Kodi Muyambitsa Nawo Phunziro la Baibulo M’mwezi wa October?
1. Kodi m’mwezi wa October tigawira chiyani?
1 M’mwezi wa October tigawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pobwerera kwa anthu amene anachita chidwi, tikulimbikitsidwa kugwiritsa ntchito kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Komanso tikulimbikitsidwa kuyesetsa kuyambitsa phunziro la Baibulo. Kodi tingachite bwanji zimenezi paulendo wobwereza?
2. Kodi kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi tingakagwiritse ntchito bwanji kuyambitsa phunziro la Baibulo pa ulendo wobwereza kwa munthu amene analandira magazini?
2 Mmene Tingagwiritsire Ntchito Kapepala kameneka: Tikhoza kunena kuti: “Magazini amene ndinakusiyirani aja amalimbikitsa anthu amitundu yonse ndiponso zipembedzo zonse kuti aziwerenga Baibulo. [Mukatero m’patseni mwininyumbayo kapepala ka Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? ndi kumulozera mafunso amene ali patsamba loyamba.] Nawa mafunso ochititsa chidwi amene Baibulo limayankha mokhutiritsa. Kodi munayamba mwafunsapo lililonse la mafunso amenewa?” Mwininyumbayo akayankha, kambiranani naye funso limodzi mwa mafunso amene ali pa kapepalako, ndiponso kuwerenga lemba limodzi losagwidwa mawu. Kenako muuzeni kuti zimene mwachitazo ndi chitsanzo chabe cha zimene Baibulo limaphunzitsa. Mukatero m’patseni buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni. Ndiyeno mungakambirane naye ndime zoyambirira za m’mutu umene wasankha kuchokera pa tsamba 2 pamene pali za m’katimu. Kapena mungakambirane naye mutu umene uli ndi mfundo zowonjezereka zokhudza nkhani imene mwakambirana naye mu kapepalako. Mungagwiritse ntchito masamba ndi ndime zotsatirazi:
● Kodi Mulungu amatiganiziradi? (tsa. 9 mpaka 11, ndime 6 mpaka 10)
● Kodi nkhondo ndi kuvutika zidzathadi? (tsa. 12, ndime 12 ndi 13)
● Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira? (tsa. 59 ndi 60, ndime 7 ndi 8)
● Kodi akufa adzauka? (tsa. 71, ndime 13 mpaka 15)
● Kodi ndingatani kuti Mulungu aziyankha mapemphero anga? (tsa. 166 ndi 167, ndime 5 mpaka 8)
● Kodi ndingatani kuti ndikhale ndi moyo wosangalala? (tsa. 9, ndime 4 ndi 5)
3. Kodi tingasinthe bwanji ulaliki wathu mogwirizana ndi mmene anthu tawapezera?
3 Ngati paulendo wobwereza woyamba mwaona kuti zinthu panthawiyo sizikutilola kuti mumusonyeze mmene timaphunzirira kuchokera m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, mungakambirane naye kuti mudzabwerenso kudzapitiriza kukambirana. Malinga ndi chidwi chimene munthuyo anasonyeza, mungakambirane naye mafunso angapo a m’kapepala kamene munamugawira kaja. Mungachite zimenezi pamaulendo obwereza angapo musanayambe kukambirana naye zimene zili m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Tiyeni tiyesetse kugwiritsa ntchito kapepala kothandiza kwambiri kameneka m’mwezi wa October kuyambitsira maphunziro a Baibulo ndiponso kuthandiza anthu a mtima wabwino kuti ‘adziwe choonadi.’—Yoh. 8:31, 32.