‘Chitani Zinthu Zonse Kaamba ka Uthenga Wabwino’
1. Kodi wolalikira Ufumu amafuna kuwachitira chiyani anthu ena, nanga n’chifukwa chiyani?
1 Mtumwi Paulo ankaona kuti anali ndi udindo wolalikira uthenga wabwino. (1 Akor. 9:16, 19, 23) Mofananamo, kuganizira anthu ena kuti apeze moyo wosatha kumatilimbikitsa kuyesetsa kuwauza uthenga wabwino.
2. Kodi polalikira ndife ofunitsitsa kusintha chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
2 Lalikirani Kumene Mungapeze Anthu: Msodzi wabwino samawedza nsomba pamalo ndi nthawi yabwino kwa iyeyo. Koma iye amapita pamalo amene nsomba zimapezeka komanso panthawi imene nsombazo angazipeze. Nafenso, monga “asodzi a anthu,” tiyenera kusintha ndandanda yathu kuti tizipeza anthu a m’dera lathu ndiponso kuti tizisangalala ndi mwayi wogwira nawo ntchito yosonkhanitsa “nsomba zamitundumitundu.” (Mat. 4:19; 13:47) Tikhoza kumalalikira madzulo kuti tizipeza anthu ali pakhomo ndipo m’mamawa tingamachite ulaliki wamumsewu. Cholinga cha Paulo chinali “kuchitira umboni bwino lomwe za uthenga wabwino,” motero anagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti akwaniritse cholinga chakechi.—Mac. 17:17; 20:20, 24.
3, 4. Tikakhala muutumiki, kodi tingasinthe bwanji ulaliki wathu, ndipo zinthu zingatiyendere bwanji?
3 Lalikirani Zinthu Zogwirizana Ndi Anthu a M’gawo Lanu: Nthawi zambiri asodzi amasintha njira zophera nsomba malinga ndi mtundu wansomba zimene akufuna kupha. Kodi tingalalikire bwanji uthenga wabwino wa Ufumu kuti ukhale wochititsa chidwi kwa anthu a m’gawo lathu? Tizilalikira nkhani imene ikukhudza anthu ambiri m’deralo ndipo tizimvetsera mwatcheru zimene angatiuze pankhaniyo. (Yak. 1:19) Tikhoza kuwafunsa mafunso kuti timve maganizo awo. (Miy. 20:5) Mwa njira imeneyi tingathe kulalikira uthenga wabwino mowafika pamtima. Paulo anakhala “zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana.” (1 Akor. 9:22) Kuti tiwafike anthu pamtima, tiyenera kulalikira mogwirizana ndi munthu aliyense payekha.
4 Ndi mwayi waukulu kuwauza anthu “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” (Yes. 52:7) Choncho, tiyeni ‘tichite zinthu zonse kaamba ka uthenga wabwino’ kuti tilalikire kwa anthu ambiri.—1 Akor. 9:23.