Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/05 tsamba 8
  • Kufikira Anthu Ambiri Mmene Tingathere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufikira Anthu Ambiri Mmene Tingathere
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Olengeza Ufumu Ali Okangalika Padziko Lonse Lapansi
    Nsanja ya Olonda—1994
  • ‘Chitani Zinthu Zonse Kaamba ka Uthenga Wabwino’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Yehova Amakonza Njira
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 7/05 tsamba 8

Kufikira Anthu Ambiri Mmene Tingathere

1. Kodi Akristu oyambirira anachitanji kuti afikire anthu ambiri ndi uthenga wabwino mmene akanathera?

1 Otsatira oyambirira a Yesu, anayesetsa ndi mtima wonse kufalitsa uthenga wa Ufumu. Anagwiritsa ntchito njira zothandiza kuti afikitse uthenga wabwino kwa anthu ambiri mmene akanathera. Akristu amene ankalemba Baibulo, analemba mawu ouziridwawo m’Chigiriki chofala chomwe chinkalankhulidwa ndi aliyense mu ufumu wa Roma. Kuwonjezera apo, alaliki achangu a m’zaka zoyambirira za ma 100 ndi 200 kumka m’tsogolo, ayenera kuti anatsogolera kugwiritsa ntchito mabuku, omwe anali osavuta kugwiritsa ntchito pofufuzira maumboni kusiyana ndi mipukutu.

2, 3. (a) Kodi Yesaya 60:16 akukwaniritsidwa bwanji m’nthawi zamakono zino? (b) Kodi makina amakono akugwiritsidwa ntchito bwanji kupititsira patsogolo kulambira koyera?

2 Kugwiritsa Ntchito Makina Amakono: Yehova kudzera mwa mneneri Yesaya analosera kuti: “Udzayamwanso mkaka wa amitundu.” (Yes. 60:16) Kukwaniritsidwa kwa makono kwa ulosi umenewu n’kwakuti, atumiki a Yehova akugwiritsa ntchito zinthu zina za amitundu kupititsira patsogolo ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, mu 1914, zaka zimene zithunzi za pakanema zooneka kuti zikuyenda ndi kulankhula zinali zisanayambe kugwiritsidwa ntchito mu zamalonda, Ophunzira Baibulo anayamba kuonetsa “Sewero la Pakanema la Zachilengedwe.” Kuonetsa zithunzi zooneka kuti zikuyenda zimenezi ndiponso masilaidi zomwe zinali zakalala ndiponso za mawu kunkatenga maola asanu ndi atatu. Kuchita zimenezi kunathandiza kupereka umboni wamphamvu kwa anthu ambiri.

3 Masiku ano, anthu a Mulungu akugwiritsa ntchito makina osindikizira ogwira ntchito mofulumira kwambiri ndiponso zipangizo zina zoyendera makompyuta kufalitsira mabaibulo ndiponso mabuku ena ofotokoza Baibulo m’zinenero zambiri zedi. Njira zofulumira kwambiri zotumizira mabuku ofotokoza Baibulo, zimakafikitsa mabukuwo kumadera akutali kwambiri padziko lapansi, kukafika kwa anthu m’mayiko 235. Kudzera m’mphamvu yake ya mzimu woyera, Yehova walimbikitsa atumiki ake kugwiritsa ntchito makina amakonowa mwanzeru, ndipo choonadi cha Baibulo chafika kwa anthu ambiri kuposa n’kale lonse m’mbiri.

4. Kodi ena asintha bwanji zochita pa moyo wawo n’cholinga choti afikire anthu ambiri ndi uthenga wabwino?

4 Kusintha Zochita Zaumwini: Nawonso olambira oona akhudzika mtima kwambiri moti asintha zochita zawo n’cholinga choti afikire anthu ambiri ndi uthenga wabwino. Ambiri akukhala moyo wosalira zambiri n’cholinga chakuti atenge nawo mbali mokwanira bwino mu ntchito yolalikira. Ena asamukira kumadera kumene kukufunika olengeza Ufumu ambiri. Ndipo ena afutukula utumiki wawo mwa kuphunzira chinenero china.

5, 6. Kodi tingachitenji kuti tifikire anthu ambiri m’gawo lathu mmene tingathere?

5 Kuwonjezeranso pamenepo, tikhoza kufikira anthu ambiri ndi uthenga wabwino mwa kulalikira nthawi imene anthu ambiri amapezeka panyumba ndiponso mwa kulalikira kumene anthu angapezeke. Ngati m’gawo lanu anthu ambiri sapezeka pakhomo kuyambira m’mawa mpaka masana, kodi mungasintheko ndandanda yanu kuti muzilalikira chakumadzulo? Kodi kuli malo amene kumapezeka anthu ambiri kumene mukhoza kulalikirako? Kodi mwayesapo ulaliki wa patelefoni ndiponso kulalikira m’gawo la malonda? Kodi mumayesetsa kupeza mipata yoti mulalikire mwamwayi?

6 Ndifedi amwayi zedi kugwira nawo ntchito yolemekezeka yolalikira za dzina la Yehova ndi Ufumu wake. Ndiyetu tiyeni tipitirizebe kulalikira nawo choonadi chopatsa moyo chochokera m’Mawu a Mulungu chimenechi kwa anthu ambiri mmene tingathere.—Mat. 28:19, 20.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena