Nyengo ya Chikumbutso ndi Nthawi Yochita Zambiri
1. Kodi nyengo zoikika zinawakhudza bwanji Aisrayeli oopa Mulungu?
1 Chaka chilichonse pa nthawi zoikidwiratu, Aisrayeli akale ankakondwerera “nyengo zoikika za Yehova.” (Lev. 23:2) Kutenga nthawi akuganizira mozama za ubwino wa Mulungu wawo kunawapangitsa kukhala ndi chimwemwe chachikulu ndiponso anakhala achangu pa kulambira koyera.—2 Mbiri 30:21–31:2.
2, 3. N’chifukwa chiyani kuli koyenera kuti tiwonjezere ntchito zathu zauzimu m’nyengo ya Chikumbutso, ndipo kodi tidzachita liti Chikumbutso?
2 Masiku athu ano, ntchito yathu yosangalatsa yotumikira Mulungu imawonjezeka chaka chilichonse pa nyengo ya Chikumbutso. Ndi nthawi imene timaganizira mozama kwambiri za mphatso ya mtengo wapatali imene Yehova anaipereka m’malo mwathu. Mphatso imeneyo ndi Mwana wake wobadwa yekha. (Yoh. 3:16; 1 Pet. 1:18, 19) Tikamasinkhasinkha za chikondi chimene Mulungu ndi Mwana wake anasonyeza, zimatilimbikitsa kuyamikira Yehova ndi kudzipereka kuchita chifuniro chake.—2 Akor. 5:14, 15.
3 Chaka chino Mgonero wa Ambuye udzachitika Lachinayi, pa March 24, dzuwa litalowa. Kodi tingatani kuti tiwonjezere utumiki wathu m’miyezi ya March, April, ndi May?
4, 5. (a) Kodi n’chiyani chimene chawathandiza ena kufikira anthu ambiri ndi uthenga wabwino? (b) Ndi njira iti yomwe mwaiona kukhala yothandiza kwanuko?
4 Kufikira Anthu Ochuluka: Pezani njira za mmene mungafikire anthu ambiri monga mmene mungathere pamene mupita mu utumiki wa kumunda. Kodi mungakonze zochita ulaliki wa khomo ndi khomo nthawi imene anthu ambiri ali panyumba, monga nthawi ya kumasana kapena madzulo? Ngati ena m’gulu lanu la phunziro la buku akufuna kuti azipita mu utumiki phunziro lisanayambe, woyang’anira phunziro la buku angakonze zoti pazikhala msonkhano wachidule wokonzekera utumiki kenako n’kukalalikira gawo limene lili chapafupi.
5 Njira ina imene mungafikire nayo anthu ambiri ndiyo kulalikira m’malo amene mumapezeka anthu ambiri. Mlongo wina ku Japan anaganiza zochita upainiya wothandiza ngakhale kuti ankagwira ntchito yolembedwa. Mkulu mu mpingo anam’thandiza pomuuza kuti akhoza kumachita ulaliki wa mumsewu pafupi ndi malo okwerera sitima tsiku lililonse asanapite ku ntchito. Atachotsa mantha ndi kupirira kusekedwa ndi antchito ena oyendera, anakhala ndi anthu okwana 40 amene amakawapatsira magazini, kuphatikizapo antchito oyendera, ogwira ntchito pa malo okwerera sitima, ndi eni ake a masitolo amene ali chapafupi. Anagawira magazini 235 mwezi uliwonse. Mwa kukambirana ndi anthu mfundo za m’Malemba kwa kanthawi kochepa tsiku lililonse, anatha kuyambitsa maphunziro a Baibulo okwana sikisi.
6. Kodi achinyamata angawonjezere motani ntchito zawo zauzimu?
6 Mipata Yolalikira: Ofalitsa omwe ali pasukulu amakhala ndi nthawi za tchuthi pa chaka. Nthawi imeneyi ingakhale yabwino kuchita upainiya wothandiza. Kuwonjezeranso pamenepo, Akristu achinyamata angathe kuwonjezera utumiki wawo mwa kulalikira kusukulu. Mungadabwe kuona mmene anzanu a m’kalasi angakhalire osangalala kufuna kudziwa za zikhulupiriro zanu. Bwanji osapezerapo mwayi wolalikira panthawi yokambirana m’kalasi kapena pamene mwauzidwa kulemba nkhani kusukulu? Ena akwanitsa kulalikira mwa kugwiritsa ntchito mavidiyo athu. Ena ayambitsa maphunziro a Baibulo ndi anzawo a m’kalasi ndipo awathandiza kupita patsogolo mpaka kudzipatulira ndi kubatizidwa. Zimenezi ndi njira zabwino ‘zolemekezera dzina la Yehova.’—Sal. 148:12, 13.
