Mmene Mungayambitsire Maphunziro M’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
Ambirife tingasangalale kwambiri kuchititsa phunziro la Baibulo koma zimativuta kuyambitsa phunzirolo. Buku latsopano lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lingatithandize kutero. Mawu oyamba amene ali pa tsamba 3 mpaka 7 cholinga chake n’choyambitsa nkhani za m’Baibulo ndi mwini nyumba pogwiritsa ntchito bukuli. Ngakhale anthu amene angoyamba kumene kulowa m’munda sazivutika kuyambitsa maphunziro ndi bukuli.
◼ Mungayese njira iyi potsegula pa tsamba 3:
Tchulani nkhani inayake imene yafala kwanuko kapena tchulani vuto linalake limene lili m’maganizo mwa anthu ambiri a m’gawo lanu. Kenaka sonyezani mwininyumbayo mafunso amene alembedwa m’zilembo zakuda kwambiri pa tsamba 3, ndipo muuzeni kuti athirirepo ndemanga. Kenaka pitani pa tsamba 4 ndi 5.
◼ Mwina mungafune kuyamba ndi kugogomezera tsamba 4 ndi 5:
Munganene kuti, “Kodi zinthu zitasinthadi n’kukhala ngati mmene zilili pachithunzi ichi, sizingakhale bwino?” Kapena mungafunse kuti: “Kodi ndi lonjezo liti pa malonjezo awa limene mungakonde kuti likwaniritsidwe?” Mvetserani bwinobwino zimene munthuyo angayankhe.
Ngati mwininyumbayo atachita chidwi kwambiri ndi lemba linalake, musonyezeni zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani imeneyo pokambirana naye ndime zimene zikulongosola nkhaniyo m’bukuli. (Onani bokosi limene lili pa tsamba lino la mphatika.) Kambiranani monga mmene mungachitire pochititsa phunziro la Baibulo. Mungachite zimenezi ulendo woyamba, kwa mphindi zisanu kapena khumi.
◼ Njira inanso ndiyo yomulimbikitsa munthu kunena zakukhosi kwake popita pa tsamba 6:
Musonyezeni mwininyumbayo mafunso amene ali pansi patsambapo n’kumufunsa kuti, “Kodi munayamba mwadzifunsapo mafunso awa?” Ngati atachita chidwi ndi funso linalake pa mafunsowo, musonyezeni ndime za m’bukuli zomwe zikuyankha funsolo. (Onani bokosi limene lili pa tsamba lino la mphatika.) Mukayamba kukambirana nkhaniyi ndi munthuyo, ndiye kuti mukuchititsa phunziro la Baibulo.
◼ Mungapite pa tsamba 7 kuti musonyeze chitsanzo cha mmene timachitira phunziro la Baibulo:
Werengani ziganizo zitatu zoyambirira pa tsambali, ndipo kenaka pitani pa mutu 3, n’kuchita chitsanzo cha phunziroli pogwiritsa ntchito ndime 1 mpaka 3. Konzani zodzabweranso kuti mudzakambirane mayankho a mafunso a m’ndime 3.
◼ Mmene Mungakonzere Zodzabweranso:
Mukamamaliza phunziro loyamba, konzani zodzapitiriza zimene mwakambiranazo. Mwina mungathe kungonena kuti: “Mu mphindi zochepa chabe, taphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani yofunikira imeneyi. Nthawi ina, tingathe kudzakambirana za [funsani funso loti mudzakambirane]. Kodi mungakonde kuti mlungu wamawa ndidzabwere nthawi yomwe ino?”
Mmene tikuyandikira nthawi imene Yehova anaika, iye akupitiriza kutiphunzitsa kuti tikwanitse kuchita ntchito imene watipatsa. (Mat. 28:19, 20; 2 Tim. 3:17) Tiyeni tigwiritse ntchito bwino buku latsopanoli poyambitsa maphunziro a Baibulo.
[Bokosi patsamba 3]
Kukambirana Malemba Amene Ali pa Tsamba 4 ndi 5
◻ Chivumbulutso 21:4 (tsamba 27 mpaka 28, ndime 1 mpaka 3)
◻ Yesaya 33:24; 35:5, 6 (tsamba 36, ndime 22)
◻ Yohane 5:28, 29 (tsamba 72 mpaka 73 ndime 17 mpaka 19)
◻ Salmo 72:16 (tsamba 34, ndime 19)
Mayankho a Mafunso a pa Tsamba 6
◻ N’chifukwa chiyani timavutika? (tsamba 108 ndi 109, ndime 6 mpaka 8)
◻ Kodi tingalimbane nazo bwanji nkhawa zimene timakhala nazo pamoyo wathu? (tsamba 184 ndi 185, ndime 1 mpaka 3)
◻ Kodi tingatani kuti banja lathu likhale ndi moyo wosangalala? (tsamba 143, ndime 20)
◻ Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira? (tsamba 58 ndi 59, ndime 5 ndi 6)
◻ Kodi tidzawaonanso okondedwa athu amene anamwalira? (tsamba 72 ndi 73, ndime 17 mpaka 19)
◻ Kodi tingatsimikize bwanji kuti Mulungu adzakwaniritsa zimene walonjeza kudzachita m’tsogolo? (tsamba 25, ndime 17)