Pitaniko Mwamsanga
Tipite mwamsanga kwa ndani? Kwa anthu amene amapempha mabuku kapena amene amatiuza kuti tiziwapititsira magazini nthaŵi zonse kapenanso amene akufuna kuti wa Mboni akawachezere kunyumba kwawo. Kodi amapempha zimenezi ndani? Anthu amene amalembera kalata ku ofesi ya nthambi kapena kuimbirako telefoni. Anthu akasonyeza chidwi chonchi, ofesi ya nthambi imadziŵitsa woyang’anira dera pomulembera kakalata kamene amakapatsa akulu a mpingo wapafupi kwambiri ndi kumene munthu wachidwiyo akukhala. Akulu akalandira kapepalaka, aziuza nthaŵi yomweyo wofalitsa amene akathandize munthu wachidwiyo dzina ndi kumene iye akukhala. Ngati wofalitsa akulephera kumupeza munthuyo panyumba, wofalitsayo angayese kupitakonso nthaŵi ina. Ngati mwapemphedwa kuyendera anthu achidwiŵa, yesetsani kuwapitira mwamsanga.