7. (a) Kodi mbale wina anagwiritsa ntchito motani mpata wake kulalikira ena? (b) Kodi zinthu zofanana ndi zimenezi zakuchitikiranipo?
7 Tsiku ndi tsiku, yesani kupeza njira zouzira anthu za Mulungu ndi malonjezo ake osangalatsa. Mbale wina amene amakwera sitima zimodzimodzi tsiku lililonse amalalikira anzake opita nawo ku ntchito pakafunika kutero. Mwachitsanzo, akamadikira sitima yoti akwere, ankalalikira mnyamata wina tsiku lililonse kwa mphindi pafupifupi zisanu. Mapeto ake, mnyamata ameneyu limodzi ndi mnzake anavomera kuphunzira Baibulo. Phunziro la Baibulolo limachitikira m’sitimayo akamapita. Kenako m’kupita kwa nthawi, mayi wina wachikulire amene ankamvetsera makambirano awowo anam’fikira mbaleyu ndi kum’pempha kuti aziphunzira naye Baibulo. Mayi ameneyunso akusangalala ndi phunziro lake pa masiku amene amakwera sitimayo. Mwanjira imeneyi, mbaleyo waphunzira ndi anthu okwana 10 m’sitimayo.
8. Kodi ndi njira iti ya utumiki imene ingathandize amene sangathe kuchita zambiri mu utumiki chifukwa cha ukalamba kapena matenda kuti awonjezere utumiki wawo?
8 Nanga bwanji ngati simungathe kuchita zambiri chifukwa cha ukalamba ndi matenda? Pangakhalebe njira zina za mmene mungawonjezere kuyamikira kwanu Yehova. Kodi mwayesapo ulaliki wa patelefoni? Ngati simukudziwa mmene mungachitire ulaliki umenewu, m’fotokozereni woyang’anira phunziro la buku wanu. Angakonze zoti ofalitsa amene amagwiritsa ntchito njira imeneyi azilalikira nanu limodzi. Mwa kulalikirira limodzi, mukhoza kuphunzira luso kwa wina ndi mnzake ndi kuthandizana kuchita ulaliki wogwira mtima. Mfundo zothandiza za mmene mungachitire ulaliki wa patelefoni mungazipeze mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2001, tsamba 3 ndi 4.
9. Kodi tingatani kuti tithandize ophunzira Baibulo kuti ayenerere kupita mu utumiki limodzi ndi mpingo?
9 Kupezeka pa Chikumbutso kungalimbikitse atsopano kufuna kuyamikira Yehova kwambiri. Mungawathandize kuchotsa mantha alionse amene angakhale nawo pofuna kuchita ulaliki mwa kuwauza zokumana nazo zolimbikitsa za mu utumiki wa kumunda ndiponso mwa kupitirizabe kuwaphunzitsa mmene angafotokozere mfundo za m’Baibulo ndi kuikira kumbuyo chikhulupiriro chawo. (1 Pet. 3:15) Ngati wophunzira Baibulo akufuna kuyamba kulalikira uthenga wabwino, lankhulani ndi woyang’anira wotsogolera. Adzakonza zoti aonane ndi wophunzirayo kuti aone ngati angayenerere kupita mu utumiki limodzi ndi mpingo. Zimasangalatsadi mtima wa Yehova kuona atsopano akuima kumbali ya ulamuliro wake wa m’chilengedwe chonse.—Miy. 27:11.
10. (a) Kodi ndandanda yokonzedwa bwino ingatithandize bwanji kuchita upainiya wothandiza? (b) Kodi munakwanitsa kuchita upainiya wothandiza m’nyengo ya Chikumbutso ya chaka chatha? Munachita bwanji kuti mukwanitse?
10 Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza? Maola 50 amene amafunika pa upainiya wothandiza sitiyenera kuwaona mopepuka. (Mat. 5:37) Zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kukonza zothera maola 12 mu utumiki wa kumunda mlungu uliwonse. Kodi pa zitsanzo za mmene mungakonzere ndandanda ya upainiya wothandiza zimene zili pa tsamba 5, chilipo chimene chikugwirizana ndi zochita zanu? Ngati palibe, kodi mungakonze ndandanda imene ingakupatseni mpata wochita upainiya wothandiza m’miyezi ya March, April, kapena May? M’pempheni Yehova kudalitsa khama lanu pofuna kuwonjezera utumiki.—Miy. 16:3.
