Bokosi la Mafunso
◼ Kodi n’koyenera kulemba Imelo adiresi yathu pamabuku amene timagawira m’munda?
Ofalitsa ena alemba Imelo adiresi yawo pa magazini kapena timapepala timene amagawira ena. Amalemba maadiresiwo mwa kudinda chidindo kapena kumata kapepala kokhala ndi adiresiyo. Ndiyeno anthu amene amalandira mabukuwo amatha kulembera wofalitsayo kuti awauze zowonjezereka. Ofalitsa amene amachita zimenezi amakhala ndi zolinga zabwino zofuna kuthandiza anthu achidwi. Komabe, adiresi yathu yovomerezeka ya Intaneti imalembedwa kale pa chikuto chomaliza cha magazini ndiponso pa timapepala tathu. Motero ndi bwino kuti tisamalembe ma Imelo adiresi athuathu pa mabuku amenewa.
Zili kwa wofalitsa aliyense payekha ngati akufuna kupereka adiresi yake pa kapepala kosamatidwa pa mabuku athu kwa anthu amene wacheza nawo m’gawo. Ndipotu zingakhale bwino kuchita zimenezi paulendo wobwereza. Ifeyo ndi amene timafunika kuyamba kubwereranso kwa anthu achidwi, osati kudikirira iwowo kuti atipemphe kaye kuti tiwauze zowonjezereka. Tikamalankhula ndi munthu m’pamene timatha kumusonyeza chidwi chenicheni.