandikira, kodi tingam’yamikire motani “Mulungu wa chifundo” ameneyu? (Sal. 59:17) Aliyense afunika kupeza nthawi yosinkhasinkha za masiku omalizira a Yesu pamene anali padziko lapansi pano. (Sal. 143:5) Kungakhalenso kothandiza kutsatira ndandanda yapadera ya Chikumbutso yowerenga Baibulo imene ili m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku, ndipo ngati n’kotheka, werenganinso ndi kufufuza zowonjezera m’mitu 112 mpaka 116 m’buku la Munthu Wamkulu limodzinso ndi mabuku ena ofotokoza Baibulo. Sinkhasinkhani pa ndime zimene mwawerengazo, ndi kuzama nazo. (1 Tim. 4:15) Sikuti kuwerenga Mawu a Mulungu ndi pemphero zimangolimbikitsa mitima yathu komanso zimasonyeza kuti Yehova timam’konda.—Mat. 22:37.

3, 4. (a) Kodi tingautsanzire bwanji mzimu wa abale athu a ku Liberia? (b) Kodi mukukonza zoitana ndani ku Chikumbutso?

3 Limbikitsani Ena Kuyamika Mulungu: Chaka chatha, anthu okwanira 16,760,607 padziko lonse anapezeka pa Chikumbutso. M’mudzi winawake ku Liberia, abale analemba kalata kwa a mfumu, kuwadziwitsa zoti adzachita Mgonero wa Ambuye m’mudzimo. Mfumuyo inauza abalewo kuti adzagwiritse ntchito bwalo losewerera mpira la m’mudzimo pochita mwambowu ndipo inalengeza m’dera lonselo kuitana anthu kuti adzakhale nawo pa mwambo umenewu. Ngakhale kuti m’mudzimo munali ofalitsa asanu okha, koma anthu okwana 636 anafika pa Chikumbutsocho.

4 Mofananamo, tikufunika kuthandiza anthu ambiri mmene tingathere kuti adzakhale nafe limodzi pa mwambo wa Chikumbutso. Bwanji osakonza mndandanda wa anthu amene mukufuna kudzawaitana? Zithunzi zimene zili patsamba la kumapeto kwa Galamukani! ya March 8 ndi Nsanja ya Olonda ya March 15 zikuitanira anthu ku mwambowu. Mungagwiritsenso ntchito timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso. Lembani mooneka bwino pa kapepalako nthawi ndi malo a mwambowu, ndi kupereka kamodzi kwa munthu aliyense amene mwamuitana. Tsiku la March 24 likamayandikira, kumbutsani aliyense ndiponso malizitsani kukonza zilizonse zimene zingafunike.

5. Kodi ophunzira Baibulo athu tingawalimbikitse bwanji kuti adzapezeke pa Chikumbutso?

5 Kodi tingatani kuti tithandize ophunzira Baibulo amene sanayambe kusonkhana kuti adzapindule mokwanira ndi mwambo umenewu? Muzipatula mphindi zochepa chabe nthawi zonse pamene mukuphunzira nawo n’kumawathandiza kumvetsetsa kufunika kwa mwambo umenewu. Nkhani zothandiza mungazipeze mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2004, tsamba 3 mpaka 7, ndi m’buku la Kukambitsirana tsamba 70 mpaka 74.

6. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kulandira bwino alendo pa Chikumbutso?

6 Landirani Bwino Alendo: Pa Chikumbutsopo, dzalankhuleni ndi alendo ndi kuwalandira bwino. (Aroma 12:13) Dzakhaleni pamodzi ndi amene munawaitana, ndipo onetsetsani kuti ali ndi Baibulo ndi buku la nyimbo. Tikufunika kudzakhala oyambirira kupereka moni wachisangalalo kwa abale kapena alongo onse amene anasiya kusonkhana ndi mpingo koma ayesetsa kudzapezeka nawo pa mwambowu. Chikondi chimene tingawasonyeze chingathe kuwathandiza kuyambiranso kusonkhana ndi mpingo mokhazikika. (Luka 15:3-7) Pa mwambo wopatulikawu, tiyeni tiyesetse kuchita zonse zomwe tingathe kulimbikitsa ena kudzakhala nafe limodzi n’kuyamika Yehova chifukwa cha “chifundo chake chodabwiza.”—Sal. 31:21.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena