Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Sept. 15
“Padziko lonse lapansi anthu ambiri amvapo za Yesu Kristu. Ena amati iye anali munthu wotchuka chabe. Enanso amamulambira monga Mulungu Wamphamvuyonse. Kodi mukuganiza kuti Yesu Kristu anali ndani makamaka? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mwatsatanetsatane kuti Yesu anali ndani, kumene anachokera ndi kumene ali panopa.” Werengani Yohane 17:3.
Galamukani! Oct. 8
“Anthu ambiri akusowa nyumba zabwino zokhalamo. Kodi mukuganiza kuti tsiku lina aliyense adzakhala ndi nyumba yakeyake? [Yembekezani ayankhe.] Mu Galamukani! imeneyi muli lipoti laposachedwapa lonena za mavuto a kusowa kwa nyumba. Ikufotokozanso chifukwa chake tiyenera kukhulupirira kuti lonjezo ili la Mulungu lidzakwaniritsidwa.” Werengani Yesaya 65:21, 22.
Nsanja ya Olonda Oct. 1
Werengani funso limene lili pachikuto. Kenako funsani kuti: “Kodi mukuchidziwa chizindikiro chimene chikutchulidwa pamenepa? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Mateyu 24:3.] Nsanja ya Olonda imeneyi ifotokoza zinthu zisanu zazikulu zimene zili mbali ya chizindikiro ndipo ikufotokoza chifukwa chake tiyenera kukhala maso ndi chizindikiro.” Sonyezani bokosi limene lili patsamba 6.
Galamukani! Oct. 8
“Kumwetsa mowa kumayambitsa mavuto osawerengeka. Magazini iyi ikusonyeza mmene mowa ungawonongere thupi lanu. [Sonyezani chithunzi patsamba 7.] Nkhanizi zikufotokoza zimene anthu angachite kuti aleke kumwetsa mowa ndi zimene enanso angachite kuti athandize anzawo kuthetsa khalidweli.”