11. Kodi akulu ndi atumiki otumikira angatani kuti athandize amene adzachite upainiya wothandiza?
11 Akulu ndi atumiki otumikira adzakuthandizani kuti nyengo ya Chikumbutso imeneyi ikhale nthawi yapadera yoyamikira Yehova. Mwachionekere, ambiri a iwo adzachita upainiya wothandiza. Akulu adzakonza zoti pakhale misonkhano yokonzekera utumiki yowonjezereka, monga masana, madzulo m’kati mwa mlungu, ndi Loweruka ndi Lamlungu, monga mmene kungafunikirire. Kuti akulu adziwe malo omwe misonkhanoyi izichitikira ndi nthawi yake, ndiponso amene azidzapezekako kuti atsogolere gulu, akuluwo angalankhule ndi amene akonza zochita upainiyawo kapena kulankhula ndi amene akuganiza zodzachita upainiya. Akulu adzayesetsa kukonza zoti pazikhala ofalitsa ena oti muzilowera nawo limodzi mu utumiki mogwirizana ndi masiku ndi nthawi imene inu mwakonza yolowera mu utumiki. Mwa njira imeneyi, pangakhale pulogalamu yokhazikika bwino ndipo zotsatira zake zingakhale zabwino.—Miy. 20:18.
12. Kodi n’chiyani chimatilimbikitsa kuyamikira Yehova nthawi zonse?
12 Chitani Zomwe Mungathe: Ngati simungathe kuchita upainiya wothandiza, kumbukirani kuti Yehova amayamikira khama lathu ndi nsembe zathu ‘monga momwe tili nazo, osati monga zitisowa.’ (2 Akor. 8:12) Tili ndi zifukwa zambiri zimene tingathokozere Yehova. Pa chifukwa chabwino Davide analemba kuti: “Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kum’lemekeza kwake kudzakhala m’kamwa mwanga kosalekeza.” (Sal. 34:1) Tiyeni nafenso chikhale cholinga chathu m’nyengo ya Chikumbutsoyi.
[Bokosi patsamba 3]
Kodi Mungatani Kuti Muchite Zambiri?
◼ Lalikirani pamene anthu ali panyumba
◼ Lalikirani m’malo amene mumapezeka anthu ambiri
◼ Lalikirani kuntchito kapena kusukulu
◼ Chitani ulaliki wa patelefoni
◼ Chitani upainiya wothandiza
[Tchati patsamba 5]
Zitsanzo za Ndandanda Yochitira Upainiya Wothandiza Njira Zopangira Ndandanda ya Maola 12 a mu Utumiki wa Kumunda Mlungu Uliwonse
M’mawa—Lolemba Mpaka Loweruka
Lamlungu lingalowe m’malo mwa tsiku lina lililonse.
Tsiku Nthawi Maola
Lolemba M’mawa 2
Lachiwiri M’mawa 2
Lachitatu M’mawa 2
Lachinayi M’mawa 2
Lachisanu M’mawa 2
Loweruka M’mawa 2
Onse Pamodzi: 12
Masiku Awiri Athunthu
Mukhoza kusankha masiku ena alionse awiri pa mlungu (Mogwirizana ndi masiku amene mungasankhe, ndandanda imeneyi ingakupatseni maola 48 okha pa mwezi.)
Tsiku Nthawi Maola
Lachitatu Tsiku Lonse 6
Loweruka Tsiku Lonse 6
Onse Pamodzi: 12
Madzulo Awiri ndi Loweruka ndi Lamlungu
Mukhoza kusankha madzulo alionse awiri a m’kati mwa mlungu.
Tsiku Nthawi Maola
Lolemba Madzulo 1 1⁄2
Lachitatu Madzulo 1 1⁄2
Loweruka Tsiku Lonse 6
Lamlungu M’mawa Kapena Masana Okha 3
Onse Pamodzi: 12
Masana Atatu ndi Loweruka
Lamlungu lingalowe m’malo mwa tsiku lina lililonse.
Tsiku Nthawi Maola
Lolemba Masana 2
Lachitatu Masana 2
Lachisanu Masana 2
Loweruka Tsiku Lonse 6
Onse Pamodzi: 12
Ndandanda Yanga ya mu Utumiki
Sankhani chiwerengero cha maola a tsiku lililonse.
Tsiku Nthawi Maola
Lolemba
Lachiwiri
Lachitatu
Lachinayi
Lachisanu
Loweruka
Lamlungu
Onse Pamodzi: 12