Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/06 tsamba 1
  • Konzani Mipata Yolalikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Konzani Mipata Yolalikira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Lemekezani Yehova Tsiku Lililonse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Tamandani Yehova Tsiku ndi Tsiku
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Lemekezani Yehova mwa Kulalikira Mwamwayi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Tamandani Yehova Nthaŵi Zonse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 2/06 tsamba 1

Konzani Mipata Yolalikira

1 Mpingo wachikristu wapangidwa ndi anthu amene ali ndi moyo wosiyanasiyana. Komabe, tonse tili ndi mtima umodzi wolemekeza Yehova. (Sal. 79:13) Ngati kufooka kwa thanzi lathu kapena mavuto ena amene tikukumana nawo akutilepheretsa kulalikira uthenga wabwino, kodi tingakonze motani mipata yolalikira?

2 M’zochita za Tsiku ndi Tsiku: Yesu ankagwiritsa ntchito mpata umene anali nawo pochita zinthu za tsiku ndi tsiku ndi anthu ena kuti azilalikira. Analankhula ndi Mateyu pamene amadutsa pa ofesi ya amisonkho, analankhula ndi Zakeyu pamene anali pa ulendo, ndipo analankhula ndi mkazi wachisamariya pamene anali kupuma. (Mat. 9:9; Luka 19:1-5; Yoh. 4:6-10) M’zochita zathu za tsiku ndi tsiku, nafenso tingathe kusintha macheza wamba kukhala ulaliki. Kuyenda ndi Baibulo ndiponso mathirakiti kapena mabulosha, kungatithandize kukhala okonzeka kulankhula za chiyembekezo chathu.—1 Pet. 3:15.

3 Kodi tikulephera kupita nawo ku ulaliki wa khomo ndi khomo chifukwa chakuti tikulephera kuyenda? Ngati ndi choncho, khalani tcheru kugwiritsa ntchito mpata uliwonse umene mungapeze pamene ogwira ntchito kuchipatala abwera kudzakuonani kapena pamene mwakumana ndi munthu wina aliyense. (Mac. 28:30, 31) Mwina chifukwa cha zovuta zina simuchoka panyumba, kodi mwayesapo ulaliki wa patelefoni kapena wa makalata? Mlongo wina amakonda kulembera makalata abale ake omwe si Mboni. Amawalembera za zimene wakumana nazo mu ulaliki ndi nkhani zinanso zolimbikitsa za m’Baibulo.

4 Kuntchito Kapena Kusukulu: Mtima wathu wofuna kutamanda Yehova udzatichititsanso kukonza mipata yobzala mbewu za choonadi kuntchito kapena kusukulu. Wofalitsa wina wa zaka eyiti anafotokoza m’kalasi yawo zimene anawerenga mu Galamukani! pa nkhani yokhudza mwezi. Atadziwa za kumene anapeza nkhaniyo, aphunzitsi ake anayamba kulandira Nsanja za Olonda ndi Galamukani! nthawi zonse. Kungoika buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pamalo oonekera kuntchito kwathu kungayambitse mafunso amene angapereke mpata wolalikira.

5 Kodi mungaganizire za zimene mungachite kuti mukonze mipata yolalikira mukamachita ntchito zanu za tsiku ndi tsiku? Mwa kugwiritsa ntchito bwino mipita imene timakhala nayo pa moyo wathu, tiyeni tiyesetse kuti tsiku lililonse ‘tizipereka chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu.’—Aheb. 13:15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena