Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/07 tsamba 1
  • Tidzagawira Magazini Yapadera ya Galamukani! mu November

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tidzagawira Magazini Yapadera ya Galamukani! mu November
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Tingayambitsire Maphunziro a Baibulo ndi Anthu Omwe Timawagawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kugawira Buku Lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Magazini Yapadera ya Galamukani! Yodzagawira mu September
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tizisonyeza Anthu Mmene Timaphunzirira Baibulo Pogwiritsa Ntchito Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 10/07 tsamba 1

Tidzagawira Magazini Yapadera ya Galamukani! mu November

1 Anthu ambiri amafunadi kudziwa phindu lenileni la Baibulo. Ena amadzifunsa kuti: Ngati Baibulo analemba ndi anthu, ndiye lingakhale bwanji Mawu a Mulungu? N’chifukwa chiyani ndiyenera kulikhulupirira kuti linganditsogolere? Ndikamawerenga ndi kuphunzira Baibulo, kodi sikungowononga nthawi ndi kudzivutitsa chabe? Kodi ndi Baibulo liti limene ndiyenera kuwerenga? Amenewa ndi ena mwa mafunso amene ayankhidwa mu Galamukani! yapadera ya November yakuti “Kodi Muyenera Kukhulupirira Baibulo?”

2 Tikufuna kuti Galamukani! yapadera imeneyi tidzagawire anthu ambiri m’gawo lathu. Ngati mungathe, Loweruka lililonse mu November dzaloweni mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba ndi mpingo wanu. Gawirani magaziniyi kwa achibale anu, anthu amene mwayandikana nawo nyumba, amene mumagwira nawo ntchito, aphunzitsi anu, anzanu akusukulu, ndiponso amene mumakambirana nawo Mawu a Mulungu. Popita kokagula zinthu ndi paulendo, tengani magaziniyi. Akulu anaitanitsa magazini ambiri moti mpingo udzakhala nawo okwanira.

3 Yambitsani Phunziro la Baibulo: Musanamalize kukambirana ndi anthu amene mwawagawira magaziniyi, konzeranitu zodzayambitsa phunziro la Baibulo. Mwachitsanzo, munganene kuti, “Ndikadzabweranso, ndingakonde kudzakusonyezani zimene Baibulo limanena pa funso lakuti, ‘Kodi Mulungu ali nalo cholinga chotani dziko lapansili?’” Ndiyeno popitanso kwa munthuyo tengani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo m’sonyezeni tsamba 4 ndi 5, kapena kambiranani mutu 3, ndime zitatu zoyambirira. Mutha kunenanso kuti, “Ndikadzabweranso, tidzakambirana ulosi wa m’Baibulo womwe ukukwaniritsidwa panopo.” Ndiyeno mukabwererako, sonyezani mwininyumba mutu 9 wa bukuli ndipo kambiranani ndime zitatu zoyambirira. Kapena mutha kungouza mwininyumbayo kuti: “Anthu ambiri amavutika kumvetsa zimene amawerenga m’Baibulo. Ndikadzabweranso, tidzaona zomwe tingachite kuti tizilimvetsa bwino.” Paulendo wobwereza, m’patseni buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kenako m’sonyezeni mmene timachitira phunziro.

4 Baibulo ndi buku lokhalo limene lili ndi “malemba opatulika,” amene angathe kutipatsa ‘nzeru za mmene tingapezere chipulumutso.’ (2 Tim. 3:15) Choncho, tonse tichite khama kugawira magazini yapadera imeneyi ya Galamukani! kuti tithandize anthu kukhulupirira Baibulo!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena